Pulogalamu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera
Mothandizidwa ndi mzimu woyera, Akristu oyambirira anadzipereka kwambiri polalikira uthenga wabwino kumadera akutali kwambiri. (Mac. 1:8; Akol. 1:23) Pulogalamu ya tsiku la msonkhano wapadera wa chaka chautumiki cha 2007 wa mutu wakuti, “Limbikirani Kulalikira Mawu,” idzatithandiza kutengera chitsanzo chawo chabwino kwambiri.—Mac. 18:5.
Ponena za Mawu a Mulungu, Mfumu Davide inati: “Mboni [“zikumbutso,” NW] za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru.” (Sal. 19:7) Pulogalamu yokonzedwa bwino ya tsiku la msonkhano wapadera wa chaka cha 2007 idzafotokoza mmene Malemba amatithandizira “kuwongola zinthu” ndipo idzatilimbikitsa kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu polalikira ndi kuphunzitsa mwachangu. (2 Tim. 3:16, 17, NW) Pulogalamu ya msonkhanowu idzatisonyeza mmene tingapewere kugwa m’misampha yosiyanasiyana ndi mmene tingapindulire pogwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo pamoyo wathu. Idzatithandizanso kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu pothandiza achinyamata ndi atsopano kupita patsogolo mwauzimu.
Chitani zotheka kuti mudzakhalepo msonkhanowu ukamadzayamba, ndipo mudzamvetsere mwatcheru. Muzidzalemba mfundo zomwe mukufuna kudzagwiritsa ntchito pamoyo wanu. Mudzasonyeze kuti mukuyamikira malangizo ndi zikumbutso zomwe zidzaperekedwe, ndipo dzaganizireni momwe mungadzagwiritsire ntchito zinthu zimene mwaphunzira.
Pulogalamu ya tsiku la msonkhano wapadera idzatithandiza kupitiriza kuyamikira Mawu a Mulungu, idzatikumbutsa kuti tipitirize kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu mwachangu, ndipo idzatisonyeza momwe tingathandizire anthu ena kuti achitenso chimodzimodzi. Choncho onetsetsani kuti musadzaphonye malangizo auzimu alionse amene Yehova amapereka mwanjira imeneyi.—Yes. 30:20b, 21.