Pulogalamu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera
1 Manyuzipepala, ma TV, kapena mawailesi ndi aphunzitsi kusukulu amalimbikitsa kwambiri kukhala olemera mwakuthupi, koma Mawu a Mulungu amatilimbikitsa “Kukhala Olemera mu Ntchito Zabwino.” (1 Tim. 6:18, NW) Umenewu ndiwo mutu wa pulogalamu ya tsiku la msonkhano wapadera kuyambira mu September 2002. Kodi tikaphunzira zotani ku msonkhano umenewu?
2 Woyang’anira dera akafotokoza zimene zimafunika kuti “Tikhale Anthu Amene Mulungu Amati ndi Olemera,” ndipo adzafunsa anthu ena amene akuyesetsa kupeza chuma chauzimu. Mlendo amene adzakamba nkhani pamsonkhanowu adzasonyeza mu nkhani yake yoyamba momwe anthu a Mulungu akuchitira “Ntchito Zabwino mu Nthaŵi Yotuta Ino.” Tonse tikalimbikitsidwa kuona momwe tingathandizire kwambiri mu ntchito yotuta ya Mulungu, imene ikuchitika masiku ano.
3 Timasangalala kwambiri kuona achinyamata achikristu akufunafuna chuma chauzimu! Zimenezi zimalemekeza Yehova ndipo zimathandiza achinyamata kuyala maziko abwino kuti adzapeze mwayi wa mautumiki ena m’tsogolo muno. Mbali yakuti “Kuyamikira Achinyamata Chifukwa cha Ntchito Zabwino Potamanda Yehova” idzaunika ntchito zabwino zimene achinyamata achikristu a m’deralo akhala akuchita.
4 Kodi chingachitike n’chiyani ngati tichita ntchito zabwino? Mlendo adzakamba zimenezi mu nkhani yake yomaliza yakuti, “Pitirizani Kuchita Ntchito Zabwino Kuti Yehova Akudalitseni.” Adzakamba mbali zinayi zimene tingapeze madalitso ochuluka: (1) patokha, (2) monga banja, (3) monga mpingo, ndipo (4) monga gulu la padziko lonse.
5 Amene anadzipatulira kwa Yehova adzakhala ndi mwayi wobatizidwa. Ngati mwakonzeka kuchita zimenezi, uzani mwamsanga woyang’anira wotsogolera wanu.
6 Akalengeza tsiku la msonkhanowu kwanuko, fulumirani kukonzekera kuti mudzapezekepo. Yesetsani kufika mofulumira kuti mukaimbe nawo nyimbo yotsegulira ndiponso mukapemphere nawo. Kupezeka ndi kumvetsera mwatcheru pulogalamu yonse ya tsiku la msonkhano wapadera kudzatilimbikitsa kupitiriza kuyenda m’njira imene imatipangitsa kukhala anthu amene Mulungu wathu, Yehova amawaona kukhala olemeradi.