Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wt mutu 7 tsamba 60-69
  • Zimene Timaphunzira Chifukwa Chakuti Mulungu Walola Kuipa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Timaphunzira Chifukwa Chakuti Mulungu Walola Kuipa
  • Lambirani Mulungu Woona Yekha
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa cha Dzina Lake Lalikulu
  • ‘Ha! Kuya Kwake kwa Nzeru za Mulungu!’
  • Mwayi Wosonyeza Kudzipereka Kwathu
  • Zimene Timaphunzira m’Kuloleza kwa Mulungu Kuipa
    Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • Chotandizira Kupirira Pobvutika
    Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo
  • Kupirira Mavuto Kuli Ndi Ubwino Wake
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Ncifukwa Ninji Mulungu Wakulola Kuipa Kupitirizabe Mpaka Lero?
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
Onani Zambiri
Lambirani Mulungu Woona Yekha
wt mutu 7 tsamba 60-69

Mutu 7

Zimene Timaphunzira Chifukwa Chakuti Mulungu Walola Kuipa

“MASIKU a zaka za moyo wanga ali oŵerengeka ndi oipa,” linatero kholo lakale Yakobo. (Genesis 47:9) Yobu ananenanso mawu onga ameneŵa kuti munthu “ngwa masiku oŵerengeka, nakhuta mavuto.” (Yobu 14:1) Mofanana ndi iwo, ambirife takumana ndi mavuto, kupanda chilungamo, ngakhalenso ngozi. Komatu, kubadwa kwathu sikunali chifukwa chakuti Mulungu anasowa chilungamo. N’zoona kuti maganizo athu ndiponso matupi athu si angwiro, ndiponso sitikukhala m’Paradaiso monga mmene Adamu ndi Hava analili. Koma kodi chikanachitika n’chiyani Yehova akanati awaphe atangopanduka? N’zoona kuti sikukanakhala matenda, chisoni, kapena imfa, komanso mtundu wa anthu nawo sukanakhalapo. Sitikanabadwa. Mwachifundo chake Mulungu anapatsa Adamu ndi Hava mpata wobereka ana, ngakhale kuti anaŵa anatengera kupanda ungwiro kwawo. Ndipo kudzera mwa Kristu, Yehova anakonza kuti tipezenso chimene Adamu anataya, moyo wosatha pa dziko lapansi la paradaiso.—Yohane 10:10; Aroma 5:12.

2 N’zolimbikitsatu kwambiri kuti tikutha kuyembekezera kudzakhala ndi moyo kosatha m’dziko latsopano la Paradaiso, momwe simudzakhala matenda, chisoni, kupweteka, imfa, ndiponso anthu oipa! (Miyambo 2:21, 22; Chivumbulutso 21:4, 5) Koma mwa zimene zili m’Baibulo timaphunzira kuti ngakhale kuti kupulumuka kwathu n’kofunika kwambiri kwa ife ndiponso kwa Yehova, pali china chofunika koposa.

Chifukwa cha Dzina Lake Lalikulu

3 Dzina la Mulungu likuphatikizidwa pokwaniritsa cholinga chake chokhudza dziko lapansi ndi anthu. Dzina limenelo, Yehova, limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhala.” Motero dzina lake limaimira mbiri yake monga Wolamulira Wamkulu, Wamkulu pokhala ndi zolinga ndi kuzikwaniritsa, ndiponso monga Mulungu wa choonadi. Chifukwa cha udindo wa Yehova, kuti chilengedwe chonse chikhale pamtendere ndi pabwino, m’pofunika kuti dzina lake limodzi ndi zimene limaphatikizapo zipatsidwe ulemu wonse umene zimafunika kupatsidwa ndiponso kuti aliyense akhale womvera kwa iye.

4 Atalenga Adamu ndi Hava, Yehova anawapatsa ntchito yoti agwire. Ananena momveka kuti cholinga chake sichinali kokha kuti agonjetse dziko lapansi, mwakutero kufutukula malire a Paradaiso, komanso chinali choti alidzaze ndi ana awo. (Genesis 1:28) Kodi cholinga chimenechi chinali kudzalephereka chifukwa cha kuchimwa kwawo? Ngati Yehova wamphamvuyonseyo akanati asakwaniritse cholinga chake chokhudza dziko lapansili ndi anthu, bwenzi dzina lake litanyozeka kwambiri.

5 Yehova anali atachenjeza Adamu ndi Hava kuti ngati samvera nadya zipatso za mtengo wodziŵitsa zabwino ndi zoipa, iwo adzafa ‘tsiku lomwe’ adzadyalo. (Genesis 2:17) Mogwirizanadi ndi mawu ake, Yehova anawaimba mlandu tsiku lomwelo anachimwa ndipo anawapatsa chilango cha imfa. Kwa Mulungu, Adamu ndi Hava anafa tsiku limenelo. Komabe, kuti cholinga chake chokhudza dziko lapansi chichitike, Yehova anawalola kukhala ndi ana asanafe imfa imene anthufe timaidziŵa. Ngakhale n’choncho, popeza Mulungu angaone zaka 1,000 monga tsiku limodzi, pamene Adamu anafa ali ndi zaka 930 linali lidakali “tsiku” limodzi ndithu. (2 Petro 3:8; Genesis 5:3-5) Motero mawu a Yehova onena za nthaŵi imene adzalandira chilango anatsimikizika kukhala oona, ndipo kufa kwawo sikunalepheretse cholinga chake chokhudza dziko lapansi. Koma kwa kanthaŵi, anthu opanda ungwiro, kuphatikizapo oipa, aloledwa kukhala ndi moyo.

6 Zimene Yehova anauza wolamulira wa ku Igupto m’masiku a Mose zimasonyezanso chifukwa chake Mulungu walola oipa kukhalapobe. Farao ataletsa ana a Israyeli kuchoka mu Igupto, Yehova sanafulumire kumupha. M’dzikolo munagwa Miliri Khumi yomwe inaonetsa mphamvu za Yehova m’njira zodabwitsa. Pochenjeza za mliri wachisanu ndi chiŵiri, Yehova anauza Farao kuti akanatha kusesa Farao ndi anthu ake omwe mosavuta padziko lapansi. Yehova anati: “Koma ndithu chifukwa chake ndakuimika kuti ndikuonetse mphamvu yanga, ndi kuti alalikire dzina langa pa dziko lonse lapansi.”—Eksodo 9:15, 16.

7 Yehova atalanditsa Aisrayeli, dzina lake linamvekadi kutali. (Yoswa 2:1, 9-11) Lerolino, patapita zaka pafupifupi 3,500, zimene anachita nthaŵi imeneyo sizinaiwalikebe. Si dzina lake lokha la Yehova limene linalengezedwa, komanso choonadi chokhudza mwini wake wa dzinalo. Izi zinabukitsa mbiri ya Yehova kuti ndi Mulungu amene amasunga malonjezo ake komanso amachitapo kanthu pothandiza atumiki ake. (Yoswa 23:14) Zinasonyeza kuti chifukwa chakuti ndi wamphamvuyonse, palibe chimene chingalepheretse cholinga chake. (Yesaya 14:24, 27) Motero tingakhale n’chidaliro chakuti posachedwa adzachitapo kanthu m’malo mwa atumiki ake okhulupirika mwa kuwononga dziko lonse loipa la Satana. Kusonyeza mphamvu zonse kumeneko ndiponso ulemerero umene kumabweretsa pa dzina la Yehova sizidzaiwalika. Phindu lake silidzatha.—Ezekieli 38:23; Chivumbulutso 19:1, 2.

‘Ha! Kuya Kwake kwa Nzeru za Mulungu!’

8 M’kalata imene analembera Aroma, mtumwi Paulo anafunsa funso lakuti: “Kodi chilipo chosalungama ndi Mulungu?” Anayankha mwamphamvu kuti: “Musatero ayi.” Ndiyeno ananenetsa kuti Mulungu ndi wachifundo ndipo anatchula zimene Yehova ananena za kulola Farao kukhala ndi moyo kwa kanthaŵi. Paulo anasonyezanso kuti anthufe tili ngati dothi lomwe woumba mbiya akugwiritsa ntchito. Kenako anati: “Ndipo titani ngati Mulungu, pofuna iye kuonetsa mkwiyo wake, ndi kudziŵitsa mphamvu yake, analekerera ndi chilekerero chambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera chiwonongeko? ndi kuti iye akadziŵitse ulemerero wake waukulu pa zotengera zachifundo, zimene iye anazikonzeratu kuulemerero, ndi ife amenenso iye anatiitana, si a mwa Ayuda okhaokha, komanso a mwa anthu amitundu?”—Aroma 9:14 -24.

9 Kuyambira pa kupanduka kwa mu Edene, onse amene atsutsa Yehova ndi malamulo ake akhala “zotengera za mkwiyo zokonzekera chiwonongeko.” Chiyambireni nthaŵi imeneyo, Yehova wazilekerera kwambiri. Oipa anyoza zochita zake, azunza atumiki ake, anapha ngakhale Mwana wake. Posonyeza kudziletsa kwambiri, Yehova wapereka nthaŵi yokwanira kuti chilengedwe chonse chione bwino ngozi imene imakhalapo chifukwa chopandukira Mulungu ndiponso pamene anthu adzilamulira mosadalira Mulungu. Panthaŵi imodzimodziyo, imfa ya Yesu inapereka njira yolanditsira anthu omvera ndiponso ‘yowonongera ntchito za Mdyerekezi.’—1 Yohane 3:8; Ahebri 2:14, 15.

10 Kwa zaka zoposa 1,900 kuchokera pamene Yesu anaukitsidwa, Yehova wapitiriza kulekerera “zotengera za mkwiyo,” sanaziwononge mofulumira. Chifukwa chiyani? Chifukwa chimodzi n’chakuti wakhala akukonzekeretsa amene adzagwirizana ndi Yesu Kristu mu Ufumu wake wakumwamba. Ameneŵa alipo okwanira 144,000, ndipo ndiwo “zotengera zachifundo” zomwe anatchula mtumwi Paulo. Poyamba, anthu achiyuda ndiwo anaitanidwa kuti apange gulu lakumwamba limeneli. Kenako Mulungu anaitana anthu ochokera m’mitundu yachikunja. Yehova sanakakamize aliyense wa ameneŵa kuti azimutumikira. Koma mwa anthu omwe anayamikira makonzedwe ake achikondi, anapatsa ena mwayi wokalamulira limodzi ndi Mwana wake mu Ufumu wa kumwamba. Kukonza gulu lakumwamba limenelo tingati kunatha tsopano.—Luka 22:29; Chivumbulutso 14:1-4.

11 Koma bwanji okhala padziko lapansi? Kulekerera kwa Yehova kwatheketsanso kuti “khamu lalikulu” lisonkhane kuchokera m’mitundu yonse. Iwo tsopano alipo okwana mamiliyoni angapo. Yehova walonjeza kuti gulu lapadziko lapansi limeneli lidzapulumuka kutha kwa dziko lino ndipo lidzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso. (Chivumbulutso 7:9, 10; Salmo 37:29; Yohane 10:16) Pamene nthaŵi ya Mulungu ikwana, namtindi wa anthu akufa adzaukitsidwa ndi kupatsidwa mwayi wokhala nzika za padziko lapansi za Ufumu wa kumwamba. Mawu a Mulungu pa Machitidwe 24:15 amaneneratu kuti: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.”—Yohane 5:28, 29.

12 Kodi pa zonsezi pakusoŵeka chilungamo? Ayi, chifukwa mwa kusawononga oipa, kapena kuti “zotengera za mkwiyo,” Mulungu akuchitira chifundo anthu enanso, mogwirizana ndi cholinga chake. Izi zimasonyeza kuti alidi wachifundo ndi wachikondi. Ndiponso, tikuphunzira zochuluka za Yehova mwiniyo chifukwa chokhala ndi nthaŵi yoona cholinga chake chikuchitika. Timachita chidwi ndi makhalidwe ake osiyanasiyana amene amaoneka, monga chilungamo chake, chifundo chake, kuleza mtima kwake, ndi nzeru zake zamitundumitundu. Mmene Yehova wachitira mwanzeru pankhani ya ulamuliro wa chilengedwe chonse, ufulu wake wolamulira, udzakhala umboni mpaka kalekale wakuti kalamuliridwe kake ndi kabwino zedi. Tikunenera pamodzi ndi mtumwi Paulo kuti: “Ha! kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziŵa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake n’zosalondoleka!”—Aroma 11:33.

Mwayi Wosonyeza Kudzipereka Kwathu

13 Atumiki ambiri a Mulungu amavutika ndi zimene zimawachitikira. Kuvutika kwawo kukupitirira chifukwa Mulungu sanawonongebe oipa ndipo sanabwezeretse zinthu m’malo mwake kwa anthu monga ananenera. Kodi zimenezi ziyenera kutikhumudwitsa? Kapena kodi zinthu zoterozo tiyenera kuziona monga mwayi woti nafenso tisonyeze kuti Mdyerekezi ndi wabodza? Tingathe kuziona moteremu ngati tikumbukira mawu ochonderera aŵa: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” (Miyambo 27:11) Satana, amene amatonza Yehova, ananenetsa kuti ngati anthu atasoŵa zinthu zakuthupi kapena kuvutika m’njira inayake, akhoza kuimba Mulungu mlandu, ngakhalenso kumuchitira mwano. (Yobu 1:9-11; 2:4, 5) Timasangalatsa mtima wa Yehova pamene, mwa kukhulupirika kwathu kwa iye pokumana ndi mavuto, timaonetsa kuti zimenezo si zoona kwa ife.

14 Ngati tidalira Yehova pamene tikumana ndi ziyeso, tingakhale ndi makhalidwe abwino kwambiri. Mwachitsanzo, chifukwa cha zoŵaŵa zimene Yesu anamva, “anaphunzira kumvera” m’njira imene sanaidziŵe n’kale lonse. Ifenso tingaphunzire pa ziyeso zathu moti tingakulitse kuleza mtima, kupirira, ndiponso kuyamikira kwambiri njira zolungama za Yehova. (Ahebri 5:8, 9; 12:11; Yakobo 1:2-4)

15 Ena adzaona zimene timachita. Mwa zimene timakumana nazo chifukwa cha kukonda kwathu chilungamo, ena a iwo m’kupita kwa nthaŵi angazindikire amene ali Akristu oona lerolino. Ndipo mwa kugwirizana nafe polambira, angakhale oyenera kulandira madalitso a moyo wosatha. (Mateyu 25:34-36, 40, 46) Yehova ndi Mwana wake akufuna anthu akhale ndi mwayi umenewu.

16 Zimakhala bwino kwambiri pamene tiona zinthu zovuta monga mpata wosonyezera kuti ndife odzipereka kwa Yehova ndiponso wothandizira kukwaniritsa zofuna zake. Mwa kuchita zimenezi tingapereke umboni wakuti tikufunadi kukhala pa umodzi ndi Mulungu ndi Kristu. Yesu anapempherera Akristu onse oona kwa Yehova kuti: “Koma sindipempherera iwo okha [ophunzira ake amene anali nawo panthaŵiyo], komanso iwo akukhulupirira Ine chifukwa cha mawu awo; kuti onse akakhale amodzi, monga Inu Atate mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, kuti iwonso akakhale mwa Ife: kuti dziko lapansi likakhulupire kuti Inu munandituma Ine.”—Yohane 17:20, 21.

17 Ngati tikhala okhulupirika kwa Yehova, adzatifupa kwambiri. Mawu ake amati: “Khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse, podziŵa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.” (1 Akorinto 15:58) Ndiponso amati: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.” (Ahebri 6:10) Yakobo 5:11 amati: “Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.” Kodi chitsiriziro cha Yobu chinali chotani? “Yehova anadalitsa chitsiriziro cha Yobu koposa chiyambi chake.” (Yobu 42:10-16) Inde, Yehova “ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.” (Ahebri 11:6) Ndipo ilitu mphoto yaikulu kwambiri imene tiyenera kuyembekezera, moyo wosatha pa dziko lapansi la paradaiso!

18 Ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu udzakonza zowonongeka zonse zimene zachitika kwa anthu m’zaka masauzande ambiri zapitazi. Chimwemwe chimene chidzakhalapo panthaŵiyo chidzaposeratu kuvutika kulikonse kumene tikukumana nako masiku ano. Sitidzasautsidwa pokumbukira zimene tinali kuvutika nazo kale. Maganizo olimbikitsa komanso zochita zabwino zimene anthu azidzachita tsiku ndi tsiku m’dziko latsopano pang’onopang’ono zidzathetsa zokumbukira zopweteka. Yehova akulengeza kuti: “Ndilenga kumwamba kwatsopano [boma latsopano lolamulira anthu la Ufumu wa kumwamba] ndi dziko lapansi latsopano [anthu olungama]; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kuloŵa mumtima. Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthaŵi zonse ndi ichi ndichilenga.” Inde, m’dziko latsopano la Yehova, anthu olungama adzatha kunena kuti: “Dziko lonse lapuma, lili du; iwo ayamba kuyimba nyimbo.”—Yesaya 14:7; 65:17, 18.

Bwerezani Zimene Mwakambirana

• Pamene akulola kuipa, kodi Yehova walemekeza kwambiri dzina lake motani?

• Kodi pamene Mulungu walolera “zotengera za mkwiyo,” ifeyo tathandizidwa bwanji kulandira chifundo chake?

• Kodi tiyenera kuyesetsa kuonanji m’zinthu zimene zimativutitsa?

[Mafunso]

1, 2. (a) Ngati Yehova akanapha opandukawo nthaŵi yomweyo mu Edene, kodi zikanatikhudza motani? (b) Kodi mwachikondi Yehova watikonzera zotani?

3. N’chiyani chikuphatikizidwa pa kukwaniritsidwa kwa cholinga cha Yehova chokhudza dziko lapansi ndi anthu?

4. Kodi cholinga cha Yehova cha dziko lapansi chinaphatikizapo chiyani?

5. (a) Kodi anthu oyambirira anali kudzafa liti ngati atadya zipatso za mtengo wodziŵitsa zabwino ndi zoipa? (b) Kodi Yehova anakwaniritsa motani mawu ake a pa Genesis 2:17 panthaŵi imodzimodziyo akuonetsetsa kuti cholinga chake chokhudza dziko lapansi chichitike?

6, 7. (a) Malinga n’kunena kwa Eksodo 9:15, 16, n’chifukwa chiyani Yehova akulola oipa kukhalapobe kwa kanthaŵi? (b) M’nkhani ya Farao, kodi mphamvu ya Yehova inasonyezedwa motani, nanga dzina Lake linamveka motani? (c) N’chiyani chomwe chidzatsatira pamene dongosolo loipa lilipoli litha?

8. Kodi Paulo anatilimbikitsa kulingalira mfundo zotani?

9. (a) Kodi ndani amene ali “zotengera za mkwiyo zokonzekera chiwonongeko”? (b) N’chifukwa chiyani Yehova wasonyeza kulekerera kwambiri polimbana ndi omutsutsa, nanga pamapeto pake zotsatira zake zidzakhala zopindulitsa motani kwa amene amamukonda?

10. N’chifukwa chiyani Yehova walekerera oipa kwa za 1,900 zapitazi?

11. (a) Kodi ndi gulu liti limene tsopano likupindula ndi kulekerera kwa Yehova? (b) Kodi akufa adzapindula motani?

12. (a) Taphunziranji za Yehova chifukwa cha kulola kwake kuipa? (b) Kodi mukumva bwanji ndi mmene Yehova wachitira ndi nkhani zimenezi?

13. Pamene tikuvutika, kodi umakhala mwayi woti titani, nanga n’chiyani chidzatithandiza kuchita zinthu mwanzeru?

14. Ngati tidalira Yehova pamene tikumana ndi ziyeso, kodi tingapindule motani?

15. Pamene moleza mtima tipirira mavuto, kodi anthu ena angapindule motani?

16. Kodi mmene ife timaonera mavuto zikugwirizana bwanji ndi kukhala pa umodzi?

17. Kodi tingakhale n’chidaliro chotani ngati tili okhulupirika kwa Yehova?

18. Kodi pamapeto pake n’chiyani chidzachitikira zokumbukira zopweteka zilizonse zimene tingakhale nazo?

[Zithunzi patsamba 67]

Yehova “anadalitsa chitsiriziro cha Yobu koposa chiyambi chake”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena