Kodi Mungalole Kuti Nyumba Yanu Igwiritsidwe Ntchito?
1 M’zaka 100 zoyambirira, Akristu ambiri analola kuti nyumba zawo zigwiritsidwe ntchito kuchitiramo misonkhano yachikristu. (1 Akor. 16:19; Akol. 4:15; Filem. 1, 2) Masiku ano mipingo ina ilibe malo okwanira ochitirako Phunziro la Buku la Mpingo ndi misonkhano yokonzekera utumiki wa kumunda. Chifukwa cha zimenezi, magulu ena a phunziro la buku amakhala ndi anthu 30 kapena kuposerapo. Nambala imeneyi imaposeratu anthu 15 amene amafunika pakagulu kalikonse.
2 Mwayi Wapadera: Kodi mwaganizapo zoti nyumba yanu azichitiramo Phunziro la Buku la Mpingo? Chipinda chabwino kuchigwiritsa ntchito chiyenera kukhala chachikulu bwino, chosamalika, chowala bwino, komanso chopita bwino mphepo. Phunziro la buku ndi msonkhano wa mpingo ndipo ndi njira imodzi imene Yehova waika yophunzitsira anthu ake. Chotero, ndi mwayi wapadera ngati phunzirolo likuchitikira m’nyumba yanu. Ambiri akuti apindula kwambiri mwauzimu chifukwa cholola kuti nyumba zawo zigwiritsidwe ntchito mwa njira imeneyi.
3 Ngati mukuona kuti nyumba yanu ikuyenerera, musazengereze, kauzeni akulu. Iwo angakhale akufunafuna malo ena ogwiritsa ntchito. Ngati sikungatheke kuchitira phunziro la buku m’nyumba yanu, kodi mungamachitiremo misonkhano yokonzekera utumiki wa kumunda? Ngakhale ngati panopa sipakufunika malo, akulu angakonde kudziŵa kuti nyumba yanu angaigwiritse ntchito. Mwina mwayiwu ungadzakupezeni m’tsogolo.
4 Onetsani Khalidwe Labwino: Pamene akusonkhana m’nyumba ya munthu wina, aliyense afunika kulemekeza katundu wa munthuyo. Makolo azionetsetsa kuti ana awo akukhala m’chipinda chochitiramo phunziro, osati kumaloŵa m’zipinda zina m’nyumbamo. M’pofunikanso kuganizira achinansi oyandikana nawo nyumba. Tifunika kusamala kuti tisamawasokoneze.—2 Akor. 6:3, 4; 1 Pet. 2:12.
5 Ahebri 13:16 amatilimbikitsa kuti tisaiŵale “kuchitira chokoma ndi kugaŵira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.” Kulola kuti nyumba yanu izigwiritsidwa ntchito kuchitiramo msonkhano wa mpingo ndi njira yabwino yogaŵana ndi ena zokoma komanso ‘yolemekezera Yehova ndi chuma chanu.’—Miy. 3:9.