SEPTEMBER 22-28
MLALIKI 1-2
Nyimbo Na. 103 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Pitirizani Kuphunzitsa M’badwo Wotsatira
(10 min.)
[Onerani VIDIYO yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Mlaliki.]
M’badwo uliwonse umakhala ndi udindo wophunzitsa m’badwo wotsatira (Mla 1:4; w17.01 27-28 ¶3-4)
Tikamaphunzitsa komanso kupatsa ena zochita, timawathandiza kuti nawonso azisangalala chifukwa chogwira ntchito mwakhama potumikira Yehova (Mla 2:24)
Musamalephere kuphunzitsa abale achinyamata chifukwa choopa kuti adzakulandani maudindo amene mumasangalala nawo
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Mla 1:1—Kodi Baibulo limatanthauza chiyani likamanena kuti Solomo anali “wosonkhanitsa”? (it “Mlaliki” ¶1)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Mla 1:1-18 (th phunziro 11)
4. Ulendo Woyamba
(2 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Pezani nkhani yomwe ingamusangalatse. Konzani zoti mudzalankhulanenso. (lmd phunziro 3 mfundo 5)
5. Ulendo Woyamba
(2 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Kambiranani nkhani imodzi yopezeka pagawo lakuti “Choonadi Chomwe Timakonda Kuphunzitsa Anthu” pogwiritsa ntchito njira yofotokozedwa mu zakumapeto A, m’kabuku kakuti Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa. (lmd phunziro 2 mfundo 3)
6. Ulendo Wobwereza
(2 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Yankhani funso limene mwininyumba anafunsa pa ulendo wapita. (lmd phunziro 9 mfundo 5)
7. Kuphunzitsa Anthu
(5 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Musonyezeni mmene phunziro la Baibulo limachitikira, ndipo konzani zoti mudzapitirize ulendo wina. (lmd phunziro 10 mfundo 3)
Nyimbo Na. 84
8. Mfundo Zitatu Zofunika pa Nkhani Yophunzitsa Ena
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Chikondi chimatilimbikitsa kuphunzitsa ena n’cholinga choti tikwanitse kugwira ntchito imene Yehova anatipatsa
M’Baibulo muli zitsanzo zabwino zambiri zomwe zimatithandiza kudziwa zimene tingachite pa nkhani yophunzitsa ena. Tingaphunzire zambiri tikaona mmene Samueli anaphunzitsira Sauli, mmene Eliya anaphunzitsira Elisa, mmene Yesu anaphunzitsira ophunzira ake komanso mmene Paulo anaphunzitsira Timoteyo. Koma Yehova ndi amene ali mphunzitsi wabwino kwambiri kuposa aliyense. Kodi tingaphunzire chiyani kuchokera pa chitsanzo chake?
Onerani VIDIYO yakuti Muzitsanzira Yehova pa Nkhani Yophunzitsa Ena (Yoh 5:20)—Kachigawo Kake. Kenako funsani funso ili:
Kodi ndi zinthu zitatu ziti zimene tingaphunzire kwa Yehova tikaona mmene amaphunzitsira ena?
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 20-21