CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 40-41
Yehova Anapulumutsa Yosefe
Yosefe anakhala kapolo komanso anakhala m’ndende kwa zaka pafupifupi 13 Yehova asanamupulumutse. M’malo mokwiya, Yosefe anaphunzira zinthu zambiri zabwino kuchokera pa zimene zinamuchitikira. (Sal. 105:17-19) Iye ankadziwa kuti Yehova sanamusiye. Kodi Yosefe anachita zinthu zabwino ziti ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto?
Iye ankagwira ntchito mwakhama komanso anali wokhulupirika ndipo zimenezi zinachititsa kuti Yehova amudalitse.—Gen. 39:21, 22
Iye ankachita zinthu mokoma mtima kwa ena ndipo sanabwezere anthu omwe anamuchitira nkhanza.—Gen. 40:5-7
Kodi zimene zinamuchitikira Yosefe zingandithandize bwanji kupirira mavuto anga?
Pamene ndikuyembekezera kuti Yehova adzandipulumutse pa Aramagedo, kodi ndi zinthu zabwino ziti zomwe ndingachite ngakhale kuti ndikukumana ndi mavuto?