Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb23 September tsamba 16
  • Muzigwiritsa Ntchito Tsamba Loyamba la JW.ORG Mukakhala mu Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzigwiritsa Ntchito Tsamba Loyamba la JW.ORG Mukakhala mu Utumiki
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Mungapezenso Pawebusaiti
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Kodi Munayamba Mwadzifunsapo?
    Galamukani!—2019
  • Mungaphunzirenso Izi
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • “Mfundozi Zindithandiza Kwambiri”
    Galamukani!—2016
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
mwb23 September tsamba 16
Zithunzi za patsamba loyamba la jw.org zokhala ndi nkhani za m’zilankhulo zosiyanasiyana.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzigwiritsa Ntchito Tsamba Loyamba la JW.ORG Mukakhala mu Utumiki

Patsamba loyamba la webusaiti yathu, pamaikidwa nkhani ndi mavidiyo amene anakonzedwa kuti azifika pamtima anthu omwe si a Mboni amene ali ndi mtima wabwino. (Mac 13:48) Zinthu zomwe zimaikidwazi, nthawi zambiri zimakhala nkhani zimene zili m’manyuzi kapena nkhani zimene anthu akulankhulalankhula.

Kodi mungagwiritse ntchito bwanji tsamba loyamba la jw.org mukakhala mu utumiki?

  • Muzilowa pa webusaitiyi pafupipafupi. Muziona nkhani zimene zaikidwa patsamba loyambali pansi pa mutu wakuti “Zina Zimene Zilipo” ndipo muziganizira mmene mungazigwiritsire ntchito pothandiza munthu wachidwi. (Kuti muone nkhani zina zimene zinaikidwa patsambali, dinani pamene alemba kuti “Onani Zambiri.”) Kudziwa zinthu zatsopano zimene zaikidwa pawebusaitiyi, kudzakuthandizani kukhala ndi mfundo zatsopano zimene mungagwiritse ntchito mu utumiki.

  • Muzigwiritsa ntchito nkhani ndi mavidiyo amene aikidwa patsamba loyamba kuti muyambe kukambirana ndi munthu. Nkhani ndi mavidiyowa zingakuthandizeni kudziwa zimene anthu a m’gawo lanu akuganiza.

  • Muzionetsa anthu tsamba loyambali. Muzisonyeza anthu mwachindunji nkhani zimene zilipo komanso muziwathandiza kudziwa mmene angapezere nkhani zina zosiyanasiyana.

  • Muziwatumizira linki. Anthu ena safuna kulankhula nafe pamasom’pamaso koma akhoza kulowa pawebusaiti yathu. Choncho musamazengereze kutumizira anthu linki imene ingawafikitse ku tsamba loyamba, ku nkhani inayake kapena vidiyo imene yaikidwa patsambali.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena