Kuchokera ku Seder Kumka ku Chipulumutso
“Ndidzanyamula chikho chachipulumutso, ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova.”—SALMO 116:13.
1. Kodi ndinyimbo yokoma yabwino kunthaŵi zonse iti imene ingayambukire mtsogolo mwanu?
KODI ndimotani mmene mungasangalalire ndi nyimbo yophatikizapo kukhala kwanu ndi mtsogolo motalika, ndi mwachimwemwe? Kwenikweni, nyimbo yotero imakhala yokondeka nthaŵi zonse. Komabe, inu muli mumkhalidwe wabwino koposa onse kumvetsetsa ndi kusangalala ndi nyimbo yokhala ndi tanthauzo imeneyi. Ayuda amaitcha Hallel (Chitamando). Yophatikizapo Masalmo 113 mpaka 118, imatifulumiza kuimba “Haleluya,” kapena “Kutamanda Ya.”
2. Kodi nyimbo imeneyi imagwiritsidwa ntchito motani, ndipo kodi njogwirizanirana motani ndi Seder?
2 Ayuda amaimba Hallel paphwando lawo la Paskha, kuimba kumene mwachiwonekere kumayambira pamene Mulungu anali ndi kachisi kumene ana ankhosa anaperekedwa nsembe. Lerolino, imaimbidwa m’nyumba za Ayuda panthawi ya phwando la Paskha ndi chakudya chotchedwa Seder. Koma ochepera amene amaiimba pa Seder yawo amapeza tanthauzo lenileni la Salmo 116:13: “Ndidzanyamula chikho chachipulumutso, ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova.” Komabe, kodi nchifukwa ninji, chipulumutso chagwirizanitsidwa ndi Paskha, ndipo kodi kungakhale kwakuti chipulumutso chanu chikuphatikizidwa?
Paskha—Phwando la Chipulumutso
3. Kodi nchiti chomwe chiri chiyambi cha Seder?
3 Kumbukurani kuti Aisrayeli anali akapolo mu Igupto pansi pa Farao wotsendereza. Pomarizira, Mulungu anadzutsa Mose kutsogolera anthu Ake kuufulu. Mulungu atabweretsa miliri isanu ndi inayi pa Aigupto, Mose analengeza wachikhumi. Yehova akakantha mwana wachisamba m’banja lirilonse la Mwigupto. (Eksodo 11:1-10) Komabe, Aisrayeli akasiyidwa. Motani? Iwo akafunikira kupha nkhosa, kuika mwazi wake pazitseko ndi pamphuthu za nyumba, ndi kukhala mkati akumadya chakudya chophatikizapo mwana wankhosa, mkate wopanda chotupitsa, ndi masamba oŵaŵa. Mkati mwa Seder imeneyo, Mulungu “akapitirira” popanda kupha mwana wawo wachisamba.—Eksodo 12:1-13.
4, 5. Kodi Paskha inatsogolera motani kuchipulumutso cha ambiri? (Salmo 106:7-10)
4 Poyankha za mliri wachikhumi umenewu, Farao anauza Mose kuti: “Ukani, tulukani pakati pa anthu anga, inu ndi ana a Israyeli; ndipo mukani katumikireni Yehova.” (Eksodo 12:29-32) Pamene Ahebriwo ndi “anthu osanganizikana” omvera chisoniwo anatuluka, Farao anasintha maganizo ake ndi kuwatsatira. Pamenepo mozizwitsa Mulungu anathandiza anthu ake kuthawa mwa kuwoloka Nyanja Yofiira mmene Farao ndi magulu ake ankhondo olondolawo anafera.—Eksodo 12:38; 14:5-28; Salmo 78:51-53; 136:13-15.
5 Mose adauza Israyeli pa Nyanja Yofiira kuti: “Musawope, chirimikani, ndipo penyani chipulumutso cha Yehova, chimene adzakuchitirani lero.” Pambuyo pake iwo anaimba kuti: “Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, ndipo wakhala chipulumutso changa; Ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza.” (Eksodo 14:13; 15:2) Inde, chilanditso cha Israyeli, ponse pawiri kuchokera pamliri wachikhumi ndi cha pa Nyanja Yofiira, chinali chipulumutso. Wamasalmo adamlongosoladi bwino Yehova kukhala Mulungu “wopereka chipulumutso chachikulu padziko lapansi.”—Salmo 68:6, 20; 74:12-14; 78:12, 13, 22.
6, 7. Kodi nchifukwa ninji Paskha idakasungidwabe, komabe nchifukwa ninji tsopano pali kusiyana ndi Paskha yoyamba?
6 Ahebri adafunikira kusunga Paskha monga chikumbutso cha chipulumutso. Mulungu adaati: “Tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, mudzilisunga la madyerero a Yehova; kumibadwo yanu.” (Eksodo 12:14) Atate anafunikira kukumbutsa banja lawo za chipulumutso chimenecho pachakudya cha Paskha chirichonse, kapena Seder. Yehova analangiza kuti: “Kudzakhala, pamene ana anu adzanena ndi inu, Kutumikirako muli nako nkotani? Mudzati, Ndiko nsembe ya Paskha wa Yehova, amene anapitirira nyumba za ana a Israyeli komweko, pamene anakantha Aigupto, napulumutsa nyumba zathu.”—Eksodo 12:25-27.
7 Chenicheni chakuti Ayuda amachita Paskha wa Seder kufikira lerolino chimatsimikizira kutsimikizirika kwa chochitika chimenecho. Komabe, zina za zizolowezi zawo zimasiyana ndi zimene Yehova analangiza. The Origins of the Seder ikuti: “Baibulo limaphatikizapo nkhani zazikulu za Paskha ndi Phwando la Mkate Wopanda Chotupitsa; komabe, malongosoledwe ameneŵa samagwirizana ndi kusungidwa kwa tchuti kwa pambuyo pake. Kwenikweni, dzoma Labaibulo limasumika maganizo pa nsembe ya paskha, limene silirinso lotchuka m’mabukhu apambuyo pa nthawi ya Baibulo.” Chifukwa chachikulu nchakuti Ayuda alibe kachisi yoperekeramo nsembe zanyama.
8. Kodi nchifukwa chapadera chiti chimene tiri nacho cha kulingalilira Paskha?
8 Akristu angaphunzire mopindulitsa mapwando onse amene Yehova anapereka kwa Israyeli wakale,a koma panthawi ino mbali zina za Paskha ndizimene zikufunikira chisamaliro chathu chapadera. Yesu, Myuda, anasunga Paskha. Pachochitika chotsirizira chimene iye adatero, anatchula phwando laumulungu lokha kaamba ka Akristu—Mgonero wa Ambuye, chikumbutso cha imfa ya Yesu. Chotero phwando Lachikristu limeneli nlogwirizana ndi Paskha.
Zoposa Mwana Wankhosa Wapaskha
9, 10. Kodi ndimotani mmene mwana wankhosa wa Paskha analiri nsembe yapadera, kapena yosiyana?
9 Ahebri 10:1 amatiuza kuti ‘Chilamulo chinali mthunzi wa zinthu zokoma zimene zirinkudza.’ Cyclopædia of Biblical, Theological, and Ecclesiastical Literature, yolembedwa ndi M’Clintock ndi Strong, imati: “Palibe mthunzi wina wa zokoma zirinkudza zopezedwa m’chilamulo zimene zingatsutsane ndi phwando la Paskha.” Kwakukulukulu mwana wankhosa wa Paskha anali ndi tanthauzo limene linapitirira phwando lokumbukira mmene Mulungu anapulumutsira woyamba kubadwa ndiyeno Ahebri onse kutuluka m’Igupto.
10 Mwana wankhosa ameneyo anali wapadera m’mbali zingapo. Mwachitsanzo, nsembe zanyama zambiri za m’Chilamulo cha Mose zinaperekedwa ndi munthu aliyense payekha kaamba ka machimo aumwini kapena kuparamula, ndipo nthuli za nyamazo zinawotchedwa paguwa lansembe. (Levitiko 4:22-35) Nyama ina yochokera ku nsembe yoyamika inaperekedwa kwa wansembe wochita zomwezo kapena kwa ansembe ena. (Levitiko 7:11-38) Komabe, mwana wankhosa waphwandolo, kapena wa Paskha, sanaikidwe paguwa lansembe, ndipo anaperekedwa ndi kagulu ka anthu, kawirikawiri banja, amenenso adafunikira kudya.—Eksodo 12:4, 8-11.
11. Kodi nliti limene linali lingaliro la Yehova kaamba ka mwana wankhosa wa Paskha, ndipo kodi analozera kuchiyani? (Numeri 9:13)
11 Yehova anawona mwana wankhosa wa Paskhayo kukhala wamtengo wapatali kwambiri kotero kuti anamutcha “nsembe yanga.” (Eksodo 23:18; 34:25) Akatswiri anena kuti “nsembe ya Paskha inali nsembe ya Yehova yabwino koposa.” Mosakaikira mwana wankhosa ameneyu analozera, kapena kuphiphiritsira nsembe ya Yesu. Tidziŵa zimenezi popeza kuti mtumwi Paulo anatcha Yesu “paskha wathu [amene] waphedwa.” (1 Akorinto 5:7) Yesu anadziŵika kukhala “Mwanawankhosa wa Mulungu” ndi “Mwanawankhosa wophedwayo.”—Yohane 1:29; Chivumbulutso 5:12; Machitidwe 8:32.
Mwazi Wopulumutsa Moyo
12. Kodi ndimbali iti imene mwazi wa mwana wankhosa udaachita pa Paskha yoyamba?
12 Kalelo mu Igupto mwazi wa mwana wankhosa unali wofunikadi kuchipulumutso. Pamene Yehova anakantha wachisamba, Iye anapitirira nyumba zimene zinali ndi mwazi pamphuthu zake. Ndiponso, popeza kuti Ahebri sanali kulira maliro za ana awo achisamba, iwo anali mumkhalidwe wa kukhoza kuguba kuwoloka Nyanja Yofiira kumka kuufulu.
13, 14. Kodi ndimotani mmene mwazi wa Yesu uliri wopulumutsa moyo ndi wofunika kaamba ka chipulumutso? (Aefeso 1:13)
13 Mwazi ngwophatikizidwanso m’chipulumutso lerolino—mwazi wokhetsedwa wa Yesu. Pamene “paskha, phwando la Ayuda, linali pafupi” mu 32 C.E., Yesu anauza unyinji wa omvetsera kuti: “Iye wakudya thupi langa ndi wakumwa mwazi wanga ali nawo moyo wosatha; ndipo ine ndidzamuukitsa tsiku lomaliza. Pakuti thupi langa ndichakudya ndithu, ndi mwazi wanga ndichakumwa ndithu.” (Yohane 6:4, 54, 55) Amvetseri ake onse Achiyuda akakumbukira Paskha yoyandikirayo ndi kuti mwazi wa mwana wankhosa unagwiritsiridwa ntchito mu Igupto.
14 Pamenepo Yesu sanali kulankhula za zizindikiro zogwiritsiridwa ntchito pa Mgonero wa Ambuye. Phwando latsopano limenelo la Akristu silinayambitsidwe kufikira chaka chimodzi pambuyo pake, chotero ngakhale atumwi amene adamva Yesu mu 32 C.E. sanadziwe konse za iro. Chikhalirechobe, Yesu ankasonyeza kuti mwazi wake unali wofunika kaamba ka chipulumutso chosatha. Paulo analongosola kuti: “Tiri ndi mawomboledwe m’mwazi wake, chikhululukiro cha zochimwa, monga mwa kulemera kwa chisomo chake.” (Aefeso 1:7) Kokha mwa kukhululukidwa pamaziko a mwazi wa Yesu kuti tingathe kukhala ndi moyo kosatha.
Kodi Ndichipulumutso Chiti ndipo Kuti?
15. Kwa Ahebri mu Igupto, kodi nchipulumutso chotani ndi mwaŵi zimene zinali zothekera, ndipo kodi nchiyani chimene sichinali chotheka? (1 Akorinto 10:1-5)
15 Chipulumutso chokhala ndi polekezera chabe chinaphatikizidwa m’Igupto wakale. Palibe aliyense amene anatuluka m’Igupto anayembekezeredwa kupatsidwa moyo wosatha pambuyo pa Kutulukako. Zowona, Mulungu adaika Alevi kukhala ansembe a mtunduwo, ndipo ena a fuko la Yuda anakhala mafumu akanthaŵi, komatu onsewo akamwalira. (Machitidwe 2:29; Ahebri 7:11, 23, 27) Pamene kuli kwakuti ‘gulu losanganizikana’ limenenso linatuluka m’Igupto linalibe mwaŵi wotero, iwo, limodzi ndi Ahebri, anayembekezera kukafika ku Dziko Lolonjezedwa ndi kusangalala ndi moyo wanthaŵi zonse akumalambira Mulungu. Ndiponso, atumiki a Yehova a Chikristu chisanakhale adali ndi maziko a kuyembekezerera kuti, m’nthawi yokwanira, iwo akasangalala ndi moyo wamuyaya padziko lapansi, kumene Mulungu analinganizira anthu kukhala. Ichi chikakhala chogwirizana ndi lonjezo la Yesu pa Yohane 6:54.
16. Kodi nchipulumutso chotani chimene atumiki akalekale a Mulungu adayembekezera?
16 Mulungu anagwiritsira ntchito ena a atumiki ake akale kulemba mawu ouziridwa onena za dziko lapansi kukhala litalengedwera kukhalamo anthu ndi onena za olungama kukhalamo kosatha. (Salmo 37:9-11; Miyambo 2:21, 22; Yesaya 45:18) Komabe, kodi ndimotani mmene alambiri owona amenewo akapezera chipulumutso choterocho ngati anafa? Mwa kubwezeretsedweranso kwawo ku moyo padziko lapansi ndi Mulungu. Mwachitsanzo, Yobu, analongosola chiyembekezo chakuti akakumbukiridwa ndi kubwezeretseredwanso ku moyo. (Yobu 14:13-15; Danieli 12:13) Momvekera, mtundu wina wa chipulumutso ndiwo moyo wosatha padziko lapansi.—Mateyu 11:11.
17. Kodi Baibulo limasonyeza kuti ena angapeze chipulumutso chiti chosiyana?
17 Baibulo limalankhulanso za chipulumutso cha moyo kumwamba, kumene Yesu Kristu adapita pambuyo pa kuukitsidwa kwake. “Akhala padzanja lamanja la Mulungu, ataloŵa m’mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu zomgonjera.” (1 Petro 3:18, 22; Aefeso 1:20-22; Ahebri 9:24) Koma Yesu sadzakhala munthu yekha wotengeredwa kumwamba. Mulungu watsimikiza kuti adzatenganso kuchokera padziko lapansi chiŵerengero chochepera cha ena. Yesu anauza atumwi kuti: “M’nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. . . . Ndipita kukukonzerani inu malo. Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa ine ndekha; kuti kumene kuli ineko, mukakhale inunso.”—Yohane 14:2, 3.
18. Kodi tiri ndi chifukwa chotani tsopano chosumikikira maganizo athu pa chipulumutso cha moyo wakumwamba?
18 Chipulumutso cha ku moyo wakumwamba m’chigwirizano ndi Yesu kwenikweni chiri chachikulu kwambiri koposa chipulumutso chokhala ndi polekezera chimene chinachokera m’Paskha woyambirira. (2 Timoteo 2:10) Panali pa madzulo a Seder yalamulo yomalizira, kapena chakudya cha Paskha, pamene Yesu anayambitsa phwando latsopano la otsatira ake, limene linasumika pachipulumutso cha moyo wakumwamba. Iye anauza atumwi kuti: “Chitani ichi chikumbukiro changa.” (Luka 22:19) Tisanalingalire mmene Akritu ayenera kusungira phwando limeneli, tiyeni tilingalire za pamene tingatero.
“Nthaŵi Yoikidwiratu”
19. Kodi nchifukwa ninji kuli kwanzeru kugwirizanitsa Paskha ndi Mgonero wa Ambuye?
19 Yesu adaati: “Ndinalakalaka ndithu kudya Paskha uwu pamodzi ndi inu, ndisanayambe kusautsidwa.” (Luka 22:15) Pambuyo pake anasanja Mgonero wa Ambuye, umene atsatiri ake akafunikira kusunga monga chikumbutso cha imfa yake. (Luka 22:19, 20) Paskha idachitidwa kamodzi pachaka. Chotero, kuli kwanzeru kuti Mgonero wa Ambuye usungidwe chaka ndi chaka. Liti? Moyenerera, m’dzinja la nthaŵi ya Paskha. Zimenezo zikutanthauza kukhala pamene Nisan 14 (kalenda Yachiyuda) inakwanirapo, mmalo mwa kumamatira nthaŵi zonse ku Lachisanu popeza kuti limenelo linali tsiku lamlungu palimene Yesu anafera.
20. Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova ziri zokondweretsedwa ndi Nisan 14?
20 Chotero Nisan 14 likakhala deti limene Paulo anali kulingalira pamene adalemba kuti: “Pakuti nthawi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera chikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza iye.” (1 Akorinto 11:26) Kwazaka mazana aŵiri zotsatira, Akristu ambiri anaumirira ku Nisan 14, akumadziwika kukhala Akwatodesimani, m’Chilatini lotanthauza “14.” M’Clintock ndi Strong akusimba kuti: “Matchalitchi a ku Asia Minor anachitira phwando imfa ya Ambuye patsiku loyenererana ndi la 14 la mwezi wa Nisan, patsiku limene, mogwirizana ndi Tchalitchi chakalekale, kupachikidwa kunachitika.” Lerolino, Mboni za Yehova zimachita Mgonero wa Ambuye chaka ndi chaka patsiku loyenererana ndi Nisan 14. Komabe, ena awona kuti, limeneli lingasiyane ndi deti limene Ayuda amasunga Paskha yawo. Chifukwa ninji?
21. Kodi mwana wankhosa wa Paskha ankafunikira kuperekedwa nsembe liti, koma kodi nchiyani chimene Ayuda amachita lerolino?
21 Tsiku la Ayuda limayambira pa kuloŵa kwadzuŵa (pafupifupi ora lachisanu ndi chimodzi madzulo) kufikira kulowa kwa dzuŵa kotsatira. Mulungu analamulira kuti mwana wankhosa wa Paskha aphedwe pa Nisan 14, “pakati pa madzulo aŵiri.” (Eksodo 12:6) Kodi pamenepo pakakhala liti? Ayuda amakono amamamatira lingaliro la arabi lakuti mwana wankhosa anafunikira kuphedwa pafupi ndi mapeto a Nisan 14, pakati pa nthaŵi pamene dzuŵa linayamba kupendeka (chifupifupi ora lachitatu) ndi kulowa kwadzuŵa kwenikweniko. Monga chotulukapo, iwo amasunga Seder yawo pambuyo pa kuloŵa kwadzuŵa, pamene Nisan 15 yayamba—Marko 1:32.
22. Kodi nchifukwa chiti chimene deti la Chikumbutso lingasiyanirane ndi deti pamene Ayuda achita Paskha wawo? (Marko 14:17; Yohane 13:30)
22 Komabe, tiri ndi chifukwa chabwino cha kumvetsetsera kalongosoledweko mosiyana. Deuteronomo 16:6 idauza Aisrayeli momvekera bwino “kupha nsembe ya paskha, madzulo, poloŵa dzuŵa.” (Kutembenuza kwa Tanakh Wachiyuda) Ichi chimasonyeza kuti “pakati pa madzulo awiri” panali kusonya kunyengo yachizirezire, yoyambira pakulowa kwadzuwa (komwe kunayamba pa Nisan 14) kufika pamdima weniweni. Ayuda Achikaraite akalerob anazindikira mwanjira imeneyi, monga momwe amachitira Asamariyac mpaka lerolino. Kuvomereza kwathu kuti mwana wankhosa wa Paskha anaperekedwa nsembe ndi kudyedwa “panthawi yake yoikika” pa Nisan 14, osati pa Nisan 15, kuli chifukwa china chimene deti lathu la Chikumbutso nthawi zina imasiyanirana ndi deti la Ayuda.—Numeri 9:2-5.
23. Kodi nchifukwa ninji miyezi imawonjezeredwa kukalenda ya Ahebri, ndipo kodi chimachitidwa motani ndi Ayuda amakono?
23 Chifukwa china chimene deti lathu lingasiyanirane ndi la Ayuda nchakuti iwo amagwiritsira ntchito kalenda yokonzedweratu, dongosolo limene silinakhaleko kufikira m’zaka za zana lachinayi C.E. Mogwiritsira ntchito dongosololi, iwo angakhazikitse madeti a Nisani 1 kapena a mapwando zaka makumi angapo kapena zaka mazana ambiri pasadakhale. Ndiponso, kalenda yakale ya mwezi weniweni inafunikira kuwonjezeredwa kwa mwezi wa 13 panthaŵi ndi nthaŵi kotero kuti kalendayo igwirizane ndi nyengo. Kalenda yamakono ya Ayuda imawonjezera mwezi umenewu panyengo zokhazikitsidwiratu; pambuyo pa zaka 19 zirizonse, uwo umawonjezeredwa kuzaka za 3, 6, 8, 11, 14, 17, ndi 19.
24, 25. M’nthawi ya Yesu, kodi ndimotani mmene miyezi inali kulinganizidwira ndi kutsimikiziridwa kwa miyezi yowonjezereka? (b) Kodi ndimotani mmene deti la Mgonero wa Ambuye limakhazikitsidwira ndi Mboni za Yehova?
24 Komabe, Emil Schürer akunena kuti “panthaŵi ya Yesu [Ayuda] anali asanakhale ndi kalenda yokonzedweratu, koma pamaziko a kungowona chabe, iwo anayamba mwezi uliwonse watsopano atawona mwezi watsopano utakhala, ndipo mofananamo pamaziko a kungowona” ankawonjezera mwezi monga momwe anawonera kufunika. “Ngati . . . unawonekera chakumapeto kwa chaka Paskha ameneyo akakhalako m’nyengo ya equinox isanakhale [chifupifupi March 21] kuwonjezeredwa kwa mwezi Nisan isadakhale kunkalamulidwa.” (The History of the Jewish People in the Age of Jesus Christ, Voliyamu 1) Chotero mwezi wowonjezeredwawo umaphatikizidwa mwachibadwa, osangowonjezera mododometsa.
25 Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova limakhazikitsa deti la Mgonero wa Ambuye mogwirizana ndi njira yakale. Nisan 1 amatsimikiziridwa pamene mwezi watsopano pafupi ndi equinox ungakhoze kuwonedwa pakuloŵa kwadzuŵa m’Yerusalemu. Kuwerenga masiku 14 kuyambira pamenepo kumafikitsa munthuwe ku Nisan 14, imene kaŵirikaŵiri iri yogwirizana ndi tsiku pamene mwezi uli wathunthu. (Wonani The Watchtower ya June 15, 1977, tsamba 383-4.) Pamaziko a njira ya m’Baibulo imeneyi, Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse zalangizidwa kuti phwando la Chikumbutso chaka chino lidzakhalako pambuyo pa kulowa kwadzuwa pa April 10.
26. Kodi ndimbali zowonjezereka ziti za Mgonero wa Ambuye zimene zimafunikira kulingalira kwathu?
26 Deti limeneli nloyenerana ndi Nisan 14, panthawi imene Yesu anachita Paskha yalamulo yomalizira. Komabe, kuchita phwando la Chikumbutso kumasumika maganizo pa chipulumutso kuposa ndi zimene phwando la Ayuda la kukumbukira Seder limachita. Tonsefe tifunikira kuzindikira chimene chimachitika pa Mgonero wa Ambuye, chimene umatanthauza, ndi mmene chipulumutso chathu chikuloŵetsedweramo.
[Mawu a M’munsi]
a Wonani Nsanja ya Olonda ya August 15, 1980, masamba 9-28.
b M’Clintock ndi Strong amawalongosola iwo kukhala “amodzi a mipatuko yakale kwambiri ndi yotchuka kwenikweni ya sunagoge wa Ayuda, amene chizindikiro chawo chowasiyanitsa ndicho kumamatira kwawo gwagwagwa kumawu onse olembedwa achilamulo.”
c “Iwo amapha nyama madzulo . . . Pakati pausiku banja lirilonse limadya nyamayo . . . ndiyeno kutentha nyama yotsalayo ndi mafupa ake kusanache . . . Akatswiri ena apereka lingaliro lakuti chipembedzo cha Asamariya chingafanane kwenikweni ndi chipembedzo chabaibulo Chiyuda cha arabi chisanachisinthe.”—The Origins of the Seder.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji Paskha iri yogwirizanitsidwa moyenerera ndi chipulumutso?
◻ Kodi ndimotani mmene nsembe ya Yesu ingakwaniritsire zambiri kuposa mmene anachitira mwanawankhosa wa Paskha?
◻ Kodi nchipulumutso chotani chimene chimapezeka kupyolera mwa Yesu?
◻ Kodi ndimotani mmene Mboni za Yehova zimakhazikitsira nthawi yoyenerera ya Mgonero wa Ambuye?