Lachisanu, October 31
Atatewo amakukondani chifukwa munandikonda ndipo mwakhulupirira kuti ine ndinabwera monga nthumwi ya Mulungu.—Yoh. 16:27.
Yehova amafunitsitsa kuuza anthu omwe amawakonda kuti amasangalala nawo. Malemba amatchula nthawi ziwiri pomwe iye anauza Yesu kuti ndi Mwana wake wokondedwa ndipo amasangalala naye. (Mat. 3:17; 17:5) Kodi mungakonde kumva Yehova akukutsimikizirani kuti amasangalala nanu? Iye salankhula nafe mwachindunji koma amatilankhula kudzera m’Mawu ake. ‘Tingamve’ mawu a Yehova onena kuti amasangalala nafe tikamawerenga mawu a Yesu m’mabuku a Uthenga Wabwino. Yesu ankatsanzira ndendende makhalidwe a Atate wake. Choncho tikamawerenga kuti Yesu ankasangalala ndi otsatira ake okhulupirika, omwe sanali angwiro, timadziwa kuti Yehova amasangalalanso ndi ifeyo. (Yoh. 15:9, 15) Tikakumana ndi mavuto sizitanthauza kuti Mulungu sakusangalala nafe. M’malomwake, zimenezi zimatipatsa mwayi wosonyeza kuti timakonda kwambiri Mulungu ndipo timamukhulupirira.—Yak. 1:12. w24.03 28 ¶10-11
Loweruka, November 1
Mʼkamwa mwa ana ndi mwa makanda mutuluke mawu otamanda.—Mat. 21:16.
Ngati ndinu makolo, muzithandiza ana anu kukonzekera ndemanga zogwirizana ndi msinkhu wawo. Nthawi zina pamisonkhano timaphunzira nkhani zikuluzikulu monga zokhudza mavuto a m’banja kapena makhalidwe. Komabe pangathe kukhala ndime imodzi kapena ziwiri zomwe mwana akhoza kuyankhapo. Komanso muzithandiza ana anu kumvetsa chifukwa chake sangalozedwe nthawi iliyonse yomwe akweza dzanja. Kuwafotokozera zimenezi kungawathandize kuti asamakhumudwe ena akalozedwa m’malo mwa iwowo. (1 Tim. 6:18) Tonsefe tingakonzekere ndemanga zomwe zingalemekeze Yehova komanso zingalimbikitse Akhristu anzathu. (Miy. 25:11) Ngakhale kuti nthawi zina tingafotokoze mwachidule zimene zinatichitikirapo, tizipewa kulankhula kwambiri zokhudza ifeyo. (Miy. 27:2; 2 Akor. 10:18) M’malomwake, tiziyesetsa kuganizira kwambiri zokhudza Yehova, Mawu ake komanso anthu ake monga gulu. w23.04 24-25 ¶17-18
Lamlungu, November 2
Choncho tisapitirize kugona ngati mmene ena onse akuchitira, koma tikhalebe maso ndipo tikhalebe oganiza bwino.—1 Ates. 5:6.
Chikondi n’chofunika kuti tikhalebe maso komanso tiziganiza bwino. (Mat. 22:37-39) Kukonda Mulungu kumatithandiza kuti tizipirira tikamagwira ntchito yolalikira ngakhale pamene kuchita zimenezi kungatibweretsere mavuto. (2 Tim. 1:7, 8) Chifukwa chokonda anthu omwe satumikira Yehova, timapitirizabe kulalikira ngakhalenso kudzera pafoni komanso polemba makalata. Sitifooka chifukwa timayembekezera kuti tsiku lina, anthu amenewa adzasintha n’kuyamba kuchita zinthu zabwino. (Ezek. 18:27, 28) Kukonda anthu kumaphatikizapo kukonda Akhristu anzathu. Timasonyeza chikondichi ‘potonthozana ndi kulimbikitsana.’ (1 Ates. 5:11) Mofanana ndi asilikali, omwe amathandizana pa nthawi ya nkhondo, ifenso timalimbikitsana. Sitingakhumudwitse mwadala abale ndi alongo athu kapenanso kuwabwezera zoipa. (1 Ates. 5:13, 15) Timasonyezanso chikondi polemekeza abale omwe amatsogolera mumpingo.—1 Ates. 5:12. w23.06 10 ¶6; 11 ¶10-11