CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 AKORINTO 7-9
Kusakhala Pabanja ndi Mphatso
Kwa nthawi yaitali, Akhristu ambiri akhala akunena kuti kusakhala pabanja kumawapatsa mpata wochita zambiri potumikira Yehova. Amanenanso kuti kumawathandiza kuti adziwane ndi anthu ambiri komanso kuti azikonda kwambiri Yehova.
mu 1937, abale ali paulendo wokalalikira ku Australia; mu 1947, mlongo amene anamaliza maphunziro a sukulu ya Giliyadi akufika ku Mexico
m’bale akulalikira ku Brazil; ali ku Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu ku Malawi
MAFUNSO OFUNIKA KUWAGANIZIRA: Ngati simuli pabanja, kodi mungatani kuti muzigwiritsa ntchito nthawi imeneyi mwanzeru?
Kodi abale ndi alongo mumpingo angathandize bwanji anthu amene sali pabanja?