3 Pakuti mwa kukoma mtima kwakukulu kumene ndinapatsidwa, ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire kuposa mmene muyenera kudziganizira.+ Koma aliyense aziganiza m’njira yakuti akhale munthu woganiza bwino,+ malinga ndi chikhulupiriro+ chimene Mulungu wamupatsa.+