Loweruka, November 1
Mʼkamwa mwa ana ndi mwa makanda mutuluke mawu otamanda.—Mat. 21:16.
Ngati ndinu makolo, muzithandiza ana anu kukonzekera ndemanga zogwirizana ndi msinkhu wawo. Nthawi zina pamisonkhano timaphunzira nkhani zikuluzikulu monga zokhudza mavuto a m’banja kapena makhalidwe. Komabe pangathe kukhala ndime imodzi kapena ziwiri zomwe mwana akhoza kuyankhapo. Komanso muzithandiza ana anu kumvetsa chifukwa chake sangalozedwe nthawi iliyonse yomwe akweza dzanja. Kuwafotokozera zimenezi kungawathandize kuti asamakhumudwe ena akalozedwa m’malo mwa iwowo. (1 Tim. 6:18) Tonsefe tingakonzekere ndemanga zomwe zingalemekeze Yehova komanso zingalimbikitse Akhristu anzathu. (Miy. 25:11) Ngakhale kuti nthawi zina tingafotokoze mwachidule zimene zinatichitikirapo, tizipewa kulankhula kwambiri zokhudza ifeyo. (Miy. 27:2; 2 Akor. 10:18) M’malomwake, tiziyesetsa kuganizira kwambiri zokhudza Yehova, Mawu ake komanso anthu ake monga gulu. w23.04 24-25 ¶17-18
Lamlungu, November 2
Choncho tisapitirize kugona ngati mmene ena onse akuchitira, koma tikhalebe maso ndipo tikhalebe oganiza bwino.—1 Ates. 5:6.
Chikondi n’chofunika kuti tikhalebe maso komanso tiziganiza bwino. (Mat. 22:37-39) Kukonda Mulungu kumatithandiza kuti tizipirira tikamagwira ntchito yolalikira ngakhale pamene kuchita zimenezi kungatibweretsere mavuto. (2 Tim. 1:7, 8) Chifukwa chokonda anthu omwe satumikira Yehova, timapitirizabe kulalikira ngakhalenso kudzera pafoni komanso polemba makalata. Sitifooka chifukwa timayembekezera kuti tsiku lina, anthu amenewa adzasintha n’kuyamba kuchita zinthu zabwino. (Ezek. 18:27, 28) Kukonda anthu kumaphatikizapo kukonda Akhristu anzathu. Timasonyeza chikondichi ‘potonthozana ndi kulimbikitsana.’ (1 Ates. 5:11) Mofanana ndi asilikali, omwe amathandizana pa nthawi ya nkhondo, ifenso timalimbikitsana. Sitingakhumudwitse mwadala abale ndi alongo athu kapenanso kuwabwezera zoipa. (1 Ates. 5:13, 15) Timasonyezanso chikondi polemekeza abale omwe amatsogolera mumpingo.—1 Ates. 5:12. w23.06 10 ¶6; 11 ¶10-11
Lolemba, November 3
[Yehova] akanena kanthu, kodi angalephere kuchita?—Num. 23:19.
Njira imodzi yomwe tingalimbitsire chikhulupiriro chathu ndi kuganizira mozama zokhudza dipo. Dipo ndi lomwe limatitsimikizira kuti malonjezo a Mulungu adzakwaniritsidwa. Tikamaganizira mosamala chifukwa chake dipo linaperekedwa komanso zimene zinalowetsedwapo, timayamba kukhulupirira kwambiri kuti lonjezo la Mulungu loti tidzakhala ndi moyo wosatha m’dziko labwino lidzakwaniritsidwa. N’chifukwa chiyani tikutero? Kodi panafunika chiyani kuti dipo liperekedwe? Yehova anatumiza Mwana wake wokondedwa woyamba kubadwa komanso mnzake wapamtima, kuti adzabadwe monga munthu wangwiro padzikoli. Ali padzikoli, Yesu anapirira mavuto osiyanasiyana. Kenako anazunzidwa komanso kufa imfa yowawa. Apatu Yehova analipira mtengo wokwera kwambiri. Mulungu wathu wachikondi sakanalola kuti Mwana wake avutike n’kufa pongofuna kuti tidzakhale ndi moyo wabwino koma waufupi. (Yoh. 3:16; 1 Pet. 1:18, 19) Chifukwa choti anapereka mtengo wokwera chonchi, Yehova adzaonetsetsa kuti tidzakhale ndi moyo wosatha m’dziko latsopano. w23.04 27 ¶8-9