Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w14 12/15 tsamba 4-5
  • Yehova Amadalitsa Anthu Opereka ndi Mtima Wonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Amadalitsa Anthu Opereka ndi Mtima Wonse
  • Nsanja ya Olonda—2014
  • Nkhani Yofanana
  • “Ntchitoyi Ndi Yaikulu”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Tiziyamikira Zimene Yehova Amatipatsa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Zochuluka Zimene Anali Nazo Zinathandiza Anthu Osowa
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Kodi Tingathandize Bwanji Anthu Ena?
    Nsanja ya Olonda—2013
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2014
w14 12/15 tsamba 4-5
Munthu akupereka ndalama

Yehova Amadalitsa Anthu Opereka ndi Mtima Wonse

YEHOVA watilemekeza kwambiri potipatsa ufulu wosankha. Iye amadalitsa kwambiri anthu amene amagwiritsa ntchito bwino ufuluwu. Iwo amagwiritsa ntchito zinthu zawo pomutumikira, pothandiza kuti dzina lake liyeretsedwe komanso pochita zinthu mogwirizana ndi cholinga chake. Yehova safuna kuti tizingomumvera chifukwa cha mantha kapena kunyengereredwa. Iye amafuna kuti tizidzipereka chifukwa chomukonda komanso kuyamikira zimene watichitira.

Mwachitsanzo, Aisiraeli ali m’chipululu cha Sinai, Yehova anawauza kuti amange chihema kuti azimulambiramo. Anati: “Nonse mupereke zopereka kwa Yehova. Aliyense amene ali ndi mtima wofunitsitsa apereke kwa Yehova.” (Eks. 35:5) Mwisiraeli aliyense anayenera kupereka zimene akanakwanitsa. Kaya zoperekazo zinali zochepa kapena zambiri, zikanathandiza pa ntchitoyi. Kodi Aisiraeliwo anatani?

“Aliyense amene anali ndi mtima wofunitsitsa” anapereka zinthu zake. Anthu anabweretsa zinthu monga ndolo, mphete, golide, siliva, mkuwa, ulusi, nsalu, ubweya wa mbuzi, zikopa za nkhosa, zikopa za akatumbu, matabwa a mthethe, miyala yamtengo wapatali ndiponso mafuta. Zinthu zimene anaperekazo “zinali zokwanira pa ntchito yonse yoyenera kuchitika, ndipo zinaposanso zinthu zofunikira pa ntchitoyo.”—Eks. 35:21-24, 27-29; 36:7.

Chimene chinasangalatsa kwambiri Yehova si kuchuluka kwa zinthuzo koma mtima wofunitsitsa umene operekawo anali nawo. Iwo anagwiritsanso ntchito nthawi yawo ndi mphamvu zawo pa ntchitoyi. Baibulo limati: “Akazi onse aluso anawomba nsalu ndi manja awo.” Limanenanso kuti: “Akazi onse aluso amene anali ndi mtima wofunitsitsa anawomba nsalu za ubweya wa mbuzi.” Yehova anathandizanso Bezaleli kuti “akhale wanzeru, wozindikira, wodziwa zinthu, ndi kuti akhale mmisiri waluso pa ntchito ina iliyonse.” Tingati Yehova anapatsa Bezaleli ndi Oholiabu luso limene linkafunika kuti ntchito yonseyo itheke.—Eks. 35:25, 26, 30-35.

Pamene Yehova ankapempha Aisiraeli kuti apereke zinthu zawo, ankadziwa kuti aliyense amene ali ndi “mtima wofunitsitsa” adzathandiza pa ntchito yokhudza kulambirayo. Iwo atapereka, Yehova anawadalitsa kwambiri powatsogolera komanso kuwathandiza kukhala osangalala. Nkhaniyi ikusonyeza kuti Yehova amadalitsa atumiki ake ngati apereka zinthu ndi mtima wonse. Izi zimachititsa kuti pasasowe zinthu kapena anthu aluso othandiza kuti cholinga chake chikwaniritsidwe. (Sal. 34:9) Yehova adzakudalitsaninso mukamadzipereka ndi mtima wonse pomutumikira.

ZIMENE ENA AMAPEREKA PA NTCHITO YAPADZIKO LONSE

Mofanana ndi nthawi ya Paulo, Akhristu ambiri masiku ano amapanga bajeti kapena kuika kandalama “kenakake pambali” kuti akaponye m’mabokosi a zopereka za “Ntchito Yapadziko Lonse.” (1 Akor. 16:2) Mwezi uliwonse mipingo imatumiza zopereka zimenezi ku ofesi ya Mboni za Yehova m’dziko lawo. N’zothekanso kutumiza nokha zopereka zanu ku maofesi ngati amenewa. Mungafunse ku ofesi ya nthambi m’dziko lanu kuti mudziwe mmene mungachitire zimenezi. Adiresi ya ofesi ya nthambi iliyonse imapezeka pa webusaiti ya www.jw.org. Mungapereke zopereka zanu m’njira izi:

ZOPEREKA MWACHINDUNJI

  • Mukhoza kupempha banki yanu kuti ichotse ndalama mu akaunti yanu n’kutumiza ku akaunti imene ofesi ya nthambi imagwiritsa ntchito. M’mayiko ena mukhoza kuchita zimenezi pogwiritsa ntchito jw.org kapena webusaiti ina.

  • Mukhoza kupereka ndalama, zinthu ngati ndolo, mphete, zibangiri ndiponso zinthu zina zamtengo wapatali. Muyenera kutumiza limodzi ndi kalata yonena kuti zinthuzo ndi zopereka.

ZONGOBWEREKA

  • Mungapereke ndalama n’kufotokoza kuti ngati nthawi ina mungazifune mudzaitanitsa.

  • Muyenera kutumiza limodzi ndi kalata yonena kuti ndalamazo ndi zongobwereka.

MPHATSO ZINA

Kuwonjezera pa kupereka mphatso za ndalama kapena zinthu zina zamtengo wapatali, pali njira zinanso zoperekera zinthu zothandiza pa ntchito ya Ufumu padziko lonse. Njira zimenezi zili m’munsimu. Musanasankhe njira iliyonse, muyenera kufunsa ku ofesi ya nthambi kuti mudziwe njira zimene ndi zotheka m’dziko lanu. Popeza malamulo amasiyana malinga ndi dziko, muyenera kufunsanso anthu odziwa bwino za malamulo ndiponso misonkho.

Inshulansi: Mungakonze zoti gulu la Yehova lidzalandire ndalama za inshulansi kapena za penshoni.

Maakaunti Akubanki: Mukhoza kupereka zinthu monga maakaunti anu akubanki, zikalata zosungitsira ndalama, kapena maakaunti a ndalama zimene mukusunga kuti mudzagwiritse ntchito mukadzapuma pa ntchito. Mukhozanso kukonza zoti mukadzamwalira, gululi lidzatenge zinthuzi. Pochita zimenezi, mutsatire malamulo amene mabanki a m’dziko lanu amayendera.

Masheya: Mungapereke ku gulu la Yehova masheya amene muli nawo m’kampani kapena kukonza zoti lidzalandire masheyawo mukadzamwalira.

Malo ndi Nyumba: Mungapereke ku gulu la Yehova malo ndi nyumba zoti zingagulitsidwe. Ngati ili nyumba yoti mukukhalamo, mukhoza kuipereka komabe n’kupitiriza kukhalamo pa nthawi yonse imene muli ndi moyo.

Chuma Chamasiye: Mukhoza kulemba mu wilo yovomerezeka ndi boma kuti gulu la Yehova lidzapatsidwe katundu wanu kapena ndalama zanu, ngati inuyo mutamwalira.

Kodi mukufuna kudziwa zambiri za mmene mungaperekere mphatsozi? Mungaimbe foni kapena kulemba kalata ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lanu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena