Kupereka Umboni Popanda Mawu
1 Popanda mawu, zinthu zimene Yehova analenga zimalengeza zambiri za makhalidwe Ake osaoneka. (Sal. 19:1-3; Aroma 1:20) Chimodzimodzinso ndi khalidwe lathu labwino, makhalidwe achikristu, ndi kaonekedwe kodzilemekeza zimapereka umboni popanda mawu. (1 Pet. 2:12; 3:1-4) Tonsefe tikhale ndi cholinga chakuti ‘tikometsere chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu m’zinthu zonse’ mwa kukhala ndi khalidwe labwino.—Tito 2:10.
2 Kodi anthu opanda ungwiro angakometsere bwanji ziphunzitso za Baibulo? Izi zingatheke pokhapokha Mawu a Mulungu ndiponso mphamvu ya mzimu woyera zitawatsogolera. (Sal 119:105; 143:10) Mawu a Mulungu “ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse.” (Aheb. 4:12) Amalowerera m’kati mwathu ndipo amatithandiza kuvala umunthu watsopano. (Akol. 3:9, 10) Mzimu woyera umatithandiza kukhala ndi makhalidwe abwino, monga chifundo, kukoma mtima, chifatso, ndi chiletso. (Agal. 5:22, 23) Kodi ifeyo tikulola Mawu a Mulungu ndiponso mzimu wake woyera kutitsogolera?—Aef. 4:30; 1 Ates. 2:13.
3 Ena Amaona: Tikamatsatira miyezo ya Yehova ndi kuyesetsa kutengera makhalidwe ake, anthu ena amaona zimenezo. Mwachitsanzo, taganizirani mwamuna wina amene anzake kuntchito amamuseka chifukwa chakuti anali wamfupi. Mlongo wina amene amagwira ntchito mu ofesi yomweyo, amamulemekezabe mwamunayo. Ataona zimenezi, mwamunayo anafunsa mlongoyo chifukwa chiyani anali wosiyana ndi anzake onse. Mlongoyo anamuuza mwamunayo kuti anali ndi khalidwe lotere chifukwa chakuti amatsatira mfundo za m’Baibulo. Anam’fotokozeranso za chiyembekezo chabwino cha Ufumu wa Mulungu. Ndiyeno, mwamunayo anayamba kuphunzira Baibulo ndipo patapita nthawi anabatizidwa. Pamene mwamunayo anabwerera kumudzi kwawo, achibale ake anachita chidwi ndi khalidwe lake labwino, ndipo ambiri a iwo anayamba kuphunzira choonadi.
4 Kaya tili kuntchito, kusukulu, kapena tili panyumba ndi achibale ndiponso achinansi athu, khalidwe labwino pamodzi ndi kupereka kwathu umboni, zithandize ena kulemekeza Mulungu.—Mat. 5:16.