Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 12/8 tsamba 12-14
  • Kodi Kukhala Bwenzi la Mulungu Kudzandithandiza?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kukhala Bwenzi la Mulungu Kudzandithandiza?
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ubwenzi ndi Mulungu
  • ‘Wodalirika Wanga Kuyambira pa Ubwana Wanga’
  • Mulungu Amatithandiza Kulondola Njira Yoyenera
  • “Thanthwe la Mtima Wanga”
  • Yehova Akhoza Kukhala Mnzanu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Nchifukwa Ninji Sindimakhala ndi Mabwenzi?
    Galamukani!—1996
  • N’chifukwa Chiyani Mnzanga Wayamba Kudana Nane?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Kodi Bwenzi Langa Lapamtima Linasamukiranji?
    Galamukani!—1997
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 12/8 tsamba 12-14

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Kukhala Bwenzi la Mulungu Kudzandithandiza?

ACHICHEPERE ambiri lerolino amakulira pansi pa zididikizo zimene kwa mbadwo wapitawo zikanakhala zodabwitsa kwambiri. Amene anachita kufufuza kwa achichepere 160,000 m’dziko lina anafotokoza kuti: “Achichepere akutiuza kuti zimene zimachititsa zovuta zawo zambiri ndi zididikizo zimene amaona kuti sangathe kulimbana nazo; kulefulidwa ndiponso kumva chisoni zimene zimathetsa chidaliro chawo; ndi makolo amene samaona zovuta zawo.” Inunso mungalingalire kuti ena samatha kudziŵa mmene moyo ungakhalire wopweteka nthaŵi zina kwa wachichepere.

Komabe, mungakhale ndi bwenzi lapamtima limene mungatembenukireko kaamba ka chilimbikitso, ndipo zimenezi zingakupatseni mpumulo pang’ono. Koma kodi si zoona kuti pali mavuto opweteka amene muyenera kuyang’anizana nawo panokha? Nzoonadi kuti nthaŵi zina kokha ‘mtima wanu udziŵa kuŵaŵa kwanu.’ (Miyambo 14:10) Koma pali Wina amene amakumvetsetsani kotheratu, ndipo amafuna kukhala bwenzi lanu. Achichepere ambiri apeza kuti ubwenzi wake uli thandizo lalikulu ngakhale panthaŵi zovuta koposa.

Ubwenzi ndi Mulungu

Wachichepere wina anafunsidwa chifukwa chachikulu chimene anayamikirira Yehova Mulungu. Yankho lake: “Kuti timdziŵe ndi kukhala mabwenzi ake apamtima.” Inde, nkotheka kuloŵa muubwenzi wabwino koposa m’chilengedwe chonse! Wamasalmo analemba kuti: “Chinsinsi cha Yehova [“Ubwenzi wapamtima ndi Yehova,” NW] chiri kwa iwo akumuwopa iye.”—Salmo 25:14.

“Ubwenzi wapamtima ndi Yehova”—ndi mwaŵi wamtengo wapatali chotani nanga! Liwu loyambilira Lachihebri limapereka lingaliro la makambitsirano achinsinsi, osabisa kanthu kwa wina wake amene ali bwenzi lapadera. Motero, uli ubwenzi wathithithi wozikidwa pa chikondi, ubwenzi wapamtima wochokera pa kudalirana. Monga bwenzi la Mulungu, mudzaona kuti kufunika kwanu monga munthu kumaŵerengeredwa ndi ameneyu amene amakumvetsetsanidi. Koma kodi mapindu a ubwenzi umenewu ngotani?

‘Wodalirika Wanga Kuyambira pa Ubwana Wanga’

Mosasamala kanthu kuti achichepere ambiri kunja amaoneka kukhala otsimikiza, iwo alibe chidaliro mumtima mwawo. “Ndimatchula malingaliro anga ndipo ena amabweretsa awo ndi kusinthiratu anga,” anadandaula motero Judy wazaka 13. “Sindimadzidalira ine mwini.” Komabe, Bwenzi lathu lakumwamba limapereka chitsogozo chenicheni cha moyo wachipambano m’Mawu ake olembedwa, Baibulo. Kwenikweni, uphungu woperekedwa m’buku la Baibulo la Miyambo wakonzedwa kuphunzitsa “mnyamata kudziŵa ndi kulingalira,” kumkhozetsa kuwongolera njira zake. (Miyambo 1:1-4; 3:1-6) Zimenezi zingakupatseni chidaliro! Mungathe kudziŵa njira yabwino koposa yokhalira ndi moyo.

Baibulo, pamodzi ndi zothandizira kuphunzira Baibulo zonga ngati magazini ano, limapereka uphungu mwachionekere pa mbali iliyonse ya moyo—kuyambira pa mmene mungasankhire mabwenzi kufika ku kakhalidwe kabwino ndi makolo anu. (Miyambo 1:8, 9; 13:20) Motero awo amene amalabadira chitsogozo chotero ‘angapatuke ku misampha ya imfa.’ (Miyambo 14:27) Mwachitsanzo, mtsikana wina wotchedwa Mae anaona mbale wake wakuthupi akunyozera miyezo ya Baibulo. Mbale wake ameneyo anafa imfa yamwamsanga yomvetsa chisoni chifukwa cha moyo wake wachisembwere. Mae anafotokoza mmene anakhozera kukaniza makhalidwe oipa amenewo akumati: “Ndimakumbukira bwino kwambiri miyezo ya Yehova ya makhalidwe abwino moonekera bwino, ndipo zimenezi zimandilimbitsa. Miyezo imeneyi imandithandiza kuona mmene Yehova alili weniweni ndi kuona kuti njira yake ndiyo yabwino koposa.”

Komabe, kukhala ndi Yehova monga bwenzi kumaphatikizapo zoposa kungophunzira miyezo yake. Mungaone chisamaliro chake chaumwini pa moyo wanu. Baibulo limanena za Mfumu Davide, amene anaphunzitsidwa ndi Mulungu kuyambira pa ubwana wake. Davide anadzakhala bwenzi la Mulungu, ndipo ngakhale kuti anakhala ndi “nsautso zambiri,” iye anaonadi Mulungu akuthandiza pa moyo wake. Davide analankhula za “zodabwitsa” za Mulungu zimene anamchitira ndi za “dzanja” la Yehova, kapena mphamvu yake, imene inasonyezedwa pa moyo wake. Pa maziko a zokumana nazo zaumwini zotero, Davide analemba kuti: “Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova; mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.” (Salmo 71:5, 17, 18, 20) Mungakhale ndi chidaliro chimodzimodzi chimenechi pamene muona madalitso a Yehova pa moyo wanu. Pamene muyesayesa kulondola chitsogozo chake—mosasamala kanthu za zovuta—mudzakhaladi mukuyenda ndi Mulungu pa unansi wamtengo wapatali.—Yerekezerani ndi Genesis 6:9.

Mulungu Amatithandiza Kulondola Njira Yoyenera

Ndi ziyeso zonse ndi zididikizo zimene zilipo m’moyo, kulondola chitsogozo cha Mulungu nkovuta. Zimenezi zinalidi choncho ndi Peggy, amene anali womwerekera ndi anamgoneka ndiponso wachiwerewere pamene anali wachichepere. Anatha kugonjetsa kumwerekera kwake ndi kusintha makhalidwe ake mwa kuphunzira Baibulo, ndipo motero anakulitsa ubwenzi ndi Mulungu. Koma Peggy anapitirizabe kuyang’anizana ndi zididikizo zimodzimodzizo zimene zinampangitsa kufunafuna pothaŵira kupyolera mwa anamgoneka. Atafunsidwa chimene chinamthandiza kupitirizabe kuzikaniza, iye anayankha kuti: “Ndingangonena kuti ndi mwa mzimu wa Yehova.”

Peggy anadziŵa kuti Mulungu amapatsa mabwenzi ake mzimu wake woyera, kapena mphamvu yogwira ntchito ndipo umenewu ungawapatse mphamvu kuti akhale monga mwa miyezo yake. (Machitidwe 5:32; 1 Akorinto 6:9-11) “Nthaŵi zina tsopano ndimamvanso ngati kale, makamaka pamene ndili ndekha,” akuvomereza motero Peggy, “koma pamenepo ndimangoyamba kupemphera. Kukhoza kugonjetsa mavuto ameneŵa kumandikondweretsa kwambiri kuposa kalikonse ndakachitapo m’moyo wanga.” Nkolimbikitsa chotani nanga kudziŵa kuti monga bwenzi, Mulungu “angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife.”—Aefeso 3:20.

Mzimu wa Mulungu umatithandiza kukhala ndi makhalidwe onga kuleza mtima, chifatso, ndi chiletso. (Agalatiya 5:22, 23) Ndiponso, m’mipingo ya Mboni za Yehova, akulu, kapena abusa, oikidwa ndi mzimu woyera, aikiziridwa ndi Mulungu kuti apereke chithandizo chogwira ntchito. Peggy akuwonjezera kuti: “Mpingo unandichirikiza kwambiri makamaka akulu. Linali thandizo labwino kwambiri.”

“Thanthwe la Mtima Wanga”

“Bwenzi limakonda nthaŵi zonse, ndipo limakhala mbale m’nthaŵi zatsoka.” Imanena motero Miyambo 17:17 mu The Basic Bible. Bwenzi limafunika makamaka “m’nthaŵi zatsoka.” Wamasalmo Asafu anavutika mtima kwambiri, komabe anayandikira kwa Mulungu monga bwenzi. Motero, ngakhale kuti ‘mtima wake udaŵaŵa’ ndi zopweteka za mkati, iye anati: “Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga.” (Salmo 73:21, 26, 28) Yehova, amene anamvetsetsadi mmene Asafu anamvera, anamlimbitsa mtima. Yehova anamthandiza kwambiri Asafu kotero kuti asataye chiyembekezo ndi chilimbiko.

Bwenzi lathu lakumwamba lingakhalenso posamira mutu panu ponga thanthwe m’nthaŵi ya nsautso. Wachichepere wina anaona zimenezi mwa zimene zinamchitikira. Pamene Bonnie anali ndi zaka 13, atsikana ena pasukulu laling’ono lakwawo kumidzi anayamba kufalitsa mphekesera yoipa, yomneneza. Kwa Bonnie zinaoneka ngati kuti aliyense anakhulupirira bodza limeneli. Anzake a m’kalasi ambiri anali kumnyalanyaza, ngakhale kumunyoza. “Mausiku ambiri ndinafika kunyumba ndikulira,” anafotokoza motero Bonnie. “Ndinafuna ngakhale kudzipha chifukwa ndinapwetekedwa mtima kwambiri.” Iye anatembenukira kwa anzake ena kuti amthandize. “Ndinayesa kulankhula ndi anthu, koma anaoneka kuti sanamvetsetse. Anachititsa vuto langa kuoneka ngati kuti lili losadetsa nkhaŵa. Nthaŵi zina ndinamva kukhala ndekhandekha.” Kodi nchiyani chimene chinampangitsa kusataya chiyembekezo pakati pa mavuto otero? Iye akupitiriza kuti: “Ngati si Yehova, ndikanadzipha. Ndimamkonda kwambiri. Iye ali bwenzi langa lapamtima.” Tsopano iye akudziŵa kuti unali ubwenzi wake ndi Mulungu umene unamthandiza kupirira chokumana nacho chovutitsa maganizo chimenecho.

Kudziŵa kuti Yehova amamvetsetsa mikhalidwe yathu ndipo amadziŵa zenizeni zimene zachitika kuli kotonthoza kwambiri pamene ena sakutisonyeza chisamaliro chimene tingayembekezere. Ndiponso, kudziŵa kuti Bwenzi lathu ndiye “Atate wa zifundo” kumathandiza kwambiri pamene tichitiridwa mwankhanza. Nthaŵi zina mtima wathu ungatitsutse, koma “Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zinthu zonse.” (2 Akorinto 1:3, 4; 1 Yohane 3:20) Kuona nkhaniyo mmene Yehova amaionera kungakhale kotonthoza kwenikweni. Mwachitsanzo, mnyamata wina wazaka 13 anagonedwa mwankhanza ndi amuna atatu. “Pambuyo pake, ndinali wamanyazi kwambiri ndipo ndinadzipatsa mlandu wa zimene zinandichitikira,” anavomereza motero. “Ndinachita tondovi kwambiri.” Ndiyeno anayamba kufufuza m’zofalitsa zozikidwa pa Baibulo za Watch Tower Society pa nkhani ya kugwiriridwa chigololo. “Pamene ndinaŵerenga nkhani imeneyi, sindinakhoze kulimbikira ndipo ndinalira. Ndinamva ngati kuti chikatundu cholema chinachotsedwa kumsana kwanga. Ndinangogwiriridwa. Mwa kudalira pa Yehova, banja, ndi mabwenzi, ndinakwanitsa kupirira nthaŵi yovutitsa imeneyi.” Ndi chichirikizo chotani nanga chimene mawu ozikidwa m’Baibulo amenewo anapereka!

Ubwenzi ndi Mulungu ungathandize m’njira zambiri! Tingakhale ndi chidaliro chenicheni m’moyo, kukulitsa mphamvu yamkati ya kulondola njira ya Mulungu, ndi kukhala ndi chichirikizo chonga thanthwe m’nthaŵi za nsautso. Koma kodi ndi motani mmene tingakulitsire ubwenzi woterewu? Nkhani yotsatira mu mndandanda uno idzafotokoza.

[Chithunzi patsamba 13]

Mulungu angakhale ‘thanthwe la mtima wanu’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena