Chilungamo Chimazindikiritsa Njira Zonse za Mulungu
“Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; Pakuti njira zake zonse ndi [chilungamo, “NW”]; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.”—Deuteronomo 32:4.
1. Ndi mikhalidwe yotani ya Yehova imene Mose anawunikira mu nyimbo yake kwa ana a Israyeli asanafe, ndipo nchifukwa ninji iye anayeneretsedwa kulankhula monga mmene iye anachitira?
YEHOVA, Woweruza wamkulu, Mpatsi wa Lamulo, ndi Mfumu, ali “wokonda [chilunjiko, NW] ndi chilungamo.” (Salmo 33:5; Yesaya 33:22) Mose, nkhoswe ya pangano la Chilamulo ndi mneneri “amen Yehova anadziŵana naye popenyana maso,” anakhala woyandikana mwathithithi ndi njira zolungama za Yehova. (Deuteronomo 34:10; Yohane 1:12) Mwamsanga Mose asanafe, anawunikira mkhalidwe wopambana wa chilungamo cha Yehova. Pa kumvetsera kwa mpingo wonse wa Israyeli, iye anaitana ndi mawu a nyimbo iyi: “Kumwamba kutchere khutu, ndipo ndidzanena; Ndi dziko lapansi limve mawu a mkamwa mwanga; . . . ndidzalalika dzina la Yehova; Nenani kuti Mulungu wathu ndi wamkulu. Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; Pakuti njira zake zonse ndi [chilungamo, NW]; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.”—Deuteronomo 32:1, 3, 4.
2. Ndimotani mmene chilungamo nthaŵi zonse chazindikiritsa zochita zonse za Mulungu, ndipo nchifukwa ninji ichi chiri chofunika?
2 Chilungamo chimazindikiritsa ntchito zonse za Yehova, ndipo chimasonyezedwa nthaŵi zonse m’chigwirizano changwiro ndi nzeru zake, chikondi, ndi mphamvu. Pa Yobu 37:23, mtumiki wa Mulungu Elihu anakumbutsa Yobu kuti: “Kunena za Wamphamvuyonse, sitingamsanthule; ndiye wa mphamvu yoposa; Koma mwa [chilungamo, NW] ndi [chilunjiko, NW] chochuluka samasawutsa.” Ndipo Mfumu Davide analemba kuti: “Pakuti Yehova akonda [chilungamo, NW], Ndipo sataya okondedwa ake.” (Salmo 37:28) Ndi chitsimikiziro chotonthoza chotani nanga! M’njira zonse za Mulungu, iye sadzakhoza ndi kamodzi komwe kusiya awo okhulupirika kwa iye. Chilungamo cha Mulungu chimatsimikizira chimenechi!
Chifukwa Chimene Chilungamo Chikusowekera
3. Nchiyani chomwe chikusoweka pakati pa anthu lerolino, ndipo ndimotani mmene ichi chayambukirira unansi wa munthu ndi Mulungu?
3 Popeza kuti Yehova ali Mulungu wa Chilungamo, Yemwe amakonda chilungamo, ndi “Mlengi wa malekezero a dziko lapansi,” nchifukwa ninji chilungamo chikusoweka chotere pakati pa anthu lerolino? (Yesaya 40:28) Mose akuyankha pa Deuteronomo 32:5 kuti: “Anamchitira zovunda si ndiwo ana ake, chirema nchawo; Iwo ndiwo mbadwo wopulukira ndi wokhotakhota!” Ntchito yoipa ya munthu yamulekanitsa iye chotero kuchoka kwa Mlengi wake kotero kuti malingaliro a Mulungu ndi njira zake zikulongosoledwa kukhala zopambana za munthu “monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi.”—Yesaya 55:8, 9.
4. Ndi njira yotani imene munthu wasankha kutenga, ndipo ndi kuti kumene ichi chamutsogolera?
4 Musaiwale kuti munthu sanalinganizidwe ndi Mlengi wake kuchita modziimira payekha kwa Iye. Yeremiya molondola akusanthula mkhalikwewo kaamba ka ife, akumanena kuti: “Inu Yehova, ndidziwa kuti njiira ya munthu siiri mwa iyemwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Kukana kwa munthu kwa njira za chilungamo za Mulungu ndi ulamuliro kwamuika iye pansi pa mphamvu zosiyana kotheratu ndipo zamphamvu kwenikweni zosawoneka, Satana Mdyerekezi ndi ziwanda zake zogwirizana naye. Mtumwi Yohane akulongosola mogogomezera kuti: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” Mphamvu za uchiwanda zimenezi ziribe chikondwerero chirichonse m’kusungirira chilungamo pakati pa mtundu wa anthu.—1 Yohane 5:19.
5. Perekani zitsanzo za kusoweka kwa chilungamo m’dziko lerolino.
5 Chitsanzo cha kusoweka kwa chilungamo m’masiku otsekera a dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu chinawunikiridwa mu 1984 ndi nduna yaikulu ya lamulo ya ku U.S., William French Smith. Akumachitira ndemanga pa kufufuza kwa milandu yopangitsa kuikidwa m’ndende m’maboma a ku America 12 pakati pa 1977 ndi 1983, Smith ananena kuti: “Unyinji ukudzinenera kuti olakwa oipa koposa—akupha anthu, ogwiririra chigololo, opititsa anam’goneka—akutumikira nyengo zochepera. Phunziro la bungwelo . . . likusonyeza mmene chiriri chopepuka kaamba ka aupandu ouma mutu kubwereranso ku makwalala kudzachita maupandu atsopano.” Nchosadabwitsa kuti Paul Kamenar wa ku Washington Legal Foundation ananena kuti: “Dongosolo la kachitidwe la chilungamo liri lofooka kaŵirikaŵiri.”
6. (a) Ndi kati komwe kanali kaimidwe ka mkhalidwe wabwino wa Yuda kuikidwa kwake m’ndende kusanachitike? (b) ndi mafunso otani amene Habakuku anafunsa, ndipo kodi iwo amagwira ntchito lerolino?
6 Chilungamo chinali chofooka mkati monse mwa mtundu wa Yuda usanagwe pamanja pa makamu a Babulo mu 607 B.C.E. Chotero, mneneri wa Mulungu Habakuku anawuziridwa mwaumulungu kunena kuti: “Pakuti chilamulo chalekeka, ndi [chilungamo, NW] sichitulukira konse; popeza woipa azinga [wolunjika, NW], chifukwa chake [chilungamo, NW] chituluka chopindika.” (Habakuku 1:4) Mkhalidwe wosalungama umenewu unapangitsa mneneriyo kufunsa Yehova kuti: “Mupenyereranji iwo akuchita mochenjera, ndi kukhala chete pamene woipa ammeza munthu [wolunjika, NW] woposa iyemwini?” (Habakuku 1:13) Lerolino, anthu oyambukiridwa ndi kachitidwe ka chisalungamo m’mbali zonse za machitachita a munthu angafunsenso bwino lomwe kuti: Nchifukwa ninji Mulungu wa chilungamo akupitirizabe kuyang’ana chisalungamo chochitidwa pa dziko lapansi? Nchifukwa ninji iye amalola ‘[chilungamo, NW] kutuluka chopindika’? Nchifukwa ninji iye “amakhala chete”? Mafunso ofunika amenewa, ndipo kokha Mawu a mtengo wapatali a Mulungu, Bailbulo, amapereka yankho lowona ndi lokhutiritsa.
Chifukwa Chimene Mulungu Walolera Chisalungamo
7. (a) Nchifukwa ninji munthu anataya Paradaiso imene Mulungu anampatsa? (b) Ndi nkhani zotani zomwe zinadzutsidwa mu Edeni, ndipo ndimotani mmene chilungamo cha Mulungu chinayankhira ku izi?
7 Ntchito za Mulungu ziri zangwiro, monga momwe zinatsimikiziridwa ndi Mose. Ichi chinali chowona m’chigwirizano ndi anthu aŵiri angwiro amene Mulungu anawaika m’Paradaiso ya mu Edeni. (Genesis 1:26, 27; 2:7) Kakonzedwe konseko kanali kolungama kaamba ka kakhalidwe kabwino ka mtundu wa anthu ndi chimwemwe. Cholembedwa chaumulungu chimatiwuza kuti: “Ndipo anaziwona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, tawonani, zinali zabwino ndithu.” (Genesis 1:31) Koma bata la mu Edeni silinakhalitse. Pansi pa chisonkhezero cha cholengedwa chauzimu chowukira, Hava ndi mwamuna wake, Adamu, anakokeredwa m’kuyang’anizana ndi Yehova pa njira Yake ya kuwalamulira iwo. Kuyenera kwa malamulo a Mulungu kwa iwo tsopano kunaikidwa m’chikaikiro. (Genesis 3:1-6) Chitokoso chimenechi ku chilungamo cha kulamulira kwa Mulungu chinadzutsa nkhani za makhalidwe zofunika kwambiri. Zolembedwa za m’mbiri za munthu wokhulupirika Yobu zimasonyeza kuti tsopano umphumphu wa zolengedwa zonse za Mulungu unakaikiridwanso. Chilungamo chinafuna kuti nthaŵi iperekedwe kuthetsa nkhani zimenezi za kufunika kwa chilengedwe cha ponse ponse.—Yobu 1:6-11; 2:1-5; onaninso Luka 22:31.
8. (a) Ndi mu mkhalidwe wa tsoka wotani mmene munthu tsopano anadzipeza iyemwini? (b) Ndi chizimezime chotani cha chiyembekezo chomwe chikuwondedwa m’nyimbo ya Mose?
8 Mkhalidwe wa tsoka wa mtundu wa anthu, wotulukapo chifukwa cha kukankhira pambali njira zolungama za Mulungu, waikidwa mofupikitsa ndi mtumwi Paulo pa Aroma 8:22. Pamenepo mtumwiyo analemba kuti: “Pakuti tidziŵa kuti cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi kufikira tsopano.” Kuchulukira kwa “kubuula” kumeneko ndi “zowawa” kwakhala chifukwa cha kusoweka kwa chilungamo pakati pa anthu popeza kuti “wina apweteka mnzake pomlamulira.” (Mlaliki 8:9) Koma chiyamikiro chipite kwa Mulungu Wamphamvuyonse kuti iye sadzalola kupotoza kwa chilungamo koteroko kupitirizabe kosatha! M’chiyang’aniro cha ichi, onani chimene Mose ananena mowonjezereka m’nyimbo yake, pa Deuteronomo 32:40, 41 (NW) kuti: “‘Pali moyo wanga kosatha,’ ngati Ine [Yehova] ndinola lupanga langa lonyezimira, ndi dzanja langa likagwira chiweruzo, ndidzabwezera chilango ondiwukira ndi kulanga ondida.”
9. Longosolani mmene dzanja la Yehova “linagwirira pa chiweruzo” pamene munthu anapanduka.
9 Dzanja la Yehova “linagwira chiweruzo” kumbuyoko mu Edeni. Popanda kuchedwa, Mulungu molondola anaweruza munthu ku imfa kaamba ka kusamvera kodzifunira kwa malamulo Ake. Iye anawuza Adamu kuti: “Chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:19) Mazana angapo pambuyo pake, mtumwi Paulo anaika mofupikitsa zotulukapo zoipitsitsa ku banja lonse la anthu a njira yauchimo ya Adamu. Iye analemba kuti: “Chifukwa chake monga, uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.”—Aroma 5:12.
10. Ndi mbewu ziŵiri ziti zomwe zakula chiyambire kuwukira kwa Adamu, ndipo ndimotani mmene Yehova wachitira?
10 Kutsatira kuyambika kwa kuwukira kwa munthu, Mulungu nayenso ananena kuti: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” (Genesis 3:15, 17-19) Kukula kwa mbewu ziŵiri zimenezi kwapitirizabe kwa zaka 6,000, ndipo “udani” wakhalapo nthaŵi zonse pakati pawo. Koma kupyola m’zochitika zosinthasintha pa dziko lapansi, njira za chilungamo za Yehova sizinasinthe. Mwa mneneri wake Malaki, iye akunena kuti: “Pakuti Ine Yehova sindisinthika.” (Malaki 3:6) Ichi chatsimikizira kuti njira za Mulungu zochitira ndi anthu opanda ungwiro ndi opanduka zazindikiritsidwa nthaŵi zonse ndi chilungamo. Palibe ndi kalelonse pamene Yehova anapatuka pa maprinsipulo ake okwezeka, olunjika, pamene akugwirizanitsa zimenezi ndi mikhalidwe yake yodabwitsa yomwe iri nzeru, chikondi, ndi mphamvu.
Mulungu Abwera ku Chipulumutso cha Munthu
11, 12. Ndimotani mmene Salmo 49 imalongosolera bwino lomwe mkhalidwe woipa wa munthu?
11 Mofanana ndi zogwirira za octopus yaikulu, chisonkhezero choipa cha Satana chafikira ku kukuta banja lonse la munthu. Eya, ndi mosowa chochita chotani nanga mmene anthu afunikira kupulumutsidwa osati kokha kuchoka ku chilango cha imfa chokhala pa iwo komanso kuchoka ku dongosolo la kachitidwe losalungama la kulamulira kwa anthu opanda ungwiro!
12 Mkhalidwe woipa wowopsya umene munthu wadzipezamo chiyambire pamene chilango cha imfa chinaperekedwa pa iye walongosoledwa bwino lomwe mu salmo lotsatirali la ana amuna a Kora: “Dzamveni kuno, anthu inu nonse; Tcherani khutu, inu nonse amakono, awamba ndi omveka omwe, Achuma ndi aumphawi omwe. Kuwombola mbale sangadzamuwombole, Kapena kumperekera dipo kwa Mulungu: (Popeza chiwombolo cha moyo wawo nchamtengo wake wapatali, Ndipo chilekeke nthaŵi zonse:) Kuti akhale ndi moyo osafa, Osawona chivundi.” (Salmo 49:1, 2, 7-9) Zonsezi zachitika m’chiyang’aniro cha chilungamo cholongosoledwa cha Mulungu!
13, 14. (a) Ndani yekha yemwe angapulumutse munthu, ndipo nchifukwa ninji uyo wosankhidwa ndi Mulungu ali woyenerera chotero? (b) Ndimotani mmene Yesu anakhalira “Eya” ku malonjezo onse a Mulungu?
13 Ndi kuti, kenaka, kumene thandizo lingachokere? Ndani yemwe angapulumutse munthu kochoka ku mphamvu ya imfa? Salmo likuyankha kuti: “Mulungu adzawombola moyo wanga ku mphamvu ya manda.” (Salmo 49:15) Kokha chikondi chachikulu cha Mulungu, chogwira ntchito m’chigwirizano ndi chilungamo Chake, chingakhoze kupulumutsa munthu kuchoka ku “mphamvu ya manda.” Mafunso athu anayankhidwa mowonjezereka mkati mwa kukambitsirana kwa nthaŵi ya usiku pakati pa Yesu ndi Mfarisi wochenjera Nikodemo. Yesu anamuwuza iye kuti: “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Mwana wa Mulungu asanadze ku dziko lapansi, iye anali ndi moyo ndi Atate wake kumwamba. M’kukhalapo kwake asanakhale munthu, iye analankhulidwa kukhala ‘akusekerera ndi ana a anthu.’ (Miyambo 8:31) Ndi molondola chotani nanga, kenaka, kwa Yehova kusankha cholengedwa chauzimu chachindunji chimenechi—Mwana Wake wobadwa yekha—kuwombola mtundu wa anthu!
14 Ponena za Yesu, Paulo ananena kuti: “Pakuti monga maŵerengedwe a malonjezano a Mulungu ali mwa iye Eya.” (2 Akorinto 1:20) Limodzi la malonjezano amenewa olembedwa ndi mneneri Yesaya likulozeredwa pa Mateyu 12:18, 21, pamene timaŵerenga ponena za Yesu kuti: Tawona mnyamata wanga, amene ndinamusankha, Wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; pa Iye ndidzaika mzimu wanga, Ndipo Iye adzalalikira [chilungamo, NW] kwa akunja. Ndipo akunja adzakhulupirira dzina lake.”—Onani Yesaya 42:1-4.
15, 16. Ndimotani mmene chinaliri chothekera kaamba ka Yesu kukhala “Atate Wosatha” wa mbadwa za Adamu?
15 Mkati mwa utmiki wa pa dziko lapansi wa Yesu, iye anachipanga kukhala chowonekera kuti anthu a mitundu yonse potsirizira pake akayembekezera m’dzina lake ndipo chotero kusangalala ndi mapindu a chilungamo cha Mulungu. Yesu ananena kuti: “Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” (Mateyu 20:28) Lamulo langwiro la Mulungu loperekedwa ku mtundu wa Israyeli linalongosola kuti: “Moyo kulipa moyo.” (Deuteronomo 19:21) Chotero, pambuyo pa kuika kwa Yesu moyo wake wangwiro mu imfa ndi kuwukitsidwa ndi mphamvu ya Mulungu kukwera kubwerera kumwamba, iye anali m’malo a kupereka mtengo wa moyo wake wangwiro kwa Yehova mosinthana ndi zoyenera za moyo wa Adamu. Mwanjirayi, Yesu anakhala “Adamu wotsirizayo [kapena wachiŵiri]” ndipo tsopano wapatsidwa mphamvu ya kuchita monga “Atate Wosatha” kwa ana onse okhulupirira a Adamu.—1 Akorinto 15:45; Yesaya 9:6.
16 Njira ya Mulungu ya chipulumutso kupyolera mwa mphatso yake yokondeka ya nsembe ya dipo ya Mwana wake, Yesu Kristu, mwakutero ‘yapangidwa kukhala yowonekera kwa amitundu.’ Ndipo ndithudi chazindikiritsidwa ndi chilungamo chaumulungu. Ndi oyamikira chotani nanga mmene tifunikira kukhalira kuti Mulungu wapereka njira kaamba ka ‘moyo wathu kuwomboledwa kuchoka ku mphamvu ya manda’!
Kusungirira Dipo
17, 18. Ndi ubwenzi wotani umene C. T. Russell analoŵamo mu ma 1870, koma ndimotani mmene Barbour anamdabwitsira iye mu 1878?
17 Mofanana ndi Akristu a m’zana loyamba, Mboni za Yehova mu nthaŵi zamakono zasungirira nthaŵi zonse chiphunzitso cha dipo la Yesu Kristu. Chiri chosangalatsa kukumbukira kuti prezidenti woyamba wa Watch Tower Society, Charles Taze Russell, pa nthaŵi imodzi anali mlembi mnzake ndi wochirikiza mwa chuma wa magazini ya chipembedzo yotchedwa The Herald of the Morning. Magaziniyo choyamba inafalitsidwa ndi a chiAdventist, N. H. Barbour wa ku Rochester, New York, U.S.A. Russell anali m’zaka zake za ma 20, koma Barbour anali wokulirapo kwambiri.
18 Kugwirizanako kunawoneka kukhala kukuyenda bwino kufikira 1878, pamene Barbour modabwitsa anafalitsa nkhani yokana chiphunzitso cha dipo. Akumalongosola chomwe chinachitika, Russell ananena kuti: “Mr. Barbour . . . analemba nkhani kaamba ka The Herald yokana chiphunzitso cha Chitetezero—yokana kuti imfa ya Kristu inali mtengo wa Dipo kaamba ka Adamu ndi fuko lake, akumanena kuti imfa ya Ambuye wathu sikakhozanso kukwaniritsa kaamba ka malipiro a chilango cha machimo a munthu kuposa ndi mmene kulasa kwa singano kupyola thupi la ntchentche ndi kuipangitsa kuvutika ndi kufa kukalingaliridwa ndi kholo la pa dziko lapansi kukhala chothetsera cholungama kaamba ka chimo laling’ono mwa mwana wake.”
19. (a) Nchiyani chimene chinali yankho la Russell ku kawonedwe ka Barbour ka dipo? (b) Kodi chokhumba cha Russell mogwirizana ndi Nsanja ya Olonda chazindikiridwa?
19 Russell akanakhoza kupatutsidwa ndi mnzake wamkuluyo, koma iye sanatero. Kwa miyezi ingapo, mkanganowu unapitirizabe mu masamba a magaziniyo, Barbour akumakana dipo ndipo Russell akumalemba mokomera ilo. Potsirizira pake, Russell analeka kuyanjana kulikonse ndi Barbour ndipo anayamba kufalitsa magazini ino, pa nthaŵiyo yotchedwa Zion’s Watch Tower and Herald of Christ’s Presence. C. T. Russell analongosola malingaliro awa ponena za magazini yatsopanoyo: “Kuyambira pa chiyambi, iyo yakhala yochirikiza yapadera ya Dipo; ndipo, mwa chisomo cha Mulungu, tiyembekeza kuti idzapitirizabe kutero kufikira mapeto.” Kodi chiyembekezo cha mkonzi Russell chazindikiridwa? Icho motsimikizirikadi chatero! M’kulongosola, tsamba 2 la kope limeneli limanena kuti magaziniyi “imalimbikitsa chikhulupiriro mwa Mfumu yolamulira tsopano, Yesu Kristu, amene mwazi wake wokhetsedwa ukutsegula njira kuti anthu apeze moyo wamuyaya.”
20. Ndi mafunso otani omwe adakali osayankhidwabe?
20 Pakali pano m’kukambitsirana kwathu, tatsatira njira ya chilungamo cha Mulungu m’kupeza chochititsa kaamba ka kupulumutsa mtundu wa anthu kochoka ku kukanidwira ku uchimo ndi imfa zokhala pa banja la munthu. Chikondi chinapereka njira imeneyo. Komabe, mafunso onga ngati awa amakhala osayankhidwa: Ndimotani mmene mapindu a nsembe ya dipo ya Yesu Kristu anapangitsidwa kukhalapo? Ndimotani mmene inu mungapindulire kuchokera ku iwo, ndipo mwamsanga chotani? Nkhani yotsatira ikupereka mayankho otsimikizirika kuwonjezera chidaliro chanu chakuti chilungamo chimazindikiritsa njira zonse za Mulungu.
Ndimotani Mmene Mukayankhira?
◻ Ndi kufunika kotani kumene Mulungu amaika pa chilungamo?
◻ Nchifukwa ninji pali kupanda chilungamo koteroko pakati pa mtundu wa anthu?
◻ Ndimotani mmene Mulungu anaperekera pothawirapo pa munthu kuchoka ku imfa?
◻ Ndi kufika ku utali wotani kumene Nsanja ya Olonda yasungirira dipo?
[Chithunzi patsamba 20]
Mose akulankhula mawu a nyimbo yake pa zidikha za Moabu
[Chithunzi patsamba 23]
Mulungu anakonda dziko lapansi kotero kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha