3 Mʼchaka cha 15 cha ulamuliro wa Kaisara Tiberiyo, Pontiyo Pilato anali bwanamkubwa wa Yudeya. Herode+ anali wolamulira chigawo cha Galileya. Filipo mʼbale wake anali wolamulira chigawo cha madera a Itureya ndi Tirakoniti. Ndipo Lusaniyo anali wolamulira chigawo cha Abilene.