Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/99 tsamba 5-6
  • Kubwereramo Kolemba M’sukulu ya Utumiki Wateokalase

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereramo Kolemba M’sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 8/99 tsamba 5-6

Kubwereramo Kolemba M’sukulu ya Utumiki Wateokalase

Kubwereramo kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase zogaŵiridwa kuyambira mlungu wa May 3 kufikira August 23, 1999. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.

[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]

Yankhani kuti Zoona kapena Kunama m’ndemanga zotsatirazi:

1. Ngati makolo akufuna kulera ana awo mwanzeru safunikira kulolera kuswa malamulo a Baibulo. [fy-CN tsa. 108 ndime 14]

2. Kuti muthandize ana aang’ono kumvetsetsa msanga kuti mnzawo amene akudwala akumva bwanji, muyenera kuwafotokozera zinthu zambiri zokhudza mankhwala. [fy-CN tsa. 123, ndime 17]

3. Malinga ndi Yohane 2:14-16, Yesu anagwiritsa ntchito mkwapulo kuingitsira anthu amene anali kuchita malonda m’kachisi. [gt-CN mutu 16; onani w95-CN 9/15, tsa. 11 ndime 12]

4. Anthu amene ali amphaŵi kwambiri sangathe kupereka nawo ndalama zothandizira pantchito ya Ufumu. [w97-CN 9/15 tsa. 5 ndime 7]

5. Kubwezera makolo ndi agogo ndiyo njira ina yolambirira Yehova. (1 Tim. 5:4) [w97-CN 9/1 tsa. 4 ndime 1-2]

6. Pachiyambi, kusunga Sabata chinali chizindikiro pakati pa Yehova ndi mitundu yonse. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani rs-CN tsa. 345 ndime 3.]

7. Pamene mwana akukula nayamba kumasankha yekha zochita, ndiye kuti zambiri zimene akuchita mlandu umakhala wake, makamaka pankhani yokhudza malamulo a Mulungu. (Aroma 14:12) [fy-CN tsa. 135 ndime 17]

8. Pamene Mose anasandutsa madzi onse a ku Igupto n’kukhala magazi, ansembe a ku Igupto nawonso anachita zimenezo ndipo mwina anagwiritsa ntchito madzi a m’chitsime kuchitira matsenga awowo. (Eks. 7:19-24) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w83 10/15 tsa. 30]

9. Mawu a Yesu a pa Luka 21:20, 21 anakwaniritsidwa mu 66 C.E. pamene magulu ankhondo a Aroma otsogozedwa ndi Kazembe Titus anatulukanso m’Yerusalemu. [w97-CN 4/1 tsa. 5 ndime 3-4]

10. Zimene Epicurus ankaphunzitsa zinali zoti zikanavulaza Akristu chifukwa zinali zogwirizana ndi kupanda kwake chikhulupiriro kotchulidwa pa 1 Akorinto 15:32. [w97-CN 11/1 tsa. 24 ndime 5]

Yankhani mafunso otsatirawa:

11. Kodi tikuphunziranji pamfundo yakuletsa kudya mafuta yomwe yatchulidwa pa Levitiko 3:17? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w84 2/15 tsa. 29 ndime 2.]

12. Kodi Yehova waloleranji kuti Satana Mdyerekezi akhalepobe? (Eks. 9:15, 16) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w92-CN 3/15 tsa. 10 ndime 14.]

13. Ngati wina m’banja wadwala kwambiri, kodi ena m’banjamo ayenera kuyamba kuchita zinthu ziti kuti adziŵe zofunika kuchita choyamba? (Miy. 15:22) [fy-CN tsa. 122 ndime 14]

14. Kodi mtundu wa Aisrayeli unali “ufumu wa ansembe” mwa njira iti? (Eks. 19:6) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 7/1 tsa. 16 ndime 8.]

15. Kodi ‘diso la kumodzi’ ndi ‘diso loipa,’ kusiyana kwake n’kotani? (Mat. 6:22, 23) [w97-CN 10/1 tsa. 26 ndime 5]

16. Kodi n’chifukwa chiyani Davide ananenedwa kuti ankayenda “ndi mtima woona ndi wolungama” ngakhale kuti ankalakwa? (1 Maf. 9:4) [w97-CN 5/1 tsa. 5 ndime 2]

17. Pamene Aisrayeli anachita “momwemo” pantchito yomanga chihema, kodi kuteroko kunachitira chithunzi mwayi wotani lerolino? (Eks. 39:32) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 12/15 tsa. 12 ndime 9.]

18. Yehova anadzivumbula yekha mwakunena kuti “Ine ndine yemwe ndili ine,” kodi zimenezi zikutanthauzanji? (Eks. 3:14) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 3/1 tsa. 10 ndime 6.]

19. Kodi nkhani ya pa Levitiko 10:1, 2, yonena zimene zinachitikira Nadabu ndi Abihu ikutiphunzitsa chiyani? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w84 2/15 tsa. 29 ndime 3.]

20. Panthaŵi ya Chilamulo cha Mose, kodi n’chifukwa chiyani mkazi akabala mwana mkaziyo anali kukhala “wodetsedwa”? (Lev. 12:2, 5) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w84 2/15 tsa. 29 ndime 5.]

Pezani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:

21. Ngakhale kuti palibe mankhwala ozizwitsa othetsera kusungulumwa, kholo lopanda mnzake lingapirirebe mwa mphamvu yochokera kwa ․․․․․․․, ndipo mphamvuyo angaipeze mwa ․․․․․․․ akhama. (1 Tim. 5:5) [fy-CN tsa. 113 ndime 21]

22. Ngati wina tsoka lam’gwera, chingakhale chifukwa cha ․․․․․․․ kapena chifukwa cha ․․․․․․․ wathu ․․․․․․․. [w97-CN 5/15 tsa. 22 ndime 7]

23. Pangano ․․․․․․․ limathandizira kupanga ‘ufumu wa ansembe, ndi mtundu wopatulika’(Eks. 19:6) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 2/1 mas. 18-19.]

24. Zimene timachita ․․․․․․․ n’zimene zimavumbula umunthu wathu wam’kati, osati zimene timachita ․․․․․․․. [w97-CN 10/15 tsa. 29 ndime 4]

25. Ngati madyerero akututa ali ndi miyambo ․․․․․․․ kapena ․․․․․․․, Akristu oona angakondweretse Yehova mwa kupeŵa ․․․․․․․ kosakondweretsa Mulungu ngati kumeneko. [w97-CN 9/15 tsa. 9 ndime 6]

Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:

26. Mawu akuti “madzulo” pa Eksodo 12:6 akutanthauza kuyambira (dzuŵa lili pamutu mpaka kuloŵa kwa dzuŵa; kulowa kwa dzuwa mpaka kugwa kwa mdima; kuyambira madzulo a tsiku limodzi pa kalenda mpaka madzulo a tsiku lotsatira). [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w73 tsa. 175]

27. Kaya banja likwanitse kusamala bwino wodwala wawo kapena lilephere kum’samala bwino, zimadalira (ndalama; mmene ena m’banjamo amamuonera; ndalama za inshuwalansi. (Miy. 17:22) [fy-CN tsa. 120 ndime 10]

28. Munthu amene mumtima mwake amati “kulibe Mulungu” ameneyo amatchedwa ‘chitsiru’ chifukwa chakuti ( n’ngwopanda khalidwe; n’ngwosaphunzira; n’ngwosaganiza bwino). (Sal. 14:1) [w97-CN 10/1 tsa. 6 ndime 8]

29. Pamene Adamu ndi Hava anapanduka, chinthu chofunika kwambiri chimene chinawatayika chinali (ungwiro wawo; unansi wawo ndi Mulungu; mudzi wawo wonga munda), umene ukanawapatsa chimwemwe. [w97-CN 10/15 tsa. 6 ndime 2]

30. Zimene Eksodo 40:34 akufotokoza zikutanthauza (umboni wakuti Yehova anavomereza chihema; chikumbutso chakuti Yehova n’ngwosaoneka; chizindikiro cha nthaŵi zamavuto zomwe zinali kudza). [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani hs-CN tsa. 71 ndime 30]

Gwirizanitsani malemba otsatirawa ndi ndemanga zondandalikidwa pansipa:

Eks. 5:2; Eks. 21:29; Miy. 1:8; Agal. 5:20; Yak. 1:14, 15

31. Aliyense wodzitcha Mkristu koma alinso wopsa mtima msanga, ndipo womenyamenya anthu a m’banja lake, komanso wosalapa, ameneyo angachotsedwe mumpingo. [fy-CN tsa. 150 ndime 23]

32. Tisanachite kanthu timayamba taganiza. [fy-CN tsa. 148 ndime 18]

33. Yehova Mulungu amanyazitsa onse amene amanyoza Umulungu wake. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w92-CN 12/15 tsa. 13 ndime 18.]

34. Ngakhale kuti Baibulo limatchula makamaka bambo kuti ndiye ali ndi udindo wophunzitsa ana, mayinso ali ndi udindo waukulu. [fy-CN tsa. 133 ndime 12]

35. Chilamulo sichinkachitira chifundo munthu wosasamala ngati wina anaphedwa chifukwa cha kusasamala kwakeko. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 11/15 tsa. 11 ndime 5.]

S-97-CN Zam, Mal & Moz #298 8/99

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena