23 Pamenepo Elikana mwamuna wake+ anamuuza kuti: “Chita zimene ukuona kuti n’zabwino kwa iwe.+ Ukhale pakhomo kufikira mwanayo atasiya kuyamwa, ndipo Yehova akwaniritse mawu ake.”+ Choncho mkaziyo anakhalabe pakhomo ndipo anapitiriza kulera mwana wake kufikira atasiya kuyamwa.+