Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp21 No. 1 tsamba 8-9
  • N’chifukwa Chiyani Mulungu Sayankha Mapemphero Ena?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • N’chifukwa Chiyani Mulungu Sayankha Mapemphero Ena?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Tili Ndi Mwayi Wopemphera kwa Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Mmene Mungapezere Chithandizo Kupyolera mwa Pemphero
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Kodi Ndimapemphero Ayani Omwe Amayankhidwa?
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
wp21 No. 1 tsamba 8-9

N’chifukwa Chiyani Mulungu Sayankha Mapemphero Ena?

Yehova Mulungu, yemwe ndi Atate wathu wakumwamba, amafuna komanso amasangalala kumva mapemphero athu ochokera pansi pa mtima. Koma pali zinthu zina zimene zingachititse kuti asayankhe mapemphero athu. Kodi zinthu zake ndi ziti, nanga tiyenera kukumbukira chiyani tikamapemphera? Mfundo za m’Baibulo zotsatirazi zingatithandize pa nkhaniyi.

Anthu kutchalitchi akuwerenga pemphero kuchokera m’buku.

“Popemphera, usanene zinthu mobwerezabwereza.”​—Mateyu 6:7.

Yehova safuna kuti tizingobwereza mapemphero amene taloweza kapena kuwawerenga kuchokera m’buku la mapemphero. Koma amafuna kuti tizilankhula kuchokera mumtima. Taganizirani mmene mungamvere ngati mnzanu atamalankhula nanu mongobwereza mawu omweomwewo tsiku lililonse. Anzanu apamtima sangachite zimenezi koma amamasuka nanu n’kumakuuzani zamumtima mwawo. Tikamapemphera kuchokera mumtima timasonyeza kuti timaona kuti Atate wathu wakumwamba ndi mnzathu.

Munthu akuyang’ana kumwamba pamene akutchova juga.

“Mumapempha koma simulandira, chifukwa mukupempha ndi cholinga choipa.”​—Yakobo 4:3.

Sitingayembekezere kuti Mulungu ayankhe mapemphero athu ngati tapempha zinthu zimene tikudziwa kuti sasangalala nazo. Mwachitsanzo, Yehova amatichenjeza kuti tisamakhale ndi mtima wadyera kapena kukhulupirira mulungu wa Mwayi. (Yesaya 65:11; Luka 12:15) Ndiye ngati munthu wotchova juga atapempha Mulungu kuti achite mphumi, kodi Mulungu angayankhe pempherolo? N’zosachita kufunsa kuti sangayankhe pemphero loterolo. Koma kuti Mulungu ayankhe mapemphero athu, tiyenera kupempha zinthu zogwirizana ndi zimene Baibulo limanena.

M’busa akupempherera asilikali.

“Munthu amene amathawitsa khutu lake kuti asamve chilamulo, ngakhale pemphero lake limakhala lonyansa.”​—Miyambo 28:9.

Kale, Mulungu sankayankha mapemphero a anthu amene sankamvera malamulo ake. (Yesaya 1:15, 16) Ndiye Mulungu sanasinthe. (Malaki 3:6) Ngati tikufuna kuti Mulungu aziyankha mapemphero athu, tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tizimvera malamulo ake. Koma bwanji ngati m’mbuyomu tinachita zinthu zina zoipa? Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Yehova sangamvetserenso mapemphero athu? Ayi. Mulungu adzatikhululukira tikasintha n’kumayesetsa kuchita zimene zimamusangalatsa.​—Machitidwe 3:19.

“Aliyense wofika kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi, ndi kuti amapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.”​—Aheberi 11:6.

Mayi akuwerenga Baibulo.

Sitimangopemphera kuti tikhazike mtima pansi tikakhala ndi nkhawa. Koma tikamapemphera timasonyeza kuti timakhulupirira Mulungu, kumukonda komanso kumulemekeza. Yakobo ananena kuti ngati ‘sitipempha ndi chikhulupiriro tisaganize kuti tidzalandira kanthu kwa Yehova.’ (Yakobo 1:6, 7) Kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba, tiyenera kuchita khama pophunzira Baibulo kuti timudziwe bwino Mulungu. Tikamachita zimenezi tidzadziwa zimene Mulungu amafuna ndipo tidzapemphera ndi chikhulupiriro cholimba.

TISATAYE MTIMA

Ngakhale kuti Mulungu sayankha mapemphero ena, amamvetsera ndiponso kuyankha mapemphero ochokera pansi pa mtima a anthu mamiliyoni ambiri. Baibulo limafotokoza zimene tingachite kuti mapemphero athu akhale ovomerezeka kwa Mulungu. Nkhani yotsatira ifotokoza zimenezi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena