3 Tsopano ana aakaziwa akadzakwatiwa ndi amuna a mafuko ena a ana a Isiraeli, ndiye kuti cholowa chawo chidzachotsedwa ku cholowa cha makolo athu, ndipo chidzawonjezedwa ku cholowa cha fuko limene aliyense adzakwatiweko. Zikadzatero ndiye kuti cholowa chathu cha malo chidzachepa.+