Ntchito Yathu Yaikulu
1. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ntchito yolalikira inali yofunika kwambiri kwa iye?
1 Ntchito yaikulu ya Yesu inali kulalikira. Iye anachita ntchito imeneyo mwakhama kwambiri moti anali kuyenda mitunda italiitali m’dziko lonse la Palestina, kulalikira kwa anthu ambiri mmene angathere. Iye ankakhala moyo wosalira zambiri kuti azithera nthawi yake yambiri pa kulalikira ndiponso kuti maganizo ake onse akhale pa ntchito imeneyi. (Mat. 8:20) Khamu la anthu litayesa kumuletsa kuti asachoke, n’cholinga choti achiritse anthu odwala, iye anati: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu ku mizinda inanso, chifukwa ndizo anandituma kudzachita.”—Luka 4:43.
2. N’chifukwa chiyani ntchito yolalikira inali yofunika kwambiri kwa Yesu?
2 N’chifukwa chiyani ntchito yolalikira inali yofunika kwambiri kwa Yesu? Nkhani yaikulu kwa iye inali kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova. (Mat. 6:9) Iye ankakonda Atate wake wakumwamba choncho ankafunitsitsa kukwaniritsa chifuniro Chake ndi kumvera malamulo Ake onse. (Yoh. 14:31) Ankakondanso kwambiri anthu ndipo ankafuna kuwathandiza.—Mat. 9:36, 37.
3. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaona kulalikira kukhala ntchito yathu yaikulu?
3 Tsanzirani Yesu: Zimakhala zovuta kuti tizionabe ntchito yolalikira mmene Yesu ankaionera, chifukwa chakuti pali zinthu zambiri m’dzikoli zimene zimafuna nthawi yathu ndiponso zimene zingatidodometse. (Mat. 24:37-39; Luka 21:34) Choncho, tiyenera kuika mtima wathu pa zinthu zofunika kwambiri ndipo tizikhala ndi nthawi yokonzekera ndi kulowa mu utumiki kawirikawiri. (Afil. 1:10) Tiziyesetsa kukhalabe ndi moyo wosalira zambiri ndiponso tizipewa kugwiritsa ntchito dzikoli mokwanira.—1 Akor. 7:31.
4. N’chifukwa chiyani panopa tiyenera kupitirizabe kugwira ntchito yathu yaikulu?
4 Munthu wanzeru akakhala ndi nthawi yochepa yochitira zinthu, amayamba ndi zinthu zofunika kwambiri. Mwachitsanzo, ngati iye wamva kuti kukubwera mphepo yowopsa yamkuntho, angathere nthawi yake yambiri komanso mphamvu zake kukonza zoti banja lake likhale motetezeka ndiponso kuti achenjeze anthu ena. Angasiye kaye kuchita zinthu zosafunika kwenikweni. Nthawi imene yatsala kuti Aramagedo ibwere yafupika. (Zef. 1:14-16; 1 Akor. 7:29) Kuti tidzipulumutse tokha ndi anthu otimvera, tiyenera kudziyang’anira ndiponso kusamala zimene timaphunzitsa, kaya mu mpingo kapena ayi. (1 Tim. 4:16) Ndithudi, kuti tidzapulumuke tiyenera kupitirizabe kuona kuti ntchito yathu yaikulu ndi yolalikira.