Branch Letter
Okondedwa Ofalitsa Ufumu:
Chaka chautumiki changothachi, Yehova wadalitsa munda wathu kwambiri. Mwachitsanzo pa avereji, mipingo itatu yatsopano inakhazikitsidwa mwezi uliwonse. Chifukwa cha kuwonjezeka kumeneku, tamanga Nyumba Yosungira Katundu yatsopano ndi kuwonjezera Chipinda Chodyera kunthambi yathu ku Lilongwe. Tsopano anthu okwana 240 angakhale m’Chipinda Chodyera chimenechi. Malo owonjezerawa amafunika panthawi ya Sukulu Yophunzitsa Utumiki ndi sukulu zina.
Mipingo ya ku Lilongwe inkatumiza anthu oposa 50 ongodzipereka Loweruka lililonse kudzathandiza ntchito zosiyanasiyana. Kuwonjezera pamenepa, antchito odzipereka 13 ochokera m’mayiko 7 anathandiza pantchitoyi. Panopa chifukwa cha ntchito yokonza panja pa Nyumba Yosungira Katunduyi, malo ozungulira akongola kwambiri.
Nyumba Yosungira Katundu yatsopanoyi utali wake ndi wa nyumba ziwiri zosanja. Ili ndi maofesi atatu osanja ndi mashelefu aakulu omwe pangaikidwe makatoni okwana 10,000 a mabuku. Zimenezi zikutanthauza kuti ngati patafunikira, m’nyumbayi tingasungiremo magazini oposa 3.5 miliyoni. Choncho, nyumbayi ndi yokwanira pa ntchito yotumiza chakudya chauzimu ku mipingo yathu yoposa 1,160.
Limodzi ndi inu, tikuyembekezera kulandira madalitso enanso kwa Yehova pamene tayamba chaka chautumiki cha 2009.—1 Akor. 3:6, 7.
Ndife abale anu,
Ofesi ya Nthambi ya Malawi