Phunzitsani M’njira Yosavuta
1. Kodi chofunika n’chiyani kuti tiziphunzitsa mogwira mtima?
1 Kufewetsa zinthu n’kofunika kuti tiphunzitse mogwira mtima. Tikaona mmene Mphunzitsi wa Luso, Yesu, ankaphunzitsira tingathe kukulitsa “luso [lathu] la kuphunzitsa.”—2 Tim. 4:2; Yoh. 13:13.
2. Kodi tingaphunzitse bwanji m’njira yosavuta, ndipo zimenezi zingawakhudze bwanji anthu?
2 Fotokozani Zinthu Mosavuta: Ulaliki wa paphiri uli ndi mfundo za choonadi zimene palibe munthu wina anazilankhulapo. Ndipo zonse zinafotokozedwa mosavuta. (Mat., machap. 5-7) Anthu amene ankamvetsera Yesu “anazizwa ndi kaphunzitsidwe kake.” Asilikali amene anatumidwa kuti akam’gwire anakhudzidwa kwambiri ndi kaphunzitsidwe kake moti anati: “Palibe munthu analankhulapo ngati iyeyu n’kale lonse.” (Mat. 7:28, 29; Yoh. 7:46) Kuti anthu ena choonadi chiwafike pamtima, sitifunikira kugwiritsa ntchito mawu ovuta kapena mafanizo okhala ndi mfundo zambiri. N’zotheka kufotokoza bwinobwino choonadi pogwiritsa ntchito mawu ozolowereka.
3. N’chifukwa chiyani anthu ena amafotokoza zinthu zambiri nthawi imodzi, nanga tingapewe bwanji zimenezi?
3 Dziwani Kuchuluka kwa Zimene Mungaphunzitse Nthawi Imodzi: Yesu ankaganizira omvera ake kuti aone kuchuluka kwa zimene angaphunzitse panthawi imodzi. (Yoh. 16:12) Tiyenera kuchita chidwi ndi omvera athu komanso kukhala okonzeka kusintha makamaka tikamalalikira kwa achibale, anthu amene angoyamba kumene kuchita chidwi ndi choonadi ndiponso ana. Tiyenera kupewa kufotokoza mfundo zambirimbiri ngakhale wophunzirayo akuoneka kuti akumvetsera mwachidwi. Anthu oona mtima adzapitirizabe kuphunzira za Mulungu woona, Yehova.—Yoh. 17:3; 1 Akor. 3:6.
4. N’chifukwa chiyani n’kopindulitsa kufotokoza mfundo zofunika m’malo mofotokoza zinthu zambiri?
4 Fotokozani Mfundo Zofunika: Yesu anafotokoza zimene ankaphunzitsa mosavuta ndipo anapewa kufotokoza zinthu zochuluka nthawi imodzi. Iye atanena kuti: “Onse ali m’manda a chikumbutso . . . adzatuluka,” anaona kuti sinali nthawi yoti afotokoze mwatsatanetsatane zimene zidzachitikire anthu omwe adzaukitsidwe. (Yoh. 5:28, 29) Tikamachititsa maphunziro a Baibulo, tiyenera kufotokoza mfundo zofunika ndi kupewa chizolowezi chofotokoza mfundo zimene sizikutchulidwa m’buku limene tikuphunziralo.
5. Kodi tidzakhala ndi madalitso otani tikamaphunzitsa m’njira yosavuta?
5 Tikuyamikira kwambiri kuti Yehova watiphunzitsa m’njira yosavuta zinthu zonse zimene tifunika kudziwa. (Mat. 11:25) Tiyeni tiziyesetsa kuphunzitsa m’njira yosavuta ndipo tidzasangalala ndi utumiki wobala zipatso.