CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 33-34
Makhalidwe Abwino Kwambiri a Yehova
Mose ankadziwa bwino kwambiri makhalidwe a Yehova ndipo zimenezi zinkamuthandiza kuchita zinthu moleza mtima ndi Aisiraeli. Ifenso tikadziwa bwino makhalidwe a Yehova tikhoza kumachita zinthu mwachifundo ndi Akhristu anzathu.
“Wachifundo ndi wachisomo”: Yehova amasamalira anthu ake mwachikondi kwambiri komanso amawadera nkhawa ngati mmene makolo amachitira ndi ana awo
“Wosakwiya msanga”: Yehova amalezera mtima atumiki ake. Iye amawamvetsa akalakwitsa zinthu ndipo amawapatsa nthawi kuti asinthe
“Wodzaza ndi kukoma mtima kosatha”: Chikondi cha Yehova ndi chokhulupirika moti adzakonda anthu ake mpaka kalekale
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndingatsanzire bwanji chifundo cha Yehova?’