Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb19 February tsamba 3
  • Kodi Mumaona Makhalidwe a Mulungu Osaoneka ndi Maso?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumaona Makhalidwe a Mulungu Osaoneka ndi Maso?
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Nkhani Yofanana
  • Muziphunzira Zambiri Zokhudza Yehova Poona Chilengedwe Chake
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Muzigwiritsa Ntchito Chilengedwe Pophunzitsa Ana Anu Zokhudza Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Mmene Chilengedwe Chimasonyezera Kuti Mulungu Ndi Wachikondi
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • “Makhalidwe a Mulungu Osaoneka ndi Maso Akuonekera Bwino”
    Nsanja ya Olonda—2013
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
mwb19 February tsamba 3

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mumaona Makhalidwe a Mulungu Osaoneka ndi Maso?

Kodi mumachita chidwi mukamaona zimene Mulungu analenga monga maluwa okongola, nyenyezi kapenanso mathithi ochititsa chidwi? Zinthu za m’chilengedwe zimatithandiza kuona makhalidwe a Yehova osaoneka ndi maso. (Aroma 1:20) Tikamaganizira zimene timaona m’chilengedwe, timatha kuzindikira kuti Mulungu ali ndi makhalidwe monga mphamvu, chikondi, nzeru, chilungamo komanso kuwolowa manja.​—Sal. 104:24.

Kodi ndi zinthu zina ziti zimene Mulungu analenga zomwe mumaona tsiku lililonse? Ngakhale zitakhala kuti mumakhala m’tawuni, mukhozabe kuona zinthu monga mbalame kapena mitengo. Kuchita chidwi ndi zimene Yehova analenga kungatithandize kuti tichepetse nkhawa, tiziona mavuto athu moyenera komanso kuti tizikhulupirira kwambiri kuti iye ali ndi mphamvu zotha kutisamalira mpaka kalekale. (Mat. 6:25-32) Ngati muli ndi ana mungachite bwino kuwathandiza kuti azichita chidwi ndi chilengedwe kuti aone makhalidwe abwino a Mulungu. Tikamayamikira zinthu zimene zili m’chilengedwe timayandikira Mlengi wathu.​—Sal. 8:3, 4.

ONERANI VIDIYO YAKUTI ZACHILENGEDWE ZIMATIPHUNZITSA ZA ULEMERERO WA MULUNGU​—KUWALA KOMANSO MITUNDU YA ZINTHU, KENAKO KAMBIRANANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi n’chiyani chimatithandiza kuti tiziona mitundu ya zinthu?

  • N’chiyani chimachititsa kuti zinthu zizioneka monyezimira komanso ngati zikusintha mtundu?

  • N’chifukwa chiyani timaona mitundu yosiyanasiyana m’mlengalenga?

  • Ndi mitundu yochititsa chidwi iti ya zinthu zimene Mulungu analenga yomwe mumaona mukakhala kunyumba kwanu?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kumachita chidwi ndi zinthu zachilengedwe?

Duwa lapinki, gulugufe wabuluu, zipatso, komanso dzuwa likulowa

Kodi kuwala komanso mitundu ya zinthu zimatithandiza bwanji kudziwa makhalidwe a Yehova?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena