M’lemekezeni Yehova ndi Ntchito Zabwino
1 Mkuntho ukakupezani, mtima wanu umakhala pansi mukapeza malo obisalamo! Ngati ndi motenthera ndi motetezeka komanso ngati anthu ake ali olandira bwino alendo, mungafune kukhalabe momwemo. Ntchito yolalikira Ufumu imatsogolera anthu a m’dongosolo la Satana kumalo otereŵa. Kodi khalidwe lathu la tsiku ndi tsiku lingakopere ena kumalo achisungiko ameneŵa? Inde, popeza Yesu ananena kuti anthu ‘adzaona ntchito zathu zabwino, ndi kulemekeza Atate wathu wa Kumwamba.’—Mat. 5:16.
2 Kodi tingakhale motani ndi khalidwe labwino kuti ntchito zathu zikopere ena kwa Yehova ndi gulu lake? Mwa kuumba moyo wathu tsiku lililonse ndi mawu a Yesu a pa Luka 6:31 ndi Luka 10:27. Izi zidzatisonkhezera kukonda anzathu ndi kuwadera nkhaŵa, mosiyana ndi dziko lino lopanda chikondi ndi losasamala za ena.
3 Mlongo wina m’bwato anaona mtsikana akulephera kusamalira khanda lake chifukwa ankachita chizungulire ndi nseru kwambiri. Mlongoyo anam’landira mwanayo. Mtsikanayo atafunsa kuti athokoze bwanji, mlongoyo anati: ‘Mudzamvere Mboni za Yehova zikadzakufikirani.’ Mtsikanayo anachitadi zimenezo, tikunena pano iye ndi mwamuna wake ndi Mboni. Ntchito zabwino zinathandiza kwambiri kuti alabadire uthenga wa Ufumu.
4 N’zokhudza Moyo Wathu Wonse: Khalidwe lathu kunyumba, kuntchito kapena kusukulu, ndiponso panthaŵi yosangalala limauza ena za ife ndi chipembedzo chathu. Choncho, tidzifunse kuti: ‘Kodi ena amandiona bwanji ndi banja langa? Kodi anansi athu amaona nyumba yathu kukhala yaudongo ndi yosamalidwa bwino pabwalo? Kodi anzathu a kuntchito ndi kusukulu amationa kukhala osunga nthaŵi ndi olimbikira? Kodi ena amati maonekedwe athu ndi abwino ndi aulemu?’ Ntchito zathu zabwino zingapangitse kulambira Yehova kukhala kokopa ena kwambiri.
5 Petro anachenjeza Akristu kuti anthu adzawanyoza. (1 Pet. 4:4) Tionetsetse kuti khalidwe lathu lisapangitse anthu kunena zoipa. (1 Pet. 2:12) Ngati ntchito zathu zatsiku ndi tsiku n’zolemekeza Mulungu amene timalambira, ndiye kuti tidzakhala ngati nyali zoikidwa pamwamba, kukopera ena kumalo achisungiko amene Yehova wapereka.—Mat. 5:14-16.