‘Tumikirani Yehova Mokondwera’
1. Kodi n’chiyani chimene chimapatsa atumiki a Yehova chimwemwe chachikulu?
1 “Kondwerani mwa Ambuye nthaŵi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani,” anatero mtumwi Paulo. (Afil. 4:4) Timakhala ndi chimwemwe chachikulu chifukwa chokhala ndi mwayi wolalikira nawo uthenga wabwino komanso wothandiza anthu onga nkhosa kuti alambire Yehova. (Luka 10:17; Mac. 15:3; 1 Ates. 2:19) Komabe, kodi tingatani tikaona kuti nthaŵi zina sitikukhala ndi chimwemwe mu utumiki wathu?
2. Kodi kukumbukira amene anatipatsa ntchito yathu kungatipatse bwanji chimwemwe?
2 Mulungu ndi Amene Anatipatsa Ntchitoyi: Kumbukirani kuti Yehova ndi amene anatipatsa ntchito yathu yolalikira. Kunena zoona, ndife anthu amwayi kwambiri chifukwa chokhala “antchito anzake a Mulungu” pa ntchito yolengeza uthenga wa Ufumu ndi kupanga ophunzira. (1 Akor. 3:9) Kristu Yesu ali nafe limodzi mu ntchito imeneyi, imene sidzabwerezedwanso. (Mat. 28:18-20) Angelo nawonso akuchita nawo ntchito imeneyi, ndipo akugwira nafe limodzi ntchito yaikulu yotuta mwauzimu imene ikuchitika pakadali pano. (Mac. 8:26; Chiv. 14:6) Malemba komanso zokumana nazo za anthu a Mulungu zimapereka umboni wochita kuonekeratu woti Yehova akudalitsa ntchito imeneyi. Choncho, tikamalalikira, timapita ‘monga [otumidwa ndi, NW] Mulungu pamaso pa Mulungu, [ndipo] timalankhula mwa Kristu.’ (2 Akor. 2:17) Zimenezi n’zopatsa chimwemwe kwambiri!
3. Kodi pemphero limatithandiza bwanji kuti tikhalebe ndi chimwemwe potumikira Mulungu?
3 Pemphero n’lofunika kwambiri kuti tikhale ndi chimwemwe potumikira Mulungu. (Agal. 5:22) Popeza tingathe kugwira ntchito ya Mulungu pokhapokha ngati iye atatipatsa mphamvu yake, tiyenera kumupempha ndi mtima wonse kuti atipatse mzimu wake, umene amaupereka mooloŵa manja kwa anthu amene amamupempha. (Luka 11:13; 2 Akor. 4:1, 7; Aef. 6:18-20) Kupempherera utumiki wathu kudzatithandiza kuti tikhalebe ndi maganizo abwino pamene ena akukana uthenga wathu. Kudzatithandiza kupitirizabe kulalikira molimba mtima komanso mwansangala.—Mac. 4:29-31; 5:40-42; 13:50-52.
4. Kodi kukonzekera bwino kumatithandiza bwanji kuwonjezera chimwemwe chathu polalikira, ndipo kodi njira zina zothandiza pokonzekera n’ziti?
4 Konzekerani Bwino: Njira yabwino yothandiza kuti tiwonjezere chimwemwe chathu tikamachita nawo utumiki ndi kukonzekera bwino. (1 Pet. 3:15) Kukonzekera koteroko sikuti kumachita kufuna nthaŵi yaitali. Zimatenga mphindi zochepa chabe kuti muŵerenge chitsanzo cha ulaliki umene mungagwiritse ntchito pogaŵira magazini atsopano kapena ulaliki umene mungagwiritse ntchito pogaŵira buku limene mukufuna kugaŵira. Kuti mupeze mawu oyamba oyenera, mungaŵerenge buku la Kukambitsirana kapena Utumiki Wathu wa Ufumu wam’mbuyomu. Ofalitsa ena aona kuti zimawathandiza akalemba ulaliki wachidule pa kapepala. Nthaŵi ndi nthaŵi, amaŵerenga kapepalako kuti akumbukire ulalikiwo. Zimenezi zimawathandiza kuti asakhale ndi mantha ndipo zimawachititsa kukhala odzidalira ndi kulalikira molimba mtima.
5. Kodi chimwemwe chimapindulitsa bwanji ifeyo komanso ena?
5 Chimwemwe chimapindulitsanso m’njira zina zambiri. Kukhala achimwemwe kumathandiza kuti anthu akopeke ndi uthenga wathu. Chimwemwe chimatipatsa mphamvu zoti tithe kupirira. (Neh. 8:10; Aheb. 12:2) Koma, koposa zonse, utumiki wathu wachimwemwe umalemekeza Yehova. Choncho, tiyeni ‘titumikire Yehova mokondwera.’—Sal. 100:2.