9 koma anandiuza motsimikiza kuti: “Kukoma mtima kwakukulu kumene ndakusonyeza n’kokukwanira,+ pakuti mphamvu yanga imakhala yokwanira iweyo ukakhala wofooka.”+ Choncho, ndidzadzitamandira mosangalala kwambiri pa kufooka kwanga,+ kuti mphamvu ya Khristu ikhalebe pamutu panga ngati hema.