Lachitatu, September 17
Osangalala ndi anthu amene akhululukidwa zochita zawo zosamvera malamulo ndipo machimo awo akhululukidwa.—Aroma 4:7.
Mulungu amakhululuka kapena kuphimba machimo a anthu omwe amamukhulupirira. Iye amawakhululukira kotheratu moti sawerengeranso machimo awo. (Sal. 32:1, 2) Amawaona kuti ndi opanda cholakwa komanso olungama chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Ngakhale kuti Abulahamu, Davide ndi atumiki ena okhulupirika ankaonedwa kuti ndi olungama, iwo anali adakali ochimwa. Koma chifukwa cha chikhulupiriro chawo, Mulungu ankawaona kuti ndi opanda cholakwa poyerekezera ndi anthu omwe sankamutumikira. (Aef. 2:12) Mtumwi Paulo anafotokoza bwino m’kalata yake zoti chikhulupiriro n’chofunika kwambiri kuti munthu akhale pa ubwenzi ndi Mulungu. Ndi mmenenso zinalili ndi Abulahamu ndi Davide. Choncho ifenso chikhulupiriro chingatithandize kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. w23.12 3 ¶6-7
Lachinayi, September 18
Nthawi zonse tizitamanda Mulungu. . . . Kuchita zimenezi kuli ngati nsembe imene tikupereka kwa Mulungu ndipo timagwiritsa ntchito milomo yathu polengeza dzina lake.—Aheb. 13:15.
Masiku ano Akhristu onse ali ndi mwayi wopereka nsembe kwa Yehova pogwiritsa ntchito nthawi, mphamvu ndiponso zinthu zawo pomutumikira. Tingasonyeze kuti timayamikira mwayi wathu wolambira Yehova poyesetsa kuchita zonse zomwe tingathe pomutumikira. Mtumwi Paulo anatchula zinthu zosiyanasiyana zokhudza kulambira kwathu zimene sitiyenera kuzinyalanyaza. (Aheb. 10:22-25) Zinthu zake zikuphatikizapo kupemphera kwa Yehova, kulengeza poyera chiyembekezo chathu, kusonkhana pamodzi ngati mpingo ndiponso kulimbikitsana, ‘makamaka panopa pamene tikuona kuti tsiku la [Yehova] likuyandikira.’ Pofuna kutsindika, chakumapeto kwa buku la Chivumbulutso, mngelo wa Yehova ananena kawiri kuti: “Lambira Mulungu.” (Chiv. 19:10; 22:9) Tiyeni tizikumbukira nthawi zonse mfundo zozama za choonadi zokhudza kachisi wamkulu wauzimu ndipo tiziyamikira mwayi wolambira Mulungu wathu wamkulu, Yehova. w23.10 29 ¶17-18
Lachisanu, September 19
Tiyeni tipitirize kukondana.—1 Yoh. 4:7.
Tonsefe tiyenera ‘kupitiriza kukondana.’ Koma tiyenera kukumbukira kuti Yesu anachenjeza kuti “chikondi cha anthu ambiri chidzazirala.” (Mat. 24:12) Yesu sankatanthauza kuti chikondi cha ophunzira ake ambiri chidzachepa. Ngakhale zili choncho, tiyenera kukhala osamala kuti tisatengere mtima wopanda chikondi womwe ndi wofala m’dzikoli. Poganizira mfundo imeneyi, tiyeni tikambirane funso lina lofunika. Kodi pali njira yodziwira ngati timakonda kwambiri abale athu? Njira imodzi yodziwira ngati timakonda kwambiri abale athu ndi kuona zimene timachita pa moyo wathu. (2 Akor. 8:8) Mtumwi Petulo anatchula chimodzi mwa zinthuzi pomwe anati: “Koposa zonse, muzikondana kwambiri chifukwa chikondi chimakwirira machimo ochuluka.” (1 Pet. 4:8) Choncho zimene timachita abale athu akalakwitsa zinthu, zingasonyeze ngati timawakonda kwambiri kapena ayi. w23.11 10-11 ¶12-13