NKHANI YOPHUNZIRA 11
NYIMBO NA. 129 Tipitirizabe Kupirira
Mukhoza Kumatumikirabe Yehova Ngakhale Mutakhumudwitsidwa
“Walimbana ndi mavuto osiyanasiyana chifukwa cha dzina langa.”—CHIV. 2:3.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Nkhaniyi itithandiza kuona kuti tingathe kupitiriza kutumikira Yehova ngakhale titakhumudwitsidwa.
1. Kodi ndi madalitso ati amene timapeza chifukwa chokhala m’gulu la Yehova?
NDI MWAYI waukulu kukhala m’gulu la Yehova masiku otsiriza ovutawa. Pamene zinthu zikuipiraipira m’dzikoli, Yehova watipatsa banja lauzimu logwirizana la abale ndi alongo. (Sal. 133:1) Amatithandizanso kuti tizikhala ndi mabanja olimba. (Aef. 5:33–6:1) Komanso amatipatsa nzeru kuti tizikhala ndi mtendere wa mumtima.
2. Kodi tiyenera kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?
2 Koma tiyenera kuchita khama kuti tipitirizebe kutumikira Yehova mokhulupirika. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa nthawi zina tikhoza kukhumudwa ndi zinthu zimene ena alakwitsa. Tikhozanso kumakhumudwa ngati timalakwitsa zinthu zinazake mobwerezabwereza. Tiyenera kupitiriza kutumikira Yehova ngakhale (1) Mkhristu mnzathu akatilakwira, (2) mwamuna kapena mkazi wathu akatikhumudwitsa, ndiponso (3) tikakhumudwa ndi zimene timalakwitsa. Munkhaniyi tikambirana mbali zitatuzi. Tizionanso zimene tikuphunzira pa chitsanzo cha munthu wokhulupirika wotchulidwa m’Baibulo.
MKHRISTU MNZANU AKAKULAKWIRANI, MUZITUMIKIRABE YEHOVA
3. Kodi ndi vuto liti limene anthu a Yehova amalimbana nalo?
3 Vuto. Akhristu ena amakhala ndi makhalidwe amene satisangalatsa. Ena angatikhumudwitse kapenanso kutichitira zinthu mosatiganizira. Anthu amene amatitsogolera akhoza kulakwitsa zinthu. Zimenezi zingachititse ena kuyamba kukayikira ngati alidi m’gulu la Mulungu. M’malo mopitiriza kutumikira Mulungu “mogwirizana” ndi abale ndi alongo awo, iwo angasiye kuchita zinthu ndi anthu amene awalakwirawo kapenanso kusiya kupita kumisonkhano. (Zef. 3:9) Kodi ndi nzeru kuchita zimenezi? Tiyeni tione zimene tikuphunzira kwa munthu wotchulidwa m’Baibulo yemwe anakumananso ndi zimenezi.
4. Kodi mtumwi Paulo anakumana ndi mavuto ati?
4 Chitsanzo cha m’Baibulo. Mtumwi Paulo ankadziwa kuti abale ndi alongo ake si angwiro. Mwachitsanzo, ena anamuweruza molakwika atayamba kugwirizana ndi mpingo. (Mac. 9:26) Pambuyo pake, ena ankamunenera miseche pofuna kuwononga mbiri yake. (2 Akor. 10:10) Paulo anaonanso munthu wina waudindo akuchita zolakwika zomwe zikanakhumudwitsa anthu ena. (Agal. 2:11, 12) Komanso mnzake wina dzina lake Maliko anamukhumudwitsa kwambiri. (Mac. 15:37, 38) Paulo akanatha kusankha kuti asamagwirizane ndi anthu amene anamukhumudwitsawa. Koma iye anapitiriza kuona zabwino mwa abale ndi alongo akewa ndipo ankatumikirabe Yehova mwakhama. Kodi n’chiyani chinathandiza Paulo kuti apitirizebe kutumikira Yehova?
5. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti Paulo asataye mtima pamene anakhumudwitsidwa ndi abale ndi alongo ake? (Akolose 3:13, 14) (Onaninso chithunzi.)
5 Paulo ankakonda abale ndi alongo ake. Kukonda anthu ena kunamuthandiza kuti aziganizira makhalidwe awo abwino osati zimene amalakwitsa. Chikondi chinamuthandizanso kuti azichita zomwe iyeyo analemba pa Akolose 3:13, 14. (Werengani.) Umboni wake ndi zimene zinachitika pa nkhani ya Maliko. Ngakhale kuti Maliko anamusiya pa ulendo wake woyamba wa umishonale, Paulo sanapitirize kumukwiyira. Patapita nthawi, iye analembera kalata mpingo wa ku Kolose ndipo m’kalatayo analembamo kuti Maliko anali ‘wantchito mnzake komanso amamulimbikitsa.’ (Akol. 4:10, 11) Atamangidwa ku Roma, Paulo anapempha Maliko kuti apite kukamuthandiza. (2 Tim. 4:11) Izi zikusonyeza kuti Paulo ankakhulupirirabe abale ake. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Paulo?
Panali mkangano waukulu pakati pa Paulo, Baranaba ndi Maliko. Koma pambuyo pake Paulo anaisiya nkhaniyi n’kumagwira ntchito bwinobwino ndi Maliko (Onani ndime 5)
6-7. Kodi tingatani kuti tizipitiriza kukonda abale ndi alongo athu ngakhale kuti amalakwitsa zinthu zina? (1 Yohane 4:7)
6 Zimene tikuphunzirapo. Yehova amafuna kuti tisasiye kusonyeza chikondi kwa abale ndi alongo athu. (Werengani 1 Yohane 4:7.) Ngati Mkhristu wina walephera kusonyeza makhalidwe abwino, tizingoona kuti amafuna kutsatira mfundo za m’Baibulo ndipo wangochita zinthu mosaganiza bwino. (Miy. 12:18) Mulungu amakonda atumiki ake okhulupirika ngakhale kuti amalakwitsa zinthu zina. Samasiya kutikonda tikalakwitsa zinazake, ndipo samatisungira chakukhosi. (Sal. 103:9) Choncho tiyenera kumatsanzira Atate wathu yemwe amakhululuka.—Aef. 4:32–5:1.
7 Tizikumbukiranso kuti pamene mapeto akuyandikira tiyenera kumagwirizana ndi abale ndi alongo athu. Tiziyembekezera kuti Akhristufe tikhoza kuzunzidwa kwambiri kapenanso kumangidwa chifukwa cha zimene timakhulupirira. Ngati zimenezi zitatichitikira, tingafune kwambiri kuti abale ndi alongo athu atithandize. (Miy. 17:17) Chitsanzo ndi zomwe zinachitikira Josep,a yemwe ndi mkulu ku Spain. Iye limodzi ndi abale ena anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali. Josep anati: “Tili kundende, zikanakhala zosavuta kukwiyira Mkhristu mnzathu chifukwa chilichonse tinkachitira limodzi. Tinkafunika tizilolerana komanso kukhululukirana ndi mtima wonse. Izi zinatithandiza kuti tizigwirizana komanso kutetezana. Tinkakhala ndi akaidi amene satumikira Yehova. Pa nthawi ina ndinavulala mkono ndipo anandiika chikhakha, moti sindinkatha kuchita zinthu zina pandekha. Koma m’bale wina ankandichapira komanso kundithandiza m’njira zosiyanasiyana. Ndimaona kuti anandisonyeza chikondi pa nthawi yovuta kwambiri.” Tilitu ndi zifukwa zabwino kwambiri zotichititsa kuthetsa kusamvana panopa.
MWAMUNA KAPENA MKAZI WANU AKAKUKHUMUDWITSANI, MUZITUMIKIRABE YEHOVA
8. Kodi anthu okwatirana amakumana ndi vuto liti?
8 Vuto. Mabanja onse amakumana ndi mavuto. Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti amene ali m’banja amakumana ndi “mavuto pa moyo wawo.” (1 Akor. 7:28) Zili choncho chifukwa chakuti banja ndi mgwirizano wa anthu awiri omwe si angwiro. Ndipo anthuwo amakhala osiyana makhalidwe, zimene amakonda ndiponso zimene amadana nazo. Angakhalenso osiyana zikhalidwe ndi kumene anakulira. Nthawi zina angakhalenso ndi makhalidwe amene sankaonekera asanalowe m’banja. Zinthu ngati zimenezi zikhoza kuyambitsa mavuto. M’malo moti aliyense azizindikira vuto lake n’kumayesetsa kuti alikonze, angayambe kuimba mlandu mnzake. Ndipo akhoza kumaona kuti kupatukana kapena kuthetsa ukwatiwo ndiye njira yothetsera mavutowo. Koma kodi zimenezo ndi zoona?b Tiyeni tikambirane za munthu wotchulidwa m’Baibulo amene anapirira mavuto aakulu kwambiri m’banja.
9. Kodi Abigayeli anakumana ndi vuto lotani?
9 Chitsanzo cha m’Baibulo. Abigayeli anakwatiwa ndi Nabala yemwe Baibulo limanena kuti anali wouma mtima komanso wopanda khalidwe. (1 Sam. 25:3) Ziyenera kuti zinali zovuta kwa Abigayeli kukhala ndi mwamuna ngati ameneyu. Kodi Abigayeli anali ndi njira yachidule yothetsera banja lake? Inde. Iye akanatha kuchita zimenezi pamene Davide, amene anali mfumu yam’tsogolo ya Isiraeli, anabwera kuti adzaphe mwamuna wake chifukwa chonyoza Davideyo ndi anyamata ake. (1 Sam. 25:9-13) Abigayeli akanatha kuthawa n’kusiya Davide kuti apange zomwe ankafuna. M’malomwake anapita kukalankhula ndi Davide kuti asaphe Nabala. (1 Sam. 25:23-27) N’chifukwa chiyani anachita zimenezi?
10. Kodi mwina n’chiyani chinathandiza Abigayeli kuti azipirira mavuto omwe ankakumana nawo m’banja?
10 Abigayeli ankakonda Yehova ndipo ankalemekeza mfundo zake zokhudza ukwati. Mosakayikira, iye ankadziwa zimene Yehova anauza Adamu ndi Hava pamene ankayambitsa banja loyambali. (Gen. 2:24) Abigayeli ankadziwa kuti Yehova amaona kuti ukwati ndi wopatulika. Iye ankafuna kusangalatsa Mulungu ndipo zimenezi zinamulimbikitsa kuti achite zonse zimene akanatha kuti ateteze banja lake ndiponso mwamuna wake. Anachita zinthu mwamsanga kuti Davide asaphe Nabala. Analinso wokonzeka kupepesa pa zinthu zimene iyeyo sanalakwitse. N’zosakayikitsa kuti Yehova ankakonda Abigayeli yemwe anali wolimba mtima komanso wosadzikonda. Kodi amuna ndi akazi angaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Abigayeli?
11. (a) Kodi Yehova amayembekezera kuti anthu apabanja azichita chiyani? (Aefeso 5:33) (b) Kodi mukuphunzira chiyani pa zimene Carmen anachita kuti ateteze banja lake? (Onaninso chithunzi.)
11 Zimene tikuphunzirapo. Yehova amafuna kuti anthu okwatirana azilemekeza banja ngakhale mwamuna kapena mkazi wawo atakhala wovuta. Mulungu amasangalala akamaona anthu apabanja akuyesetsa kuthetsa mavuto awo ndiponso kusonyezana chikondi ndi ulemu. (Werengani Aefeso 5:33.) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Carmen. Atakhala m’banja kwa zaka 6, iye anayamba kuphunzira ndi a Mboni za Yehova ndipo pambuyo pake anabatizidwa. Carmen anati: “Mwamuna wanga sanasangalale nazo. Iye ankachita nsanje poona kuti ndimamusiya n’kupita kukatumikira Yehova. Choncho ankandinyoza komanso kundiopseza kuti andisiya.” Ngakhale zinali choncho, Carmen anapitirizabe kupirira m’banja lake. Kwa zaka 50, anayesetsa kuti azikonda komanso kulemekeza mwamuna wake. Iye anati: “Pamene zaka zinkapita, ndinaphunzira kuchita zinthu mwanzeru komanso kulankhula mosamala kwa mwamuna wanga. Ndinkadziwa kuti ukwati ndi wopatulika kwa Yehova choncho ndinkachita chilichonse chomwe ndingathe kuti ndiuteteze. Sindinaganizepo zosiyana ndi mwamuna wanga chifukwa ndimakonda Yehova.”c Ngati mutakumana ndi mavuto m’banja lanu musamakayikire kuti Yehova adzakuthandizani kuti mupirire.
Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Abigayeli anachita kuti ateteze banja lake? (Onani ndime 11)
MUKALAKWITSA ZINAZAKE, MUZIPITIRIZABE KUTUMIKIRA YEHOVA
12. Kodi tingakumane ndi vuto liti tikachita tchimo lalikulu?
12 Vuto. Munthu angathe kukhumudwa kwambiri ngati atachita tchimo lalikulu. Baibulo limanena kuti machimo athu angachititse kuti tikhale ndi mtima “wosweka komanso wophwanyika.” (Sal. 51:17) M’bale wina dzina lake Robert anachita khama kwa zaka zambiri kuti ayenerere kukhala mtumiki wothandiza. Komabe iye anachita tchimo lalikulu ndipo ankaona kuti wakhumudwitsa Yehova. Robert anati: “Chikumbumtima chinkandivutitsa kwambiri moti zinkangokhala ngati ndasenza katundu wolemera. Zimenezi zinachititsa kuti ndisamamve bwino ngakhale pang’ono. Ndinkalira komanso kupemphera kwa Yehova. Pa nthawiyo ndinkaganiza kuti Mulungu sangataye nthawi kumvetsera mapemphero anga chifukwa ndinali nditamukhumudwitsa.” Tikachita tchimo tikhoza kutaya mtima chifukwa chakuti mtima wathu wosweka ungatichititse kuganiza kuti Yehova watitaya. (Sal. 38:4) Ngati munamvapo choncho, tiyeni tikambirane chitsanzo cha munthu wotchulidwa m’Baibulo yemwe anapitirizabe kutumikira Yehova ngakhale kuti analakwitsa kwambiri zinthu zina.
13. Kodi mtumwi Petulo analakwitsa kwambiri zinthu ziti, nanga n’chiyani chinachititsa zimenezi?
13 Chitsanzo cha m’Baibulo. Pa usiku womaliza wa Yesu, mtumwi Petulo analakwitsa zinthu zingapo zomwe zinachititsanso kuti alakwitse kwambiri zinthu zina. Choyamba, Petulo anasonyeza kudzidalira ponena modzitama kuti adzakhalabe wokhulupirika ngakhale atumwi enawo atamusiya Yesu. (Maliko 14:27-29) Kenako ali m’munda wa Getsemane, Petulo analephera kukhala maso. (Maliko 14:32, 37-41) Pambuyo pake anathawa gulu la anthu litabwera kudzagwira Yesu. (Maliko 14:50) Pomaliza, Petulo anakana katatu kuti sakudziwa Yesu, mpaka anafika polumbirira bodzali. (Maliko 14:66-71) Kodi Petulo anatani atadziwa kuti walakwitsa kwambiri zinthu? Iye anasweka mtima ndipo analira kwambiri mwina chifukwa chodziimba mlandu. (Maliko 14:72) Kodi mukuganiza kuti Petulo anamva bwanji patangopita maola ochepa pamene Yesu ankaphedwa? Iye ayenera kuti ankadziona kuti ndi wachabechabe.
14. Kodi n’chiyani chinathandiza Petulo kuti apitirizebe kutumikira Yehova? (Onani chithunzi chapachikuto.)
14 Pali zifukwa zingapo zimene zinathandiza Petulo kuti apitirizebe kutumikira Yehova. Iye sanadzipatule koma anapita kwa abale ake ndipo n’kutheka kuti anamulimbikitsa. (Luka 24:33) Kuwonjezera pamenepo, Yesu ataukitsidwa anaonekera kwa Petulo, mwina n’cholinga choti amulimbikitse. (Luka 24:34; 1 Akor. 15:5) Pambuyo pake, m’malo mokalipira Petulo chifukwa cha zimene analakwitsa, Yesu anauza mnzakeyu kuti adzalandira maudindo akuluakulu. (Yoh 21:15-17) Petulo anadziwa kuti walakwitsa kwambiri koma sanataye mtima. N’chiyani chinamuthandiza? Iye ankadziwa kuti Mbuye wake Yesu sanasiye kumukonda. Komanso abale ake auzimu anapitiriza kumuthandiza. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Petulo?
Lemba la Yohane 21:15-17 likusonyeza kuti Yesu sanasiye kukonda Petulo ndipo izi zinalimbikitsa Petuloyo kuti apitirize kutumikira Yehova (Onani ndime 14)
15. Kodi Yehova amafuna kuti tisamakayikire chiyani? (Salimo 86:5; Aroma 8:38, 39) (Onaninso chithunzi.)
15 Zimene tikuphunzirapo. Yehova amafuna kuti tisamakayikire zoti iyeyo amatikonda komanso kutikhululukira. (Werengani Salimo 86:5; Aroma 8:38, 39.) Tikachimwa timadziimba mlandu ndipo zimenezi ndi zomveka. Koma sitiyenera kuganiza kuti si ife oyenera kukondedwa kapena kukhululukidwa. M’malomwake tiyenera kufufuza thandizo mwamsanga. Robert yemwe tamutchula kale uja anati: “Ndinachimwa chifukwa chakuti ndinkadalira mphamvu zanga kuti ndipewe mayesero.” Iye anazindikira kuti ankafunika kuuza akulu. Robert anati: “Nditangochita zimenezi, akuluwo anandithandiza kudziwa kuti Yehova amandikonda. Iwonso anasonyeza kuti amandikonda. Anandithandiza kukhulupirira kuti Yehova sananditaye.” Ifenso tisamakayikire kuti Yehova amatikonda komanso kutikhululukira tikalapa machimo athu, kupempha thandizo komanso kuyesetsa kuti tisabwereze zimene tinalakwitsazo. (1 Yoh. 1:8, 9) Kukhulupirira zimenezi kungatithandize kuti tisamataye mtima tikapunthwa kapena kugwa.
Kodi mumatani kapena mudzatani akulu akamakuthandizani? (Onani ndime 15)
16. N’chifukwa chiyani mukufunitsitsa kupitiriza kutumikira Yehova?
16 Yehova amayamikira kwambiri tikamayesetsa kuti tizimutumikira masiku omaliza ovutawa. Iye akhoza kutithandiza kuti tipitirizebe kumutumikira ngakhale titakhumudwitsidwa. Tikhoza kumakonda abale ndi alongo athu komanso kuwakhululukira akatilakwira. Tingasonyeze kuti timakonda kwambiri Mulungu komanso kulemekeza mfundo zake tikamayesetsa kuthetsa mavuto m’banja lathu. Tikachita tchimo, tizipempha Yehova kuti atithandize, tizivomereza kuti amatikonda komanso kutikhululukira ndiponso tizipitirizabe kumutumikira. Tisamakayikire kuti tidzapeza madalitso ambiri ngati “sitisiya kuchita zabwino.”—Agal. 6:9.
KODI TINGATANI KUTI TIZIPITIRIZABE KUTUMIKIRA YEHOVA . . .
Mkhristu mnzathu akatilakwira?
mwamuna kapena mkazi wathu akatikhumudwitsa?
tikalakwitsa zinazake?
NYIMBO NA. 139 Yerekezerani Kuti Muli M’dziko Latsopano
a Mayina ena asinthidwa.
b Mawu a Mulungu salimbikitsa kupatukana ndipo amafotokoza momveka bwino kuti anthu akapatukana sakhala ndi ufulu wokwatira kapena kukwatiwanso. Koma pali mavuto ena akuluakulu omwe angachititse Akhristu kupatukana. Onani mawu a kumapeto 4, “Kodi Okwatirana Angapatukane pa Zifukwa Ziti?” mu buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale.
c Kuti mupeze chitsanzo china, onani vidiyo ya pa jw.org yakuti Tisamapusitsidwe ndi Mtendere Wosakhalitsa—Darrel ndi Deborah Freisinger.