Pulogalamu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera
Masiku ano pali nkhani zambiri zofotokoza zimene tingachite kuti mtima wathu ukhale wathanzi n’cholinga choti tikhale ndi moyo wosangalala komanso wautali. Kusamalira mtima wathu wophiphiritsira n’kofunika kwambiri kuposa mtima wathu weniweni. Motero, mutu wa pulogalamu ya tsiku la msonkhano wapadera umene udzayamba mu September 2003 ndi woyenerera. Mutu wake ndi wakuti: “Kutumikira Yehova ndi Mtima Wangwiro.” (1 Mbiri 28:9) Kodi tingayembekezere kukaphunzira zotani?
Woyang’anira dera adzakamba nkhani yakuti “Kuthandiza Ena Kukondwera Potumikira Yehova.” Anthu amene adzafunsidwa adzasonyeza chimwemwe chimene chimapezeka pokulitsa chidwi ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo kwa anthu amene akufuna kutumikira Yehova. Mosakayika, onse amene adzapezekapo adzalimbikitsidwa ndi nkhani ya mlendo yoyamba yakuti, “Kutchinjiriza Mitima Yathu M’dziko la Mavutoli.” Chigawo cha m’maŵa chidzatha ndi nkhani ya ubatizo.
Masana, nkhani yakuti “Thandizani Ena,” idzafotokoza mmene tingathandizire anthu ena. Kodi makolo angatetezere bwanji mitima ya ana awo ku zinthu zimene zingawaononge, ndipo angawathandize bwanji kuyandikira kwa Yehova? Nkhani yakuti “Thandizani Ana Anu Kukondwera mwa Yehova,” idzafotokoza mfundo zothandiza ndipo idzasonyeza mmene munthu angachitire zimenezo.
Kodi tikugwiritsa ntchito zonse zimene Yehova amapereka zimene zingatithandize kuti mtima wathu wophiphiritsira ukhale wathanzi ndiponso wolimba? Nkhani yomaliza ya mlendo yakuti, “Khalanibe ndi Mtima Wangwiro Potumikira Yehova,” idzatchula mbali zinayi zofunika kwambiri zimene zimatithandiza kuti tikhalebe ndi moyo wabwino wauzimu. Kodi timathera nthaŵi yochuluka bwanji ndiponso tikusonyeza khama lotani pankhani ya pemphero lochokera pansi pa mtima, kuphunzira Mawu a Mulungu, kulalikira mwachangu, ndi kusonkhana ndi Akristu ena? Kodi tingapite patsogolo m’mbali zimenezi?
Yehova akutipempha kuti: “Lozetsa mtima wako kumwambo, ndi makutu ako ku mawu a nzeru.” (Miy. 23:12) Konzani pakalipano zoti mukapezeke pa tsiku lopindulitsa limeneli la malangizo a m’Malemba. Kuchita zimenezi kudzakulimbitsani kuti mupitirizebe kutumikira Yehova ndi mtima wangwiro ndiponso mokondwera.