Mphotho ya Yobu—Magwero a Chiyembekezo
“Yehova anadalitsa chitsiriziro cha Yobu koposa chiyambi chake.”—YOBU 42:12.
1. Kodi nchiyani chimene Yehova amachitira anthu ake, ngakhale pamene mayesero awafooketsa kwambiri?
YEHOVA “ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.” (Ahebri 11:6) Iye amasonkhezeranso anthu ake odzipereka kuchitira umboni molimba mtima, ngakhale ngati mayesero awapangitsa kukhala ofooka monga akufa. (Yobu 26:5; Chivumbulutso 11:3, 7, 11) Zimenezo zinakhaladi choncho kwa Yobu wovutikayo. Ngakhale kuti ananamiziridwa ndi otonthoza atatu onyengawo, iye sanatontholetsedwe ndi kuwopa anthu. M’malo mwake, iye anapereka umboni molimba mtima.
2. Ngakhale kuti zakumana ndi chizunzo ndi mavuto, kodi ndimotani mmene Mboni za Yehova zapulumukira m’mayesero awo?
2 Mboni za Yehova zambiri zamakono zakumana ndi chizunzo chachikulu ndi mavuto otero kwakuti zatsala nenene kufa. (2 Akorinto 11:23) Komabe, monga Yobu, iwo asonyeza chikondi kwa Mulungu ndipo achita chilungamo. (Ezekieli 14:14, 20) Iwo apyolanso m’mayesero awo ali otsimikiza kukondweretsa Yehova, olimbitsidwa kupereka umboni molimba mtima, ndi odzazidwa ndi chiyembekezo chenicheni.
Yobu Apereka Umboni Molimba Mtima
3. Kodi Yobu anapereka umboni wotani m’kulankhula kwake komaliza?
3 M’kulankhula kwake komaliza, Yobu anapereka umboni wokulirapodi kuposa umene anali atapereka poyamba. Iye anatontholetseratu omtonthoza ake onyengawo. Mowanyodola kwambiri, iye anati: “Wamthandiza bwanji wopanda mphamvu.” (Yobu 26:2) Yobu anatamanda Yehova, amene mphamvu yake imachititsa dziko lathu lapansi lobulungikali kulenjekeka pachabe mumlengalenga nayala mitambo yokhala ndi madzi pamwamba pa dziko lapansi. (Yobu 26:7-9) Komabe, Yobu ananena kuti zozizwitsa zimenezo ‘zangokhala malekezero a njira za Yehova.’—Yobu 26:14.
4. Kodi nchiyani chimene Yobu ananena ponena za umphumphu, ndipo kodi nchifukwa ninji ananena motero?
4 Pokhala wotsimikiza za kupanda liwongo kwake, Yobu analengeza kuti: “Mpaka kufa ine sinditaya [umphumphu, NW] wanga.” (Yobu 27:5) Mosiyana ndi zinenezo zonamazo zimene anapatsidwa, iye sanali atachita kanthu kalikonse kamene kanayenerera zimene zinamgwerazo. Yobu anadziŵa kuti Yehova samamvetsera mapemphero a ampatuko koma adzafupa osunga umphumphu. Zimenezi zingatikumbutse bwino lomwe kuti posachedwa mkuntho wa Armagedo udzakantha oipa kuwachotsa pamalo awo aulamuliro, ndipo sadzapulumuka padzanja la Mulungu losalekerera. Kufikira nthaŵiyo, anthu a Yehova adzayenda mu umphumphu wawo.—Yobu 27:11-23.
5. Kodi ndimotani mmene Yobu anafotokozera nzeru yoona?
5 Tangoyerekezerani atatu odziŵa zaumunthu kwambiriwo akumamvetsera pamene Yobu anasonyeza kuti munthu wagwiritsira ntchito maluso ake kupeza golidi, siliva, ndi chuma china m’dziko lapansi, ndi m’nyanja. “Mtengo wake wa nzeru uposa wa korali wofiira,” iye anatero. (Yobu 28:18) Otonthoza Yobu onyengawo sakanatha kugula nzeru yoona. Magwero ake ndiwo Mlengi wa mphepo, mvula, mphezi, ndi bingu. Ndithudi, “kuwopa [kwaulemu] Ambuye ndiko nzeru; ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha.”—Yobu 28:28.
6. Kodi nchifukwa ninji Yobu analankhula za moyo wake woyamba?
6 Mosasamala kanthu za kuvutika kwake, Yobu sanaleke kutumikira Yehova. M’malo mwa kuchoka kwa Wam’mwambamwambayo, mwamuna waumphumphu ameneyu anakhumba “uphungu [wake wakale] wa Mulungu.” (Yobu 29:4) Yobu sanali kudzitamandira pamene anasimba za mmene ‘anapulumutsira wozunzika, kudziveka chilungamo, ndi mmene analili atate wa waumphaŵi.’ (Yobu 29:12-16) M’malo mwake, iye analikutchula zenizeni za moyo wake monga mtumiki wokhulupirika wa Yehova. Kodi mwapanga mbiri yabwino yotero? Ndithudi, Yobu anali kusonyezanso poyera chinyengo cha zinenezo zoperekedwa ndi achinyengo atatu amaonekedwe opembedza.
7. Kodi Yobu anali munthu wotani?
7 Yobu anasekedwa ndi osafikana msinkhu wake ‘amene atate awo sakanawaika pamodzi ndi agalu olinda nkhosa zake.’ Ananyansidwa naye namthira malovu. Ngakhale kuti anazunzika kwambiri motero, Yobu sanasonyezedwe chifundo. (Yobu 30:1, 10, 30) Komabe, chifukwa chakuti anali wodzipereka kotheratu kwa Yehova, iye anali ndi chikumbumtima choyera ndipo anatha kunena kuti: “Andiyese ndi muyeso wolingana, kuti Mulungu adziŵe ungwiro wanga.” (Yobu 31:6) Yobu sanali wachigololo kapena wachiwembu, ndipo sanalephere kuthandiza osoŵa. Ngakhale kuti anali wolemera, iye sanadalire chuma chakuthupi. Ndiponso, Yobu sanaloŵe m’kupembedza mafano mwa kulambira zinthu zopanda moyo, zonga mwezi. (Yobu 31:26-28) Pokhulupirira Mulungu, iye anapereka chitsanzo chabwino monga wosunga umphumphu. Mosasamala kanthu za mavuto ake onse ndi kukhalapo kwa omtonthoza ake onyengawo, Yobu anadzitetezera mwaluso ndi kupereka umboni wabwino kwambiri. Mawu ake pokhala atatha, anayembekezera Mulungu monga Woweruza ndi Wofupa wake.—Yobu 31:35-40.
Elihu Alankhula
8. Kodi Elihu anali yani, ndipo kodi anasonyeza motani ulemu ndi kulimba mtima komwe?
8 Pafupipo panali mnyamata wina Elihu, mbadwa ya Nahori mwana wa Buzi ndipo motero wachibale wa Abrahamu bwenzi la Yehova. (Yesaya 41:8) Elihu anasonyeza ulemu kwa amuna achikulirewo mwa kumvetsera ku mbali zonse za kukambitsiranako. Komabe, iye analankhula molimba mtima ponena nkhani zimene iwowo analakwa. Mwachitsanzo, iye adapsa mtima ndi Yobu pakuti “anadziyesera yekha wolungama, wosati Mulungu.” Elihu anapsa mtima makamaka ndi otonthoza onyengawo. Mawu awo anamvekera monga ngati kuti anali kutamanda Mulungu komabe kwenikweni iwo anali kumtonza mwa kukhala kumbali ya Satana pa mkanganowo. Pokhala ‘wodzazidwa ndi mawu’ ndi wosonkhezeredwa ndi mzimu woyera, Elihu anali mboni yosakondera ya Yehova.—Yobu 32:2, 18, 21.
9. Kodi ndimotani mmene Elihu anaperekera lingaliro la kuchira kwa Yobu?
9 Yobu anakhala ndi nkhaŵa yaikulu kudzichirikiza m’malo mochirikiza Mulungu. Kwenikweni, iye anatsutsana ndi Mulungu. Komabe, pamene moyo wa Yobu unayandikira imfa, panali chiyembekezo cha kuchira. Motani? Eya, Elihu anasonkhezeredwa kunena kuti Yehova anachitira chifundo Yobu ndi uthenga uwu: “Mlanditse, angatsikire kumanda, ndampezera dipo. Mnofu wake udzakhala se, woposa wa mwana; adzabwerera ku masiku a ubwana wake.”—Yobu 33:24, 25.
10. Kodi Yobu anafunikira kuyesedwa kufikira pati, koma kodi tingakhale otsimikizira za chiyani polingalira za 1 Akorinto 10:13?
10 Elihu anawongolera Yobu pa kunena kuti munthu sapindula kanthu ndi kukondwera mwa Mulungu mwa kusunga umphumphu. Elihu anati: “Nkutali ndi Mulungu kuchita choipa, ndi Wamphamvuyonse kuchita chosalungama. Pakuti ambwezera munthu monga mwa ntchito yake.” Yobu anachita mwansontho mwa kugogomezera kulungama kwa iye mwini, komatu anachita zimenezo popanda chidziŵitso chokwanira ndi nzeru. Elihu anawonjezera kuti: “Mwenzi nayesedwe Yobu kufikira kutha, chifukwa cha kuyankha kwake monga anthu amphulupulu.” (Yobu 34:10, 11, 35, 36) Mofananamo, chikhulupiriro ndi umphumphu wathu zingatsimikiziridwe mokwanira kokha ngati ‘tiyesedwa kufikira kutha’ mwanjira ina yake. Komabe, Atate wathu wakumwamba wachikondiyo sadzatilola kuyesedwa kuposa kumene tingapirire.—1 Akorinto 10:13.
11. Pamene tiyesedwa momvetsa ululu, kodi tiyenera kukumbukira chiyani?
11 Pamene Elihu anapitiriza kulankhula, kachiŵirinso anasonyeza kuti Yobu anali kugogomezera kwambiri chilungamo cha iye mwini. Chigogomezerocho chiyenera kulunjikitsidwa pa Mpangi wathu Wamkulu. (Yobu 35:2, 6, 10) Mulungu “sasunga woipa akhale ndi moyo, koma awaninkha ozunzika zowayenera iwo,” Elihu anatero. (Yobu 36:6) Palibe munthu amene angapezere chifukwa njira ya Mulungu ndi kunena kuti wachita chosalungama. Iye ali wokwezeka kwambiri kuposa mmene tidziŵira, ndipo zaka zake nzosasanthulika. (Yobu 36:22-26) Pamene tiyesedwa momvetsa ululu, kumbukirani kuti Mulungu wathu wamuyaya ngwolungama ndipo adzatifupa chifukwa cha ntchito zathu zokhulupirika zomtamanda.
12. Kodi nchiyani chimene mawu omaliza a Elihu amasonyeza ponena za kupereka chiweruzo kwa Mulungu pa oipa?
12 Elihu akali chilankhulire, kavumvulu anali kupangika. Pamene anayandikira, mtima wake unayamba kunjenjemera. Iye ananena za zinthu zazikulu zopangidwa ndi Yehova ndipo anati: “Tamverani ichi, Yobu, Taimani, mulingirire zodabwiza za Mulungu.” Mofanana ndi Yobu, ife tifunikira kulingalira ntchito zodabwiza za Mulungu ndi ulemerero wochititsa mantha. “Kunena za Wamphamvuyonse, sitingamsanthule,” Elihu anatero. “Ndiye wa mphamvu yoposa; koma mwa chiweruzo ndi chilungamo chochuluka [sadzazichepetsa, NW]. M’mwemo anthu amuwopa.” (Yobu 37:1, 14, 23, 24) Mawu omaliza a Elihu amatikumbutsa ife kuti pamene Mulungu apereka chiweruzo pa oipa posachedwapa, sadzachepetsa chiweruzo ndi chilungamo ndipo adzasunga awo amene amamuwopa monga olambira ake aulemu. Ndi mwaŵi wotani nanga kukhala pakati pa osunga umphumphu otero amene amavomereza Yehova monga Mfumu Yachilengedwe Chonse! Pirirani monga momwe anachitira Yobu, ndipo musalole konse Mdyerekezi kukuchotsani m’malo anu odala pakati pa makamu achimwemwe ameneŵa.
Yehova Ayankha Yobu
13, 14. (a) Kodi Yehova anayamba kufunsa Yobu ponena za chiyani? (b) Kodi ndi mfundo zotani zimene zingaphunziridwe m’mafunso ena amene Mulungu anafunsa Yobu?
13 Ha, Yobu ayenera kukhala atadabwa chotani nanga pamene Yehova analankhula naye m’kavumvulu! Kavumvulu ameneyo anali wochititsidwa ndi Mulungu, mosiyana ndi mphepo yaikulu imene Satana anagwiritsira ntchito kugwetsera nyumba ndi kupha ana a Yobu. Yobu anasoŵa chonena pamene Mulungu anafunsa kuti: “Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi? . . . Kapena anaika ndani mwala wake wa pangondya, muja nyenyezi za mmaŵa zinaimba limodzi mokondwera, ndi ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe?” (Yobu 38:4, 6, 7) Yehova anafunsa Yobu mafunso ambiri onena za nyanja, chovala chake cha mtambo, mbanda kucha, zipata za imfa, kuunika ndi mdima, magulu anyenyezi. Yobu sanathe kunena kanthu kalikonse pamene anafunsidwa kuti: “Kodi udziŵa malemba a kuthambo?”—Yobu 38:33.
14 Mafunso ena anasonyeza kuti munthu asanalengedwe ndi kupatsidwa ulamuliro pa nsomba, mbalame, nyama, ndi zokwaŵa, Mulungu anali kuzisamalira—popanda thandizo lililonse kapena uphungu wa munthu. Mafunso enanso a Yehova anatchula za zolengedwa zonga ngati njati, nthiwatiwa, ndi kavalo. Yobu anafunsidwa kuti: “Kodi chiombankhanga chikwera m’mwamba pochilamulira iwe, nichimanga chisanja chake m’mwamba?” (Yobu 39:27) Ndithudi ayi! Tangoganizirani mchitidwe wa Yobu pamene Mulungu anamfunsa kuti: “Kodi wodzudzulayo atsutsane ndi Wamphamvuyonse?” Mposadabwitsa kuti Yobu anati: “Taonani, ndakhululuka ine, ndidzakubwezerani mawu otani? Ndigwira pakamwa.” (Yobu 40:2, 4) Popeza kuti nthaŵi zonse Yehova ali wolondola, ngati tiyesedwa kutsutsana naye, tiyenera ‘kugwira pakamwa pathu.’ Mafunso a Mulungu anasonyezanso mwamphamvu kupambana kwake, ulemerero, ndi nyonga, monga momwe zasonyezedwera m’chilengedwe.
Behemoti ndi Livyatanu
15. Kodi buku la Yobu limadziŵikitsa mvuu ndi dzina liti m’malembo oyambirira, ndipo kodi nchiyani chimene chili ina ya mikhalidwe yake?
15 Kenako Yehova anatchula za mvuu, yotchedwa Behemoti m’malembo oyambirira. (Yobu 40:15-24) Pokhala yapadera chifukwa cha ukulu wake, kulemera kwake kwakukulu, ndi chikopa chake cholimba, nyama yokhalira moyo pa zomera imeneyi ‘imadya udzu.’ Mphamvu ndi nyonga yake zili mchuuno ndi m’mitsempha ya m’mimba mwake. Mafupa a miyendo yake ali olimba ngati “misiwe ya mkuwa.” Behemoti sichita mantha ndi liyambwe la madzi koma imasambira mosavuta kumka kumene likuchokera.
16. (a) Kodi buku la Yobu limadziŵikitsa ng’ona ndi dzina liti m’malembo oyambirira, ndipo kodi umboni wina wa zimenezi ndi wotani? (b) Kodi mphamvu ya Behemoti ndi Livyatanu ingasonyezenji ponena za kukwaniritsa magawo mu utumiki wa Yehova?
16 Mulungu anafunsanso Yobu kuti: “Kodi ukhoza kukoka ng’ona ndi mbedza? Kapena kukanikiza kalandira wake ndi chingwe?” Ng’ona ikutchedwa Livyatanu m’malembo oyambirira. (Yobu 41:1-34) Singapangane za mtendere ndi munthu aliyense, ndipo palibe munthu aliyense wanzeru amene angakhale wolimba mtima kuputa nyama yokwaŵa imeneyi. Mivi siithaŵitsa, ndipo “iseka kuthikuza kwake kwa nthungo.” Livyatanu yolusa imachititsa nthubwinthubwi pozama ngati nkhali ya mafuta. Chenicheni chakuti Livyatanu ndi Behemoti zinali zamphamvu kwambiri kuposa Yobu zinamthandiza kudzichepetsa. Nafenso tiyenera kuvomereza modzichepetsa kuti sitili amphamvu mwa ife tokha. Timafunikira nzeru ndi nyonga zoperekedwa ndi Mulungu kuti tipeŵe kulumidwa ndi Satana, Njokayo, ndi kukwaniritsa magawo athu mu utumiki wa Yehova.—Afilipi 4:13; Chivumbulutso 12:9.
17. (a) Kodi Yobu ‘anapenya Mulungu’ motani? (b) Kodi nchiyani chimene chinasonyezedwa ndi mafunso amene Yobu anali wosakhoza kuyankha, ndipo kodi zimenezi zingatithandize motani?
17 Atachepetsedwa kotheratu, Yobu anavomereza lingaliro lake lolakwa ndipo anavomereza kuti anali atalankhula mosadziŵa. Komabe, iye anali atasonyeza chikhulupiriro chakuti ‘akapenya Mulungu.’ (Yobu 19:25-27) Kodi zimenezo zikanachitika motani, popeza kuti palibe munthu aliyense angaone Yehova ndi kukhalabe ndi moyo? (Eksodo 33:20) Kwenikweni, Yobu anaona zisonyezero za mphamvu yaumulungu, anamva liwu la Mulungu, ndipo maso ake amtima anatsegulidwa kuti aone choonadi chonena za Yehova. Chifukwa chake Yobu ‘anadzinyansa, ndi kulapa m’fumbi ndi mapulusa.’ (Yobu 42:1-6) Mafunso ambiri amene iyeyo anali wosakhoza kuyankha anasonyeza kupambana kwa Mulungu ndipo anasonyeza kuchepetsetsa kwa munthu, ngakhale munthu wodzipereka kwa Yehova wonga Yobu. Zimenezi zimatithandiza kuona kuti zofuna zathu siziyenera kuikidwa pamwamba pa kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova ndi kuchirikizidwa kwa ulamuliro wake. (Mateyu 6:9, 10) Nkhaŵa yathu yaikulu iyenera kukhala ya kusunga umphumphu kwa Yehova ndi kulemekeza dzina lake.
18. Kodi nchiyani chimene otonthoza Yobu onyenga anafunikira kuchita?
18 Komabe, bwanji nanga za otonthoza onyenga odzilungamitsawo? Moyenerera Yehova akanapha Elifazi, Bilidadi, ndi Zofari chifukwa cha kusanena zoona ponena za iye, monga momwe Yobu anachitira. “Mudzitengere ng’ombe zisanu ndi ziŵiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri, mumuke kwa mtumiki wanga Yobu,” Mulungu anatero, “mudzifukizire nokha nsembe yopsereza; ndi mtumiki wanga Yobu adzapempherera inu.” Atatuwo anafunikira kudzichepetsa kuti achite motero. Yobu wosunga umphumphuyo anafunikira kuwapempherera, ndipo Yehova anaona pemphero lake kukhala lovomerezeka. (Yobu 42:7-9) Komano bwanji za mkazi wa Yobu, amene anamlimbikitsa kuchitira mwano Mulungu ndi kufa? Kukuonekera kuti iyeyo anayanjanitsidwa naye mwa chifundo cha Mulungu.
Mphotho Zolonjezedwa Zimatipatsa Chiyembekezo
19. Mogwirizana ndi nkhani ya Yobu, kodi ndimotani mmene Yehova anasonyezera kupambana Kwake pa Mdyerekezi?
19 Yobu atangoleka kuvutika maganizo ndi mavuto ake anayambanso kuchita utumiki wa Mulungu, Yehova anamsinthira mkhalidwewo. Yobu atapempherera atatuwo, Mulungu ‘anachotsa ukapolo wake’ ndi kumpatsa ‘zake zonse mpaka kuziwirikiza.’ Yehova anasonyeza kupambana Kwake pa Mdyerekezi mwa kubweza dzanja lopereka nthenda la Satana ndi kuchiritsa Yobu mozizwitsa. Mulungu anathamangitsanso makamu a ziŵanda ndi kuwatsekereza akumachingiranso Yobu ndi tchinga Lake la angelo.—Yobu 42:10; Salmo 34:7.
20. Kodi Yehova anafupa ndi kudalitsa Yobu m’njira zotani?
20 Abale ake a Yobu, alongo ake, ndi odziŵana naye anafika kudzadya naye, kumchitira chisoni, ndi kumtonthoza pa tsoka limene Yehova analola kuchitika pa iye. Aliyense wa iwo anapatsa Yobu ndalama ndi mphete ya golidi. Yehova anadalitsa mapeto a Yobu kuposa chiyambi chake, kotero kuti anafikira kukhala ndi nkhosa 14,000, ngamila 6,000, ng’ombe zamagoli 1,000 ndi abulu aakazi 1,000. Yobu anakhalanso ndi ana aamuna asanu ndi aŵiri ndi ana aakazi atatu, chiŵerengero chimodzimodzicho chimene anali nacho poyamba. Ana ake aakaziwo—Yemima, Keziya, ndi Kerenihapuki—anali akazi okongola koposa m’dzikolo, ndipo Yobu anawapatsa choloŵa pakati pa alongo awo. (Yobu 42:11-15) Ndiponso, Yobu anakhala ndi moyo zaka zina 140 naona mibadwo inayi ya mbadwa zake. Cholembedwacho chimamaliza ndi kuti: “Namwalira Yobu, wokalamba ndi wa masiku ochuluka.” (Yobu 42:16, 17) Kutalikitsidwa kwa moyo wake kunali ntchito yozizwitsa ya Yehova Mulungu.
21. Kodi timathandizidwa motani ndi nkhani ya m’Malemba yonena za Yobu, ndipo kodi tiyenera kutsimikiza kuchitanji?
21 Cholembedwa cha m’Malemba chimenechi chonena za Yobu chimatipangitsa ife kuzindikira kwambiri za machenjera a Satana ndi kutithandiza kuona mmene ulamuliro wachilengedwe chonse umayambukirira umphumphu waumunthu. Monga Yobu, onse amene amakonda Mulungu adzayesedwa. Koma ife tingapirire monga momwe anachitira Yobu. Iye anatuluka m’mayesero ake ali ndi chikhulupiriro ndi chiyembekezo, ndipo mfupo zake zinali zambiri. Monga atumiki a Yehova lerolino, tili ndi chikhulupiriro ndi chiyembekezo choona. Ndipo ndi chiyembekezo chachikulu chotani nanga chimene Wopereka Mphotho Wamkuluyo watiikira pamaso pa aliyense wa ife! Kukumbukira mfupo yakumwamba kudzathandiza otsalira kutumikira Mulungu mokhulupirika m’moyo wawo wonse padziko lapansi. Ambiri amene ali ndi ziyembekezo za padziko lapansi sadzafa konse, koma amene adzatero adzafupidwa ndi chiukiriro m’Paradaiso padziko lapansi, limodzi ndi Yobu mwiniyo. Pokhala ndi chiyembekezo chenicheni chotero mu mtima ndi m’maganizo, onse okonda Mulungu atsimikiziretu Satana kukhala wonama mwa kuima mochirimika kumbali ya Yehova monga osunga umphumphu ndi ochirikiza okhulupirika a ulamuliro wake wachilengedwe chonse.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi mfundo zina zonenedwa ndi Yobu m’kuyankha kwake komaliza omtonthoza ake onyenga nziti?
◻ Kodi Elihu anasonyeza motani kuti anali mboni yosakondera ya Yehova?
◻ Kodi Mulungu anafunsa Yobu mafunso ena otani, ndipo kodi iwo anali ndi chiyambukiro chotani?
◻ Kodi mwapindula motani ndi nkhani ya m’Malemba yonena za Yobu?
[Zithunzi patsamba 18]
Mawu a Yehova ponena za Behemoti ndi Livyatanu anathandiza Yobu kudzichepetsa