CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 12-14
Pangano Lomwe Limakukhudzani
Yehova anachita pangano ndi Abulahamu. Panganoli linathandiza kuti Yesu ndi odzozedwa akhale ovomerezeka mwalamulo kuti akalamulire ngati mafumu kumwamba
Panganoli linayamba kugwira ntchito m’chaka cha 1943 B.C.E., pamene Abulahamu anawoloka mtsinje wa Firate popita ku Kanani
Panganoli lipitirizabe kugwira ntchito kufikira pamene Ufumu wa Mesiya udzawononge adani onse a Mulungu n’kupereka madalitso kwa mabanja onse a padziko lapansi
Yehova anadalitsa Abulahamu chifukwa anali ndi chikhulupiriro cholimba. Kodi tikuyembekezera kudzalandira madalitso otani chifukwa cha pangano la Abulahamu?