12 Abale awo ogwira ntchito panyumbapo+ analipo 822. Panalinso Adaya mwana wa Yerohamu.+ Yerohamu anali mwana wa Pelaliya, Pelaliya anali mwana wa Amuzi, Amuzi anali mwana wa Zekariya, Zekariya anali mwana wa Pasuri,+ ndipo Pasuri anali mwana wa Malikiya.+