Programu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera
1 Programu yathu ya tsiku la msonkhano wapadera yoyamba mu September idzakhala ndi mutu wakuti “Pitirizani Kuchitira Umboni Choonadi.” Programu yonse idzasumika maganizo pa chitsanzo chimene Yesu anatisiyira ndi mmene anagwiritsirira ntchito mwaŵi uliwonse kugaŵana choonadi ndi ena. Idzagogomezera thayo lathu monga ophunzira a Kristu la kumtsanzira iye m’kuchitira umboni choonadi.—1 Akor. 11:1.
2 Mbali imene mpingo umachita m’kuchirikiza choonadi idzalingaliridwa. Kugwiritsira bwino ntchito magazini athu ndi zofalitsidwa zina kudzagogomezeredwanso.
3 Nkhani yaikulu yokambidwa ndi wokamba nkhani wochezera ili ndi mutu wakuti “Kuchitira Umboni Choonadi—Zimene Kumakwaniritsa.” (Yoh. 8:32) Programu ya tsiku la msonkhano wapadera imeneyi idzazamitsadi chiyamikiro chathu cha choonadi ndi kuthandiza tonsefe kukhalabe ochirimika ndi kukhala ‘okhazikika m’choonadi.’—2 Pet. 1:12; 1 Akor. 15:58.