Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 1/8 tsamba 23-27
  • Mfungulo Zopezera Maphunziro Abwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mfungulo Zopezera Maphunziro Abwino
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chichirikizo cha Makolo, Mfungulo Yofunika
  • Kugwirizana ndi Aphunzitsi
  • Pamene Mwana Wanu Afika Panyumba
  • Limbikitsani Kuŵerenga ndi Kusenza Thayo
  • Kudzipereka kwa Wophunzira, Mfungulo Yofunika
  • Makolo—Khalani Ochirikiza a Mwana Wanu
    Galamukani!—1994
  • Mmene Makolo Angathandizire
    Galamukani!—2012
  • Makolo Omwe Achita Ntchito Yawo ya Kunyumba
    Galamukani!—1988
  • Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 1/8 tsamba 23-27

Mfungulo Zopezera Maphunziro Abwino

POSACHEDWAPA The New York Times inasonyeza nkhani ya pachikuto choyamba yonena za Latoya, wophunzira wakusekondale wazaka 16. Iye anati anali ndi zaka 11 pamene atate wake anayamba kummenya ndi kumgona. Amake, amene anali kugwiritsira ntchito anamgoneka, anali atachoka panyumba. “Panyumba,” inatero nyuzipepalayo, “panali malo osiyidwa opanda chimbudzi, kapena chipinda chimene anali kuwopa kugonamo.” Komabe, Latoya anali munthu wina. Ngakhale kuti panali zonsezi, kuchiyambiyambi kwa chaka chino Latoya anakhala pulezidenti wa National Honor Society kusukulu yawo yasekondale ndipo anapeza avareji ya B ya kupambana m’makalasi ake.

Kodi nchiyani chimene chingathandize mwana, ngakhale m’mikhalidwe yoipa, kupambana kusukulu? Kaŵirikaŵiri, mfungulo yopezera maphunziro abwino ndiyo kukhala ndi kholo limene limasamala—makamaka kholo limodzi kapena makolo onse aŵiri a mwanayo—limene lili lochirikiza ndi lodziloŵetsa kwambiri m’maphunziro a mwanayo. Wophunzira sukulu yasekondale wina wakalasi lapamwamba analingalira kuti zimenezi nzofunika kwambiri kwakuti anasonkhezereka kunena kuti: “Ana angapambane kusukulu ndi chichirikizo cha makolo.”

Aphunzitsi ochuluka akuvomereza. Mphunzitsi wa ku New York City akunena kuti: “Pa wophunzira aliyense amene amachita bwino ndi kumaliza maphunziro—ndipotu alipo ambiri—pamakhala kholo limene linali lochirikiza nthaŵi zonse.”

Chichirikizo cha Makolo, Mfungulo Yofunika

Chaka chatha Reader’s Digest inafufuza funso lakuti, “Kodi nchifukwa ninji ophunzira ena amachita bwino kuposa ena?” Limodzi la mayankho ena linali lakuti “mabanja olimba amasonkezera ana kusukulu.” Makolo a mabanja otero amapereka kwa ana awo chisamaliro chachikondi ndi kuwaphunzitsa makhalidwe ndi zonulirapo zoyenera. Komano kholo lina linati: “Simungathe kupereka chitsogozo choyenera ngati simudziŵa bwino zimene zikuchitika kusukulu.”

Njira yabwino yodziŵira ndiyo kupitako. Nakubala wina amene amapitako analemba kuti: “Pamene ndiyenda m’malikole a sukulu ya mwana wanga wamkazi, ndimamva mawu onyansa, otukwana. Ana amakhala akukumbatirana ndi kumpsompsonana paliponse—ngati zimenezi zikanakhala kanema, akanaikidwa m’gulu la X.” Maulendo otero angakuthandizeni kuzindikira mmene lerolino kulili kovuta kwa ana anu kupeza maphunziro abwino, ndiponso kukhala ndi makhalidwe abwino.

Nchifukwa chake, chofalitsidwa chakuti The American Teacher 1994 chinati: “Nkotheka kuti ophunzira amene amachitiridwa chiwawa anganene kuti makolo awo samafika kaŵirikaŵiri kusukulu, monga ngati kukaonana mwachindunji ndi aphunzitsi, pamisonkhano ya makolo kapena ya magulu, kapena kufika kusukulu.”

Nakubala wina wodera nkhaŵa anasonyeza zimene makolo afunikira kuchita. “Fikani kusukulu!” iye anatero. “Asonyezeni oyang’anira sukulu kuti muli ndi chidwi pa zimene mwana wanu akuphunzira. Ine ndimapita kusukulu kaŵirikaŵiri ndi kukakhala nawo m’kalasi.” Nakubala wina anagogomezera phindu la kukhala wochirikiza mwana. Iye anafotokoza kuti: “Ana anga apita kangapo ku ofesi kukalankhula ndi aphungu ndipo iwo angonyalanyazidwa. Pamene ndinapitako ndi mwana wanga tsiku lotsatira, anafunitsitsa kundithandiza—ndi mwana wangayo.”

Nakubala ameneyu wa anyamata anayi anagogomezeranso za kufunika kwa kusonyeza chidwi m’zochitika zakusukulu zimene zimakhudza mwachindunji maphunziro a mwana wanu. “Pitani patsiku lokadziŵana ndi aphunzitsi ndi makolo ena, tsiku la zionetsero za mapulojekiti asayansi—ku kanthu kalikonse kamene ana anu angakhale akuchita kamene makolo aitanidwa kudzakhalapo,” iye anatero. “Zimenezi zimakupatsani mpata wa kudziŵana ndi aphunzitsi a mwana wanu. Amafuna kudziŵa kuti mumaona maphunziro a mwana wanu kukhala mbali yofunika kwambiri ya moyo wake. Pamene aphunzitsi adziŵa zimenezi, amakonda kuwonjezera nthaŵi ndi kuyesayesa kuthandiza mwana wanu.”

Kugwirizana ndi Aphunzitsi

Makolo ena angalingalire kuti ali ndi zinthu zina zofunika kwambiri kuchita pamadzulo amene sukulu zimalinganiza mpambo wa kuchitira zinthu pamodzi kwa makolo ndi aphunzitsi. Komabe, kodi nchiyani kwenikweni chimene chimafunika kwambiri kuposa kupezeka kwanu kwa awo amene amayesa kuthandiza ana anu kupeza maphunziro abwino? Mgwirizano wabwino wa kholo ndi mphunzitsi ngwofunika!

Ku Russia kuli makonzedwe abwino okulitsira mgwirizano wa makolo ndi aphunzitsi. Magawo onse a maphunziro akusukulu amalembedwa mu chimene amatcha kuti Dnievnik—cholembapo ntchito yatsiku ndi tsiku chimene chimaphatikizidwa pamodzi ndi kalendala. Wophunzira ayenera kupita ndi Dnievnik yake m’kalasi lililonse ndi kuisonyeza kwa aphunzitsi ataifuna. Ophunzira ayeneranso kusonyeza Dnievnik kwa makolo awo, amene amapemphedwa kuisaina sabata lililonse. Zili monga momwe Victor Lobachov, atate wa ku Moscow wa ana ausinkhu wakusukulu ananenera, “chidziŵitso chimenechi chimathandiza makolo kudziŵa magawo antchito ndi magiredi a ana awo.”

Komabe, aphunzitsi lerolino amadandaula kaŵirikaŵiri kuti makolo amalephera kusonyeza chidwi pamaphunziro a ana awo. Mphunzitsi wina wa sukulu yasekondale ku United States anati panthaŵi ina anatumiza makalata 63 kwa makolo akumawadziŵitsa za kusachita bwino m’maphunziro kwa ana awo. Makolo atatu okha ndiwo amene anaonana naye!

Zoonadi, zimenezo nzomvetsa chisoni! Makolo ayenera kukhala oloŵetsedwa kwambiri m’maphunziro a mwana wawo, limene lili thayo lawo lalikulu. Mphunzitsi wina anafotokoza nkhaniyo molondola pamene anati: “Cholinga chachikulu cha maphunziro akusukulu ndicho kuchirikiza makolo kutulutsa achichepere osinkhuka okhoza kusenza thayo.”

Motero, makolo ayenera kuyamba kudziŵana ndi aphunzitsi a ana awo. Zili monga momwe kholo lina linanenera kuti, “aphunzitsi amafuna kukhala omasuka kukufikirani panthaŵi iliyonse.” Ndipo makolo ayenera kulola—ngakhale kulimbikitsa—aphunzitsi kulankhula mosabisa ponena za mwana wawo. Makolo ayenera kufunsa mafunso olunjika onga akuti: Kodi mukupeza mavuto ndi mwana wanga? Kodi ngwaulemu? Kodi amafika pamaphunziro onse? Kodi amafika panthaŵi yake?

Bwanji ngati mphunzitsiyo atchula kanthu kena ponena za mwana wanu kamene kali kosakondweretsa? Musalingalire kuti si zoona. Mwachisoni, ana ambiri amene amakhala ngati aulemu kunyumba kapena kumalo awo olambirirako kwenikweni amakhala ndi moyo wapaŵiri. Chotero mvetserani mwaulemu zimene mphunzitsiyo akunena, ndipo fufuzani zimene iyeyo akunena.

Pamene Mwana Wanu Afika Panyumba

Kodi inu monga kholo mumamva motani pamene mufika panyumba kuchokera kuntchito? Wotopa? Wogwiritsidwa mwala? Mwana wanu angakhale akumva moipirapo pamene afika panyumba kuchokera kusukulu. Chotero atate wina analimbikitsa kuti: “Pangitsani kufika panyumba kukhala chinthu chabwino. Mwinamwake tsikulo linali lovuta kwambiri kwa iwo.”

Pamene kuli kotheka, zimakhaladi bwino ngati kholo lili panyumba pamene mwanayo afika. Zili monga momwe nakubala wina ananenera, “ana sangakuuzeni zimene zikuchitika ngati simulipo kuti mulankhule nawo. Chotero ndimatsimikiza kukhala ndili panyumba pamene anawo afika.” Kholo lifunikira kudziŵa osati kokha zimene mwana wake akuchita komanso zimene iyeyo akuganiza ndi mmene akumvera. Kudziŵa zimenezi kumaloŵetsamo nthaŵi yochuluka, khama, ndi kufunsa modekha. (Miyambo 20:5) Kulankhulana kwa tsiku ndi tsiku nkofunika.

Mphunzitsi wa sukulu yapulaimale ku New York City anati: “Tsiku lina, mwana wanu angakhale ataphunzitsidwa makhalidwe a sukulu zokhala m’mavuto.” Chotero analimbikitsa kuti: “Khalani maso pa zimene zikukula mumtima mwa mwana wanu. Patulani nthaŵi, mosasamala za mmene mwatopera, kuti mumchititse kunena zakukhosi ndi kuloŵetsa makhalidwe abwino pamalo a makhalidwe oipa.”—Miyambo 1:5.

Mofananamo, mphunzitsi wina wa sukulu yasekondale wanthaŵi yaitali analangiza kuti: “M’malo mwa kungofunsa zimene zachitika kusukulu, kungakhale kopindulitsa kufunsa mafunso achindunji ponena za tsikulo ndi zochitika zake. Zimenezi siziyenera kuchitidwa m’njira yaukali kapena yofunafuna zifukwa koma mwamakambitsirano abwino ndi mwanayo.”

Richard W. Riley, mlembi wazamaphunziro wa United States, analimbikitsa kuti: “Lankhulani mwachindunji ndi mwana wanu, makamaka ana anu osinkhuka, ponena za ngozi ya anamgoneka ndi zakumwa zaukali ndi makhalidwe amene mukufuna kuti ana anu akhale nawo. Kukambitsirana kwachindunji kotero, ngakhale kukuvuteni motani, kungapulumutse miyoyo yawo.”

Kholo, makamaka limene lili ndi mathayo mumpingo wachikristu, siliyenera konse kupereka chithunzi chakuti lili lotanganitsidwa kosakhoza kumvetsera zimene ana ake akunena. Ngakhale kuti zimene adzanena zidzakhala zovutitsa maganizo, asonyezeni ndi nkhope yanu ndi mkhalidwe kuti muli wokondwa kuti akulankhula nanu momasuka. Wophunzira wina analangiza kuti: “Musaipidwe pamene mwana wanu alankhula za anamgoneka kapena za kugonana kusukulu.”

Chifukwa cha kusweka kwa mabanja, lerolino pali ambiri amene angatchedwe kuti ‘ana amasiye.’ (Yobu 24:3; 29:12; Salmo 146:9) Mumpingo wachikristu, kaŵirikaŵiri mumakhala wina amene angathandize wachichepere amene afunikira thandizo. Kodi ndinu amene mungatero?

Limbikitsani Kuŵerenga ndi Kusenza Thayo

Achichepere ambiri samaika mtima pantchito ya kusukulu monga Latoya, amene tatchula poyamba. Ambiri amafuna kuwalimbikitsa kwambiri kuŵerenga. Ponena za ana ake, yemwe kale anali phungu wa sukulu ya ku New York City Joseph Fernandez anati: “Tinali ndi nyengo zoikika za kuŵerenga panyumba. Tinawapezera mabuku, tinawalimbikitsa kupita kulaibulale, ndi kuona kupita kusukulu ndi kutengamo mbali kukhala chinthu chofunika kwambiri.”

Woyang’anira sukulu wina anati: “Tifunikira kupatsa ana athu mabuku ndi kuwasimbira nkhani monga momwe timachitira tsopano lino ndi wailesi yakanema, akanema, mavidiyo ndi malo ogulitsiramo zinthu.” Pamene ana akuchita homuweki yawo, makolo angalinganize kuti azikhala pafupi akumachita phunziro laumwini kapena kuŵerenga. Motero ana anu angaone kuti mumaŵerengera maphunziro.

M’nyumba zambiri wailesi yakanema ili chopinga chachikulu koposa pakuphunzira. “Podzafika zaka 18,” akutero mphunzitsi wina, “achichepere amakhala atathera maola 11,000 m’kalasi ndipo 22,000 akumaonerera wailesi yakanema.” Makolo angafunikire kuikira ana awo malire pakuonerera TV, mwinamwake iwo eniwo akumaonerera panthaŵi zina. Ndiponso, dziperekeni inu mwini pakuphunzira kanthu kena ndi ana anu. Ŵerengani pamodzi. Linganizani nthaŵi tsiku ndi tsiku yopendera homuweki.

Ana amalandira magawo antchito ambiri kusukulu oti akalembe. Kodi iwo angakwaniritse kulemba zimenezi? Mwinamwake iwo angatero ngati inu mwawaphunzitsa kusamalira mathayo panyumba. Njira yofunika yochitira zimenezi ndiyo kuwagaŵira ntchito zapanyumba zatsiku ndi tsiku. Pamenepo sonyezani kuti mukufuna kuti achite zimenezo malinga ndi nthaŵi yake yolinganizidwa. Zoona, kuphunzitsa kumeneko kumafuna kuyesayesa kwanu kwakukulu, komano kumaphunzitsa ana anu kusenza thayo limene afunikira kuti apambane kusukulu ndi m’moyo wamtsogolo.

Kudzipereka kwa Wophunzira, Mfungulo Yofunika

Phungu wopereka chitsogozo Arthur Kirson anasonyeza mfungulo ina ya maphunziro abwino pamene anati ponena za Latoya, wotchulidwa pachiyambi: “Nthaŵi yoyamba imene ndinakumana naye inali pambuyo pa chimodzi cha zochitika zina zazikulu zakunyumba. Mwanayo anali atakhala potero ndi nkhope yokandikakandika [chifukwa cha nkhanza imene anati atate wake anamchitira]. Ndipo chinthu chokha chimene ndinaona akudera nacho nkhaŵa chinali ntchito yakusukulu.”

Inde, mfungulo yofunika ya maphunziro abwino ndiyo kudzipereka kwambiri kwa mwanayo pakuphunzira. Wachichepere wina wa ku New York City akuti: “M’sukulu masiku ano zili kwa ophunzira kukulitsa kudzisonkhezera ndi kudzilanga kuti apindule.”

Mwachitsanzo, nakubala wina amene anali ndi nkhaŵa pa maphunziro a mwana wake anauzidwa ndi mphunzitsi kuti: “Musadere nkhaŵa akazi a Smith. Justin ngwanzeru kwambiri, safunikira kudziŵa kutchula zilembo. Adzakhala ndi mlembi womchitira zimenezo.” Mosasamala kanthu kuti mwanayo angakhale wanzeru motani, kuphunzira maluso a kuŵerenga ndi kulemba—kuphatikizapo kulemba bwino, kulemba zoŵerengeka, ndi kulemba zilembo kolondola—nkofunika.

Mochititsa mantha, aphunzitsi ena sanatsutse pamene katswiri wina wa psychology Carl Rogers anati: “Palibe amene ayenera kuyesa kuphunzira kanthu kena kamene wina akukaona kukhala kosafunika.” Kodi cholakwika nchiyani ndi mawuwa? Nkwachionekera kuti mwana kaŵirikaŵiri samatha kuona mapindu amtsogolo a zimene akupemphedwa kuphunzira. Nthaŵi zambiri iye samazindikira msanga mapindu ake kufikira panthaŵi ina m’moyo. Mwachionekere, mwanayo pakali pano afunikira kukhala wodzipereka kuti apeze maphunziro abwino!

Cindy, wazaka 14 wa m’giredi lachisanu ndi chinayi, ali chitsanzo chabwino cha wachichepere amene ali wodzipereka motero. Iye akulongosola kuti: “Tikaŵeruka kusukulu ndimatsalira kuti ndikambitsirane ndi aphunzitsi ndi kudziŵana nawo. Ndimayesa kudziŵa zimene amafuna kwa ophunzira awo.” Amatcheranso khutu m’kalasi ndipo amaika mtima pa homuweki yake. Pamene akumvetsera m’kalasi kapena pamene akuŵerenga, ophunzira ochita bwino amakonda kuchita zimenezo ali ndi pensulo ndi pepala kuti alembe manotsi ofunika.

Chofunikanso pakupeza maphunziro abwino ndicho kutsimikiza kupeŵa mayanjano oipa. Cindy anasimba kuti: “Nthaŵi zonse ndimafunafuna munthu wina amene ali ndi makhalidwe abwino. Mwachitsanzo, ndimafunsa anzanga akusukulu zimene amaganiza ponena za uje ndi uje amene amagwiritsira ntchito anamgoneka kapena kuchita chisembwere. Ngati anena kuti, ‘Zaipa pati?’ ndimazindikira kuti si mabwenzi abwino. Koma ngati wina anyansidwadi ndi khalidwe limenelo nanena kuti amafuna kukhala wosiyana nawo, pamenepo ndimamsankha kukhala naye panyengo yachakudya.”

Mwachionekere pali zovuta zambiri lerolino kuti munthu apeze maphunziro abwino. Koma maphunziro amenewo ali otheka ngati ophunzira ndi makolo omwe agwiritsira ntchito mfungulo. Kenako tidzafotokoza za makonzedwe ena amene angakuthandizeni kwambiri kupeza maphunziro abwino.

[Bokosi patsamba 23]

Kulekerera Kapena Chilango Chachikondi?

Baibulo limachenjeza kuti kulekerera ana kumabweretsa tsoka. (Miyambo 29:21) Povomereza zimenezi, Albert Shanker, pulezidenti wa American Federation of Teachers, anati: “Pali makolo amene amaganiza kuti akuchita zonse moyenera kwa ana awo ngati achita zonse mwanjira imene anawo akufuna kuti iwo achite. Ndipo tidziŵa kuti kumeneko nkulakwa.”

Ngakhalenso ana ambiri amadziŵa kuti kulekerera kumeneko nkulakwa. Kuchiyambiyambi kwa chaka chino nyuzipepala ina ya ku Massachusetts inasimba kuti: “Kufufuza kochitidwa pakati pa ophunzira a m’giredi lachisanu ndi chimodzi mpaka lakhumi ndi ziŵiri a ku 1572 West Springfield kunapeza kuti ‘kulekerera kwa makolo’ nkumene kumachititsa ana amsinkhu umenewu kugwiritsira ntchito anamgoneka ndi zakumwa zaukali osati chitsenderezo cha ausinkhu wawo.”

Kulekerera ana kumeneko kwachirikizanso mliri wa chiwerewere. Indedi, monga momwe Baibulo limanenera, kulephera kupereka chilango kumabweretsa manyazi pabanja.—Miyambo 29:15.

[Bokosi patsamba 26]

Zimene Makolo Angachite

✔ Dziŵani sukulu ya mwana wanu, zolinga zake, ndi mmene imaonera makhalidwe ndi zikhulupiriro zimene muli nazo.

✔ Dziŵanani ndi aphunzitsi a mwana wanu, ndipo yesani kukulitsa unansi wabwino ndi iwo.

✔ Khalani ndi chidwi chachikulu pa homuweki ya mwana wanu. Ŵerengani naye nthaŵi zambiri.

✔ Lamulirani zimene mwana wanu amaonerera pa TV ndi nthaŵi imene amaonerera.

✔ Yang’anitsitsani kadyedwe ka mwana wanu. Zakudya zosamanga thupi zingakhale ndi ziyambukiro zoipa pa kusumika maganizo kwake.

✔ Tsimikizirani kuti mwana wanu amagona mokwanira. Ana otopa samaphunzira bwino.

✔ Yesani kuthandiza mwana wanu kusankha mabwenzi abwino.

✔ Khalani bwenzi lapamtima la mwana wanu. Afunikira mabwenzi okula msinkhu amene angapezeke.

Zimene Ana Angachite

✔ Ndi thandizo la makolo anu, linganizani zonulirapo zamaphunziro ndi njira zozipezera. Kambitsiranani zonulirapo zimenezi ndi aphunzitsi anu.

✔ Sankhani masabujekiti anu mosamala ndi thandizo la aphunzitsi ndi makolo anu. Makosi odzisankhira amene ali okhweka kaŵirikaŵiri sali abwino kwambiri.

✔ Yesani kukulitsa unansi wabwino ndi aphunzitsi anu. Fufuzani zimene akufuna kwa inu. Kambitsiranani nawo za kupita patsogolo kwanu ndi mavuto.

✔ Tcherani khutu m’kalasi. Musatengeke ndi khalidwe losokoneza zinthu.

✔ Sankhani mabwenzi anu mwanzeru. Angathe kuthandiza kapena kudodometsa kupita patsogolo kwanu kusukulu.

✔ Lembani bwino homuweki yanu ndi magawo ena antchito monga momwe mungathere. Patulani nthaŵi yapadera. Pemphani makolo anu kapena munthu wina wachikulire kuti akuthandizeni ngati mukufuna thandizo.

[Chithunzi patsamba 24]

Mvetserani mwaulemu ngati mphunzitsi ali ndi dandaulo pamwana wanu

[Chithunzi patsamba 25]

Funsani mwana wanu ponena za sukulu tsiku lililonse

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena