Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w16 November tsamba 19-20
  • “Ntchitoyi Ndi Yaikulu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Ntchitoyi Ndi Yaikulu”
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Nkhani Yofanana
  • Tiziyamikira Zimene Yehova Amatipatsa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Yehova Amadalitsa Anthu Opereka ndi Mtima Wonse
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Zochuluka Zimene Anali Nazo Zinathandiza Anthu Osowa
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Kodi Tingathandize Bwanji Anthu Ena?
    Nsanja ya Olonda—2013
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
w16 November tsamba 19-20
Mfumu Davide ikumuonetsa munthu mapulani a kachisi. M’bale akuyang’ana pepala lomwe palembedwa pulani ya nyumba

“Ntchitoyi Ndi Yaikulu”

PA NTHAWI ina Mfumu Davide anaitana akalonga ake, nduna za panyumba ya mfumu komanso amuna amphamvu kumsonkhano wofunika kwambiri ku Yerusalemu. Oitanidwawo anasangalala atamva chilengezo chapadera. Yehova anasankha Solomo, mwana wa Davide, kuti amange nyumba yaikulu yoti anthu azilambiriramo Mulungu woona. Mulungu anauza Davide mapulani onse a nyumbayo ndipo Davideyo anafotokozera Solomo. Davide anati: “Ntchitoyi ndi yaikulu chifukwa chinyumba chachikuluchi, si cha munthu ayi, koma ndi cha Yehova Mulungu.”—1 Mbiri 28:1, 2, 6, 11, 12; 29:1.

Kenako Davide anafunsa kuti: “Ndani lero ali wokonzeka kupereka mphatso kwa Yehova?” (1 Mbiri 29:5) Kodi inuyo mukanakhalapo mukanathandiza pa ntchitoyi? Aisiraeli anayesetsa mmene akanathera kuti athandize pa ntchitoyo. Iwo “anasangalala chifukwa cha nsembe zaufulu zimene anapereka, pakuti anapereka nsembezo kwa Yehova ndi mtima wathunthu.”—1 Mbiri 29:9.

Patapita zaka zambirimbiri, Yehova anakhazikitsa kachisi wamkulu kuposa amene Solomo anamanga. Kachisiyu amatchedwa kachisi wamkulu wauzimu ndipo ndi njira yothandiza anthu kuti azimulambira kudzera mu nsembe ya Yesu. (Aheb. 9:11, 12) Kodi Yehova amathandiza bwanji anthu kuti agwirizanenso naye? Iye amachita zimenezi kudzera mu ntchito yolalikira. (Mat. 28:19, 20) Ntchitoyi ikuthandiza kuti chaka chilichonse anthu mamiliyoni ambiri aziphunzitsidwa Baibulo, anthu masauzande ambiri azibatizidwa komanso mipingo mahandiredi ambiri izikhazikitsidwa.

Zonsezi zikuchititsa kuti mabuku ambiri azisindikizidwa komanso pazimangidwa Nyumba za Ufumu ndiponso Malo a Misonkhano ambiri. Kunena zoona ntchito yolalikira ndi yaikulu ndipo ikuthandiza anthu.—Mat. 24:14.

Chifukwa chokonda Yehova komanso anzawo, anthu a Mulungu masiku ano amayesetsanso kupereka zinthu zawo kuti zikhale “mphatso kwa Yehova.” Iwo amadziwanso kuti ntchito yolalikira ikufunika kugwiridwa mwachangu. Zimasangalatsa kwambiri ‘tikamalemekeza Yehova ndi zinthu zathu zamtengo wapatali’ komanso tikamaona zinthuzo zikugwiritsidwa ntchito bwino kuti zithandize pa ntchito yofunika kwambiriyi.—Miy. 3:9.

Zimene Ena Amapereka Pothandiza Pa Ntchito Yapadziko Lonse

Akhristu ambiri masiku ano amapanga bajeti kapena kuika kandalama “kenakake pambali” kuti akaponye m’mabokosi a zopereka za “Ntchito Yapadziko Lonse.” (1 Akor. 16:2) Mwezi uliwonse mipingo imatumiza zopereka zimenezi ku ofesi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lawo. N’zothekanso kutumiza nokha zopereka zanu kumaofesi ngati amenewa. Mungafunse ku ofesi ya nthambi ya m’dziko lanu kuti mudziwe mmene mungachitire zimenezi. Adiresi ya ofesi ya nthambi iliyonse imapezeka pa webusaiti ya www.jw.org. Mungapereke zopereka zanu m’njira izi:

ZOPEREKA MWACHINDUNJI

  • Mukhoza kupempha banki yanu kuti ichotse ndalama mu akaunti yanu n’kutumiza ku akaunti ya ofesi ya nthambi. M’mayiko ena mukhoza kuchita zimenezi pogwiritsa ntchito jw.org kapena webusaiti ina.

  • Mukhoza kupereka ndalama kapena zinthu zina zamtengo wapatali monga ndolo, mphete ndiponso zibangiri. Muyenera kutumiza limodzi ndi kalata yonena kuti zinthuzo ndi zopereka.

ZONGOBWEREKA

  • Mungapereke ndalama n’kufotokoza kuti ngati nthawi ina mungadzazifune, mudzaziitanitsa.

  • Muyenera kutumiza limodzi ndi kalata yonena kuti ndalamazo mwangowabwereka.

MPHATSO ZINA

Kuwonjezera pa kupereka mwachindunji, pali njira zinanso zoperekera zinthu zothandiza pa ntchito ya Ufumu padziko lonse. Njira zimenezi zili m’munsimu. Musanasankhe njira iliyonse, muyenera kufunsa ku ofesi ya nthambi kuti mudziwe njira zimene ndi zotheka m’dziko lanu. Popeza malamulo amasiyana malinga ndi dziko, muyenera kufunsanso anthu odziwa bwino za malamulo ndiponso misonkho.

Inshulansi: Mungakonze zoti gulu la Yehova lidzalandire ndalama za inshulansi kapena za penshoni.

Maakaunti a Kubanki: Mukhoza kupereka zinthu monga maakaunti anu a kubanki, zikalata zosungitsira ndalama, kapena maakaunti a ndalama zimene mukusunga kuti mudzagwiritse ntchito mukadzapuma pa ntchito. Mukhozanso kukonza zoti mukadzamwalira, gulu la Yehova lidzatenge zinthuzi. Pochita zimenezi, mutsatire malamulo amene mabanki a m’dziko lanu amayendera.

Masheya: Mungapereke ku gulu la Yehova masheya amene muli nawo m’kampani kapena kukonza zoti lidzalandire masheyawo mukadzamwalira.

Malo Kapena Nyumba: Mungapereke ku gulu la Yehova malo kapena nyumba zoti zingagulitsidwe. Ngati ili nyumba yoti mukukhalamo, mukhoza kuipereka komabe n’kupitiriza kukhalamo pa nthawi yonse imene muli ndi moyo.

Chuma Chamasiye: Mukhoza kulemba mu wilo yovomerezeka ndi boma kuti gulu la Yehova lidzapatsidwe katundu wanu kapena ndalama zanu, ngati inuyo mutamwalira.

Ngati mukufuna kudziwa zambiri tsatirani linki yakuti, “Perekani Ndalama Zothandizira Ntchito ya Padziko Lonse” patsamba loyamba la webusaiti ya jw.org apo ayi imbani foni kapena kulemba kalata ku ofesi ya nthambi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena