Tsanzirani Khristu Pochita Utumiki
1 Yesu anatipatsa chitsanzo pautumiki wathu. Anasonyeza kambirimbiri ndiponso m’njira zochuluka kuti amakonda kwambiri Mulungu ndi anthu. Iye anaphunzitsa anthu ofatsa choonadi ndipo anachita zinthu zosonyeza chifundo kwa anthu omwe anali ovutika ndiponso oponderezedwa.—Mat. 9:35.
2 Chitsanzo cha Yesu ndiponso Zimene Anaphunzitsa: Yesu sanataye nthawi n’kulowerera m’ndale kapena kuchita ntchito zongothandiza anthu pamoyo wakuthupi basi. Komanso sanalole kuti zinthu zomwe anali kuchita pofuna kungothandiza anthu zisokoneze kapena kuti zimuiwalitse ntchito yake yaikulu. (Luka 8:1) Maganizo ake onse anali pa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, popeza ndi njira yokhayo imene idzathetseretu mavuto a anthu. Yesu anali ndi ntchito yambiri yoti achite koma nthawi yochitira ntchitoyo inali yochepa. Pamene anthu a ku Kaperenao anafuna kuti Yesu akhalebe komweko, iye anati kwa ophunzira ake: “Tiyeni tipite kwina . . . kuti ndikalalikire kumenekonso, pakuti ndicho cholinga chimene ndinabwerera.”—Maliko 1:38.
3 Atatha kuphunzitsa ophunzira ake, Yesu anawatumiza atawapatsa malangizo osapita m’mbali awa: ‘Lalikirani kuti, Ufumu wa kumwamba wayandikira.’ (Mat. 10:7) Iye anaphunzitsa otsatira ake kuti aziika zinthu zaufumu poyamba m’moyo wawo. (Mat. 6:33) Yesu asanapite kumwamba, ananena mawu omaliza kwa ophunzira ake osonyeza bwino zimene iwo anayenera kuchita. Iye anati: “Choncho pitani mukapange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse.”—Mat. 28:19.
4 Kufunika kwa Ufumu: Nkhani yaikulu imene Yesu anali kuphunzitsa inali yonena za Ufumu wa Mulungu, ndipo analimbikitsa ophunzira ake kuti atsatire chitsanzo chake. Zochita za anthu zofuna kuthetsa mavuto sizingapite patali. (Yer. 10:23) Ufumu wa Mulungu, ndi wokhawo umene udzayeretsa dzina la Mulungu ndi kubweretseratu mpumulo kwa anthu. (Mat. 6:9, 10) Kuphunzitsa choonadi cha Ufumu anthu amene “akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zichitidwa pakati [padziko],” kumawathandiza kukhala ndi moyo wosangalala, ndi wokhutiritsa panopo ndiponso amakhala ndi chiyembekezo chodalirika cham’tsogolo.—Ezek. 9:4.
5 Yesu akupitirizabe kutsogolera ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndipo akutitsimikizira kuti adzatithandiza. (Mat. 28:20) Kodi tikuyesetsa kuchita utumiki wathu motsanzira kwambiri utumiki wa Yesu? (1 Pet. 2:21) M’masiku omaliza ovuta ano, tiyeni tichite zonse zomwe tingathe kuti titsatire bwino lomwe chitsanzo chimene Yesu anatisiyira mu utumiki.