Onse Anakondwera ndi Kutulutsidwa kwa Buku Latsopano pa Msonkhano Wachigawo
Buku Latsopanolo Likusonyeza Chidziŵitso cha Mulungu
1 Pa msonkhano wachigawo chilimwe chathachi, tinasangalala chotani nanga ndi programu yonse! Pa masana a tsiku lachiŵiri chimwemwe chathu chinasefukira pamene tinamva chilengezo chonena za buku latsopano, Knowledge That Leads to Everlasting Life, ndi chidziŵitso chake chimene chinatsatira. Anthu miyandamiyanda a dziko lapansi afunikira chidziŵitso chimene ndi Mulungu yekha angapereke—kudziŵa Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu.—Miy. 2:1-6; Yoh. 17:3.
2 Wolankhula nkhaniyo anafotokoza bwino chotani nanga mbali za bukulo! Mitu ya nkhani yodzutsa chidwiyo, zithunzithunzi zake zothandizazo, kufotokoza kwake choonadi komveka, mafunso ofeŵa, ndiponso, pamapeto a mutu uliwonse, bokosi lakuti “Test Your Knowledge” zili pakati pa zinthu zimene zidzakopa onse amene adzaliŵerenga. Koma ophunzira Baibulo athu adzapindula kwambiri pamene aphunzira mofulumira ziphunzitso zazikulu za Baibulo.
3 M’nkhani zotsiriza patsiku lachiŵiri ndi lachitatu, tinalimbikitsidwa kukhala ndi phunziro la banja mogwiritsira ntchito buku latsopanoli. Pofika tsopano, mwachionekere tadziŵa zamkati mwake. Mosakayikira inu mwakambitsiranaponso mfundo zina zofunika kudziŵa pogaŵira buku latsopanoli m’munda.
4 Mfundo Zoti Mupende: Mungakumbukire kuti pokamba nkhani yakuti “Chifukwa Chake Anthu Afunikira Chidziŵitso Chonena za Mulungu,” wokamba nkhaniyo anagogomezera mfundo zingapo, kuphatikizapo zotsatirapozi: (1) Pamene mukugwiritsira ntchito bukuli kuchititsa maphunziro, sikuli kwanzeru kuloŵetsamo nkhani zinanso, zimene zingaphimbe mfundo zazikulu; ingosumikani maganizo pa kufotokoza zimene bukulo likusonyeza m’mutu uliwonse. (2) Mitu yake njaitali bwino kotero kuti inu kaŵirikaŵiri mudzakhoza kumaliza umodzi panthaŵi iliyonse pamene muphunzira. (3) Pamapeto pa mutu uliwonse, mafunso okhala m’bokosi lakuti “Test Your Knowledge” adzapereka kupenda kwachidule.
5 Kugwiritsira Ntchito pa Maphunziro a Baibulo: Ofalitsa angapo afuna kuti adziŵe ngati angathe kusinthira maphunziro awo a Baibulo m’buku limeneli latsopano. Ngati mwafola kale mitu yambiri m’buku limene mukuphunzira nawo pakali pano, ndi bwino kuti mumalize kuphunzira bukulo. Komano ngati sizili choncho, ndi bwino kuti musinthire ku buku la Knowledge. Ngati munagwiritsira ntchito brosha kapena trakiti kuyambitsira phunziro la Baibulo, sonyezani buku latsopanolo panthaŵi yoyenera ndi kuligwiritsira ntchito m’phunziro. Chidziŵitso china chonena za kugwiritsiridwa ntchito kwa buku la Knowledge chidzatulutsidwa mu Utumiki Wathu Waufumu m’miyezi ikudzayo.
6 Yehova watipatsa buku latsopano limeneli kuti litithandize kuphunzitsa ena za chidziŵitso chimene chimatsogolera ku moyo wosatha. Tsopano tifunikira kukonzekera bwino ndi kukhala ndi mbali mokwanira mu ntchito yofuna kuchitidwa.