Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/99 tsamba 3-4
  • Kodi Tsopano Khomo Lochita Upainiya Lakutsegukirani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Tsopano Khomo Lochita Upainiya Lakutsegukirani?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Utumiki Waupainiya—Kodi Ngoyenera Inu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Apainiya Othandiza 3,000 Akufunika
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Madalitso a Utumiki Waupainiya
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Ndandanda ya Upainiya Wokhazikika
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 8/99 tsamba 3-4

Kodi Tsopano Khomo Lochita Upainiya Lakutsegukirani?

1 Lemba lathu la chaka cha 1999 limatikumbutsa kuti tidakali mu “tsiku la chipulumutso” la Yehova. (2 Akor. 6:2) Koma posachedwapa tsiku lake la chipulumutso litha. Ndiyeno “tsiku [lake] loweruza” lidzayamba. (2 Pet. 2:9) Pamene Yehova akupitiriza kupereka mwayi wa chipulumutso kwa anthu, n’zosangalatsa zedi kuona anthu owonjezerekawonjezereka akulabadira!

2 Anthu a Yehova adzipereka kufikira anthu omvetsera nthaŵi isanathe. Kwa ofalitsa Ufumu ambiri, izi zatanthauza kuyamba utumiki waupainiya. Kodi tsopano khomo lochita upainiya lakutsegukirani? Chifukwa chiyani tikufunsa motere?

3 Kusonyeza Kuyamikira: Malinga ndi chilengezo mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 1999, maola ofunika kwa apainiya othandiza ndi okhazikika omwe anachepetsedwa. Kuti akwanitse maola atsopanowa, apainiya okhazikika ayenera kuthera maola 70 mu utumiki mwezi uliwonse kuti adzikwanitsa maola 840 pa chaka chautumiki. Apainiya othandiza adzithera maola 50 mu utumiki mwezi uliwonse. Awa ndi ena mwa mawu ambiri amene anenedwa osonyeza kuyamikira chifukwa cha kusintha kumeneku:

“Ilidi ndi dalitso lochokera kwa Atate wathu wakumwamba!”

“Palibe mawu amene angalongosole chimwemwe, chikondi, ndi kuyamikira kwanga makonzedwe amenewa!”

“Adzapangitsa ndandanda yathu kukhala yosavuta kwambiri kukwaniritsa!”

“Pemphero lathu n’lakuti ambiri tsopano alembetse utumiki wanthaŵi zonse ndi kusangalala ndi madalitso amene amadza mwa kutumikira Yehova mokulirapo.”

4 Pamene tikuyandikira pachimake penipeni pa tsiku la chipulumutso la Mulungu, n’kwachidziŵikire kuti Yehova akufuna kuti anthu ake apereke chitamando chomaliza mokweza kwambiri. Kukula ndi mphamvu ya uthenga umenewu zawonjezeka (1) ndi kukwera kopitiriza kwa chiŵerengero cha ofalitsa Ufumu komanso (2) ndi chidwi cha aliyense chofuna kuwonjeza zimene angathe kuchita polalikira Ufumu. Yehova, amene ‘amakulitsa,’ wachititsa njira ziŵirizi kupambana mwa kudalitsa mzimu wofunitsitsa wa onse amene alandira chipulumutso.—1 Akor. 3:6, 7; Sal. 110:3.

5 Osaiŵala Cholinga Chake: Paulo anali kunena za tsiku la chipulumutso la Yehova pamene analangiza Akristu anzake kuti: “Ndipo ochita naye pamodzi [Yehova] tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu [“ndi kuiŵala cholinga chake,” NW].” ‘Sitidzaiŵala cholinga chake’ ngati tiona nthaŵi ino kukhala “nyengo yabwino yolandiridwa” kugwira ntchito yopulumutsa ena pampata uliwonse. (2 Akor. 6:1, 2) Lerolino, mawu a Paulo ndi ofunika kwambiri. Akristu osonyeza chikondi chenicheni kwa Yehova amauona kukhala mwayi kutengamo mbali mokwanira mmene angathere mu utumiki umene iye wawapatsa. Kodi tsopano mukutengamo mbali mokwanira mu utumiki monga mpainiya wokhazikika?

6 ndi Cholinga Choyenera: M’Malaŵi muno, cholinga chathu n’chakuti tidzakhale ndi apainiya okhazikika 3,500 atalembetsa pa September 1. Tikukhulupirira kuti chimenechi ndi cholinga choyenera komanso chotheka. Chifukwa chiyani tili otsimikiza chonchi? Mu March 1997 tinali ndi abale ndi alongo 3,557 amene anali apainiya othandiza, ndipo mu April 1998 pafupifupi 2,900 anachita zofananazo. Ambiri mwa anthu amenewa anapereka maola 60—kungopereŵera maola 10 okha kuti akwanitse maola atsopano ofunika kwa mpainiya wokhazikika! Ngakhale kutakhala kuti 400 okha mwa amene anachita upainiya wothandiza alembetsa upainiya wokhazikika chaka chautumiki chisanathe, ndiye kuti podzafika September tidzakhala ndi apainiya okhazikika 3,500 kapena kuposerapo!

7 Ndandanda ndi Yofunika: Kodi inu mukuonabe kuti maola 70 pamwezi mu utumiki wakumunda ali ovuta kukwaniritsa? Mwina kuganiza za maola 17 pamlungu kungathandize. Mwa kugwiritsa ntchito chitsanzo cha ndandanda imene ili patsamba lotsatirayi, yesani kupanga ndandanda ya mpainiya wokhazikika imene idzagwirizana ndi mikhalidwe yanu. Popanga ndandanda yanuyo, lankhulani ndi mpainiya wozolowera kuti akuuzeni mmene amakwanitsira utumiki waupainiya kwinaku maudindo aumwini ndi abanja. Funsani woyang’anira dera mmene apainiya m’deralo amachitira ntchito yawo ya utumiki mlungu uliwonse. Ndiyeno yang’anani kwa Yehova kuti adalitse zolinga zanu zochita upainiya.—Miy. 16:3.

8 Upangeni Kukhala Ntchito ya Banja: Kodi mwalingalira zochita upainiya monga ntchito ya banja? Mungakhale pansi ndi banja lanu n’kukambirana—mwa kulinganiza zinthu bwino ndi kugwirizana—mmodzi kapena aŵiri m’banjamo angakhale okhoza kuchita upainiya. Komabe, ena angapeze kuti atapenda mikhalidwe yawo mosamalitsa sikotheka kuchita upainiya wokhazikika pakalipano. Ngati zili choncho, pangani kuchita upainiya kukhala cholinga cha m’tsogolo. Koma yambani kukonzekera mwa kukhala ndi tsiku lenileni lodzayamba kuchita upainiya. Mwinamwake mungachite upainiya wothandiza nthaŵi zingapo pa chaka mpaka mutadzakwanitsa cholinga cha utumiki waupainiya.

9 Apainiya okhazikika oposa 3,000 amene alipo pakalipano m’Malaŵi ali ndi mikhalidwe yosiyanasiyana. Si onse amene ali ndi thanzi labwino, ndipo ambiri ali ndi maudindo abanja ndi azandalama. Komabe, onsewa ‘akuchita machawi’ kuti achite upainiya, zimene kaŵirikaŵiri zawapangitsa kukhala ndi moyo wosalira zambiri koma wokhutiritsa kwambiri.—Akol. 4:5.

10 Kodi Moyo Wanu Ufunikira Kukhala Wosalira Zambiri? Kukhala ndi moyo wosalira zambiri kungakhale kiyi yokutsegulirani inu khomo lochitira upainiya. Kodi moyo wanu uli ngati nyumba yaikulu ya zipinda komanso katundu wa m’nyumba osafunika kwenikweni, yofuna nthaŵi, ndalama, ndi ntchito yambiri poisamalira? Ngati mukuti inde, ndiye kuti kusintha moyo wanu kuti ukhale wachikatikati kungakutheketseni kuchita upainiya. Kodi mungachepetse nthaŵi imene mumagwira ntchito yakuthupi? Kodi mungapatule nthaŵi pa imene mumathera pa zinthu zosafunika kwenikweni kapena kodi mungasonyeze chikatikati panthaŵi imene mumathera pazosangalatsa?

11 Baibulo, pa 1 Timoteo 6:8, limatilangiza kuti: “Pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.” Kukhala wokwaniritsidwa ndi zochepa ndi mfundo yofunika pochita zomwe tingathe mu utumiki wa Yehova ndipo kumatipeputsira zinthu kuti tiike zinthu zauzimu pamalo oyamba. (Mat. 6:22, 33) Patsamba 104 la 1998 Yearbook pa lipoti la Japan, pali mfundo zingapo zosonyeza chifukwa chake m’dzikolo muli mzimu waupainiya. Nayi imodzi: “Nyumba zambiri za Ajapani ndi zazing’ono, choncho zimafuna nthaŵi yochepa pozisamalira, ndipo malinga ndi chikhalidwe chawo, ambiri miyoyo yawo ndi yosalira zambiri.” Kodi zimenezo sindizo tanthauzo lenileni la 1 Timoteo 6:8?

12 Kuzungulira dziko lonse, atumiki a Mulungu akulalikira uthenga wabwino mwachangu kwambiri tsiku la chipulumutso la Yehova lisanathe. Ubwino wake ndi wakuti chaka chatha mwezi uliwonse pafupifupi anthu 700,000 anachita utumiki waupainiya. Kodi mungasinthe moyo wanu kuti muchite nawo ntchitoyo? Tikukupemphani kupenda mikhalidwe yanu mosamala ndi mwapemphero pamene mukuyankha funso lakuti: “Kodi tsopano khomo lochita upainiya lakutsegukirani?”

[Mawu Otsindika patsamba 3]

CHOLINGA: APAINIYA OKHAZIKIKA 3,500!

[Bokosi patsamba 4]

Zitsanzo za Ndandanda ya Upainiya Wokhazikika

Maola Ofunika Pamlungu: 17

Tsiku Limodzi Pamlungu ndi Wikendi

Tsiku Maola

Lachisanu 8

lowêruka 6

Lamlungu 3

Chiwonkhetso cha Maola: 17

Masiku Aŵiri Pamlungu ndi Loŵeruka

Tsiku Maola

Lachiŵiri 7

Lachinayi 7

lowêruka 3

Chiwonkhetso cha Maola: 17

Masiku Atatu Pamlungu ndi Lamlungu

Tsiku Maola

Lolemba 5

Lachiŵiri 5

Lachisanu 5

Lamlungu 2

Chiwonkhetso cha Maola: 17

Madzulo Aŵiri ndi Wikendi

Tsiku Maola

Lolemba 3

Lachitatu 3

Loŵeruka 8

Lamlungu 3

Chiwonkhetso cha Maola: 17

Pangani Ndandanda Yanuyanu ya Upainiya Wokhazikika

Tsiku Maola

Lolemba

Lachiŵiri

Lachitatu

Lachinayi

Lachisanu

Loŵeruka

Lamlungu

Chiwonkhetso cha Maola: 17

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena