SEPTEMBER 15-21
MIYAMBO 31
Nyimbo Na. 135 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Kodi Tingaphunzire Chiyani Kuchokera pa Malangizo Achikondi a Mayi?
(10 min.)
Muziphunzitsa ana anu maganizo a Yehova pa nkhani ya kugonana komanso banja (Miy 31:3, 10; w11 2/1 19 ¶7-8)
Muziphunzitsa ana anu maganizo a Yehova pa nkhani ya kumwa mowa (Miy 31:4-6; ijwhf nkhani na. 4 ¶11-13)
Muziphunzitsa ana anu kuti azithandiza ena ngati mmene Yehova amachitira (Miy 31:8, 9; g17.6 9 ¶5)
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Miy 31:10-31—Kodi n’chiyani chinkathandiza Aisiraeli kuloweza Malemba a Chiheberi? (w92 11/1 11 ¶7-8)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Miy 31:10-31 (th phunziro 10)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Yambani kukambirana ndi munthu amene wanena kapena kukuchitirani zinazake zabwino, kapenanso mwamuona akuchitira winawake zabwino. (lmd phunziro 5 mfundo 3)
5. Ulendo Woyamba
(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambiranani nkhani imodzi yopezeka pagawo lakuti “Choonadi Chomwe Timakonda Kuphunzitsa Anthu” mu zakumapeto A, m’kabuku kakuti Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa. (lmd phunziro 1 mfundo 4)
6. Ulendo Wobwereza
(5 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Itanirani munthu amene walandira Nsanja ya Olonda Na. 1 2025 kuti adzamvetsere nkhani yapadera. (lmd phunziro 7 mfundo 4)
Nyimbo Na. 121
7. Muzithandiza Ana Anu Kugwiritsa Ntchito Zipangizo Zamakono Mwanzeru
(8 min.) Nkhani yokambirana.
Kodi munayamba mwaonapo mwana wamng’ono akugwiritsa ntchito mapulogalamu a pafoni kapena patabuleti? Zimaoneka kuti ana savutika kugwiritsa ntchito mapulogalamuwa. Nthawi zambiri sangafunike kuwathandiza kudziwa mmene angagwiritsire ntchito zipangizo zamakono, koma nthawi zonse amafunika kuwathandiza kuti azizigwiritsa ntchito mwanzeru.
Onerani VIDIYO yakuti Muzigwiritsa Ntchito Nthawi Mwanzeru. Kenako funsani mafunso awa:
N’chifukwa chiyani n’zofunika kudziikira malire a nthawi yomwe tingamagwiritse ntchito zipangizo zamakono?
Kodi nthawi yathu timafunikanso kuigwiritsa ntchito pa zinthu zina ziti?
Mukamakhazikitsa malamulo m’banja lanu, muzigwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo, osati zimene makolo ena amachita. (Aga 6:5) Mwachitsanzo, dzifunseni kuti:
Kodi zochita za mwana wanga zimasonyeza kuti ndi wodziletsa komanso wozindikira moti akhoza kumagwiritsa ntchito foni yanga kapenanso kukhala ndi yakeyake?—1Ak 9:25
Kodi ndizilola mwana wanga kugwiritsa ntchito chipangizo chamakono pamene ali yekhayekha?—Miy 18:1
Kodi ndi mapulogalamu komanso mawebusaiti ati amene ndingamulole kuti azigwiritsa ntchito, nanga ndizimuletsa ati?—Aef 5:3-5; Afi 4:8, 9
Kodi angafunike kumawagwiritsa ntchito kwa nthawi yaitali bwanji kuti azipezanso nthawi yochitira zinthu zina zofunika komanso zosangalatsa?—Mla 3:1
8. Zofunika Pampingo
(7 min.)
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 18-19