Lachisanu, September 19
Tiyeni tipitirize kukondana.—1 Yoh. 4:7.
Tonsefe tiyenera ‘kupitiriza kukondana.’ Koma tiyenera kukumbukira kuti Yesu anachenjeza kuti “chikondi cha anthu ambiri chidzazirala.” (Mat. 24:12) Yesu sankatanthauza kuti chikondi cha ophunzira ake ambiri chidzachepa. Ngakhale zili choncho, tiyenera kukhala osamala kuti tisatengere mtima wopanda chikondi womwe ndi wofala m’dzikoli. Poganizira mfundo imeneyi, tiyeni tikambirane funso lina lofunika. Kodi pali njira yodziwira ngati timakonda kwambiri abale athu? Njira imodzi yodziwira ngati timakonda kwambiri abale athu ndi kuona zimene timachita pa moyo wathu. (2 Akor. 8:8) Mtumwi Petulo anatchula chimodzi mwa zinthuzi pomwe anati: “Koposa zonse, muzikondana kwambiri chifukwa chikondi chimakwirira machimo ochuluka.” (1 Pet. 4:8) Choncho zimene timachita abale athu akalakwitsa zinthu, zingasonyeze ngati timawakonda kwambiri kapena ayi. w23.11 10-11 ¶12-13
Loweruka, September 20
Muzikondana.—Yoh. 13:34.
Sitingamvere lamulo la Yesu lakuti tizikondana ngati timakonda ena mumpingo n’kumalephera kukonda ena. N’zoona kuti tingamagwirizane kwambiri ndi ena kuposa ena, ngati mmenenso Yesu ankachitira. (Yoh. 13:23; 20:2) Koma mtumwi Petulo akutikumbutsa kuti tiyenera kuyesetsa kuti ‘tizikonda abale’ onse ngati anthu a m’banja lathu. (1 Pet. 2:17) Petulo anatilimbikitsa kuti ‘tizikondana kwambiri kuchokera mumtima.’ (1 Pet. 1:22) Apa mawu akuti ‘kukondana kwambiri’ akutanthauza kukonda winawake ngakhale pamene zili zovuta kutero. Mwachitsanzo, bwanji ngati m’bale watikhumudwitsa m’njira inayake? Mwachibadwa timafuna kumubwezera osati kumusonyeza chikondi. Komatu Petulo anaphunzira kwa Yesu kuti kubwezera sikusangalatsa Mulungu. (Yoh. 18:10, 11) Iye analemba kuti: “Munthu akakuchitirani choipa musamabwezere ndi choipa, akakuchitirani chipongwe musamabwezere ndi chipongwe. M’malomwake muziwachitira zabwino.” (1 Pet. 3:9) Muzilola kuti kukonda kwambiri ena, kuzikulimbikitsani kuti muzikomera mtima komanso kuganizira ena. w23.09 28-29 ¶9-11
Lamlungu, September 21
Nawonso akazi akhale . . . ochita zinthu mosapitirira malire, okhulupirika pa zinthu zonse.—1 Tim. 3:11.
Timadabwa kuona mmene mwana amakulira mofulumira kwambiri n’kukhala munthu wamkulu. Zimaoneka kuti kukula kumeneku kumangochitika pakokha. Koma kukula mwauzimu sikumachitika pakokha. (1 Akor. 13:11; Aheb. 6:1) Kuti munthu akule mwauzimu amafunika kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Timafunikanso mzimu woyera kuti utithandize kukhala ndi makhalidwe abwino, kukhala ndi luso lochitira zinthu bwino komanso kukonzekera maudindo athu am’tsogolo. (Miy. 1:5) Polenga anthu, Yehova anawalenga mwamuna ndi mkazi. (Gen. 1:27) Mwamuna ndi mkazi amaoneka mosiyana komanso amakhala osiyana m’njira zina. Mwachitsanzo, Yehova analenga amuna ndi akazi kuti azikwaniritsa maudindo osiyana. Choncho iwo amafunika kukhala ndi makhalidwe komanso maluso amene angawathandize kukwaniritsa bwino maudindo awowo.—Gen. 2:18. w23.12 18 ¶1-2