Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 6/1 tsamba 4-7
  • Nchifukwa Ninji Kuwopa Mulungu, Osati Anthu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nchifukwa Ninji Kuwopa Mulungu, Osati Anthu?
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Msampha wa Kuwopa Munthu
  • Kodi Ndani Amene Tiyenera Kuwopa?
  • Kuwopa Mulungu Wa Chikondi?
  • Kodi Ndani Yemwe Mumawopa?
  • Nchifukwa Ninji Tiyenera Kuwopa Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Khalani ndi Mtima Woopa Yehova
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kuwopa Mulungu Kodi Kungakupindulitseni?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kuphunzira Kupeza Chisangalalo M’kuwopa Yehova
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 6/1 tsamba 4-7

Nchifukwa Ninji Kuwopa Mulungu, Osati Anthu?

“KUWOPA anthu kutchera msampha; koma wokhulupirira Yehova [adzatetezeredwa, NW].” (Miyambo 29:25) Ndi mawu amenewa mwambi wakale umatikhalitsa maso ku mtundu wa kuwopa kumene kulidi ululu wa maganizo​—kuwopa munthu. Iko kwafanizidwa ndi msampha. Nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti nyama yaing’ono, monga kalulu, imakhala yopanda thandizo pamene yagwidwa mumsampha. Iyo imafuna kuthaŵa, koma msamphawo umaigwira mowonjezerekawonjezereka. M’nkholeyo, m’chenicheni, amathedwa mphamvu.

Ngati ife tagwidwa ndi kuwopa munthu, tiri kwakukulukulu mofanana ndi kalulu ameneyo. Tingadziŵe chimene tiyenera kuchita. Tingafune ngakhale kuchichita icho. Koma mantha amatigwira ife mu ukapolo. Timakhala othedwa mphamvu ndi osakhoza kuchita kanthu.

Msampha wa Kuwopa Munthu

Lingalirani zitsanzo zina m’nthaŵi za Baibulo za awo omwe anagwidwa ndi msampha wa mantha. M’masiku a Yoswa, amuna 12 anatumidwa kukazonda dziko la Kanani kuloŵerera kokonzekeredwa kwa Aisrayeli kusanachitike. Azondiwo anabwerera ndi kusimba kuti dzikolo linali lachonde ndi lolemera, mongadi mmene Mulungu ananenera. Koma khumi a azondiwo anawopsyezedwa ndi nyonga ya nzikazo. Chotero, atagwidwa ndi kuwopa munthu, iwo anapereka ripoti losinjiriridwa ponena za nyonga imeneyi kwa Aisrayeli ndi kuchititsa mtundu wonse kugwidwa ndi mantha. Aisrayeli anakana kumvera lamulo la Mulungu la kuloŵa m’Kanani ndi kulanda dzikolo. Monga chotulukapo, mkati mwa zaka 40 zotsatira, chiŵerengero chonse cha amuna achikulire a nthaŵiyo, kusiyapo kokha oŵerengeka, anafa m’chipululu.​—Numeri 13:21–14:38.

Yona anali m’nkhole wina wa kuwopa munthu. Pamene iye anagawiridwa kukalalikira mu mzinda waukulu wa Nineve, iye “ananyamuka kuti athaŵire ku Tarisi, kuzemba Yehova.” (Yona 1:3) Chifukwa ninji? Anthu a ku Nineve anali ndi mbiri ya kukhala anthu a nkhalwe ndi achiwawa, ndipo Yona motsimikizirika anadziŵa chimenecho. Kuwopa munthu kunam’chititsa iye kuthaŵira m’njira yosiyana kuchoka ku Nineve. Zowona, iye pomalizira pake analandira ntchito yake koma kokha pambuyo pa kulandira chilango chachilendo kuchokera kwa Yehova.​—Yona 1:4, 17.

Ngakhale mafumu angawope anthu. Pa chochitika china, Mfumu Sauli mwachindunji sanamvere lamulo lochokera kwa Mulungu. Chodzikhululukira chake? “Ndinachimwa; pakuti ndinalumpha lamulo la Yehova, ndi mawu anu omwe; chifukwa ndinawopa anthuwo, ndi kumvera mawu awo.” (1 Samueli 15:24) Zaka mazana angapo pambuyo pake, pamene Yerusalemu anali pansi pa kuwukiridwa ndi Ababulo, Yeremiya, mneneri wokhulupirika, anapatsa uphungu Mfumu Zedekiya kugonjera ndipo mwakutero kupulumutsa Yerusalemu kuchokera ku kukhetsa mwazi kochulukira. Koma Zedekiya anakana. Chifukwa ninji? Iye anawulula kwa Yeremiya kuti: “Ine ndiwopa Ayuda amene anandipandukira ine kunka kwa Akasidi, angandipereke ine m’manja mwawo, angandiseke.”​—Yeremiya 38:19.

Pomalizira, ngakhale mtumwi akakhoza kukhala wamantha. Pa tsiku lomwe Yesu anayenera kufa, iye anachenjeza otsatira ake kuti onse akamsiya iye. Petro, ngakhale kuli tero, molimba mtima analengeza kuti: “Ambuye, ndiripo ndikapite ndi inu ku ndende ndi ku imfa.” (Luka 22:33; Mateyu 26:31, 33) Mawu amenewo anatsimikizira kukhala olakwa chotani nanga! Kokha maora angapo pambuyo pake, Petro mwamantha anakana kuti anali atakhala ndi Yesu kapena ngakhale kumudziŵa iye. Kuwopa munthu kunagonjetsa iye! Inde, kuwopa munthu kulidi ululu wa maganizo.

Kodi Ndani Amene Tiyenera Kuwopa?

Ndimotani mmene tingalakire kuwopa munthu? Mwakukuloŵa iko m’malo ndi mantha abwino owonjezereka. Mtundu umenewu wa mantha unalimbikitsidwa ndi mtumwi mmodzimodziyo, Petro, pamene iye anati: “Opani Mulungu.” (1 Petro 2:17) Mngelo wowonedwa ndi Yohane mu Chibvumbulutso anafuula kwa mtundu wa anthu kuti: “Opani Mulungu, mpatseni ulemerero.” (Chibvumbulutso 14:7) Mfumu ya nzeru Solomo nayonso inalimbikitsa mantha oterowo, pamene iyo inanena kuti: “Mawu atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti [iri ndi thayo lonse la munthu, NW].” (Mlaliki 12:13) Inde, kuwopa Mulungu kuli thayo.

Kuwopa Mulungu kumadzetsa mapindu. Wamasalmo wakale anaimba kuti: “Indedi chipulumutso chake [cha Yehova] chiri pafupi ndi iwo akumuwopa iye.” (Salmo 85:9) Mwambi wa Baibulo nawonso umagogomezera kuti: “Kuwopa Yehova kutanimphitsa masiku.” (Miyambo 10:27) Inde, kuwopa Yehova kuli chinthu chabwino, chopindulitsa. ‘Koma motsimikizirika,’ inu munganene kuti, ‘Yehova ali Mulungu wokonda. Nchifukwa ninji tiyenera kuwopa Mulungu wachikondi?’

Kuwopa Mulungu Wa Chikondi?

Chifukwa chakuti kuwopa Mulungu sikuli mantha opondereza, kuwopa kothetsa mphamvu komwe kumagwira anthu m’mikhalidwe ina. Iko kuli mtundu wa kuwopa kumene mwana angamve kaamba ka atate wake, ngakhale kuti iye amawakonda atate wake ndi kudziŵa kuti atate wake amamkonda iye.

Kuwopa Mulungu kuli kwenikweni ulemu waukulu kaamba ka Mlengi womwe umachokera ku kuzindikira kuti iye ali magwero otheratu a chilunjiko, chilungamo, nzeru, ndi chikondi. Iko kumaloŵetsamo mantha abwino a kusakondweretsa Mulungu chifukwa chakuti iye ali Woweruza Wamkulu wokhala ndi mphamvu ya kupereka mphoto ndi kulanga. “Kugwa m’manja a Mulungu wamoyo nkowopsya,” analemba tero mtumwi Paulo. (Ahebri 10:31) Chikondi cha Mulungu sichiri chinthu chinachake choyenera kutengedwa mosasamala, osatinso chiweruzo chake chiri chinthu choseŵeretsa. Chimenecho ndicho chifukwa chake Baibulo limatikumbutsa ife kuti: “Chiyambi cha nzeru ndicho kuwopa Yehova.”​—Miyambo 9:10.

Tiyenera kukumbukira, ngakhale kuli tero, kuti pamene kuli kwakuti Yehova ali ndi mphamvu ya kulanga awo omwe samamumvera iye​—ndipo iye kaŵirikaŵiri wachita tero​—iye mwanjira iriyonse sali ndi ludzu la kukhetsa mwazi kapena wankhanza. Iye ndithudi ali Mulungu wachikondi, ngakhale kuti iye, mofanana ndi kholo lachikondi, nthaŵi zina amakwiya mwachilungamo. (1 Yohane 4:8) Ndicho chifukwa chake kumuwopa iye kuli kwabwino. Iko kumatitsogolera ife kumvera malamulo ake, omwe anakonzedwa kaamba ka ubwino wathu. Kumvera malamulo a Mulungu kumabweretsa chimwemwe, pamene kuli kwakuti kusamvera iwo nthaŵi zonse kumabweretsa zotulukapo zoipa. (Agalatiya 6:7, 8) Wamasalmo anawuziridwa kulengeza kuti: “Opani Yehova, inu oyera mtima ake; chifukwa iwo akuwopa iye sasoŵa.”​—Salmo 34:9.

Kodi Ndani Yemwe Mumawopa?

Ndimotani mmene kuwopa Mulungu kumatithandizira ife kugonjetsa kuwopa munthu? Chabwino, anthu angatinyoze ife kapena ngakhale kutizunza ife kaamba ka kuchita chimene chiri chabwino, chomwe chimaika chididikizo pa ife. Koma kuwopa Mulungu kwaulemu kudzaika chididikizo pa ife kuti timamatire ku njira yabwino, popeza sitimafuna kusamukondweretsa iye. M’kuwonjezera, chikondi cha Mulungu chidzatifulumiza kuchita chomwe chimadzetsa chisangalalo ku mtima wake. Kuwonjezerapo, ife timakumbukira kuti Mulungu amatifupa molemerera kaamba ka kuchita chomwe chiri chabwino, chomwe chimatipangitsa ife kumukonda iye ngakhale moposerapo ndi kutipangitsa ife kufuna kuchita chifuno chake. Chotero, kapenyedwe kolinganizika ka Mulungu kamatithandiza kulaka mantha aliwonse amene tingakhale nawo a anthu.

Mwachitsanzo, ambiri akudidikizidwa m’kuchita chimene chiri cholakwika chifukwa cha kuwopa chimene anzawo amaganiza. Anthu achichepere pa sukulu angasute, kugwiritsira ntchito chinenero choipa, kudzitama pa kuzoloŵera kachitidwe ka kugonana (kenikeni kapena kongolingalira), ndipo ngakhale kuyesera ndi zakumwa zoledzeretsa kapena anam’goneka. Chifukwa ninji? Osati chifukwa chakuti nthaŵi zonse amafuna kutero, koma chifukwa chakuti iwo amawopa chimene anzawo akanena ngati iwo anachita mosiyanako. Kwa wa zaka za pakati pa 13 ndi 19, kunyozedwa ndi kusekedwa kungakhale kovuta kupirira mofanana ndi chizunzo chakuthupi.

Munthu wamkulu nayenso angadzimve wodidikizidwa kuchita cholakwa. Mwinamwake mkulu pa ntchito adzawuza wolembedwa ntchito kukulitsa mtengo wa zinthu wa wogula kapena kudzaza chipepala cha msonkho cha kampani mosawona mtima kotero kuti achepetse ngongole ya msonkhowo. Mkristu angadzimve kuti ngati iye samvera, adzataikiridwa ntchito yake. Chotero, kuwopa munthu kungamudidikize iye kuchita chimene chiri cholakwika.

M’nkhani zonse ziŵiri, kuwopa Mulungu kwabwino ndi ulemu kaamba ka malamulo ake kukachinjiriza Mkristu kusathedwa mphamvu ndi kuwopa munthu. Ndipo chikondi cha Mulungu chikamuletsa iye kudziloŵetsa m’machitachita amene Mulungu awaletsa. (Miyambo 8:13) Mowonjezerapo, chikhulupiriro chake mwa Mulungu chikamutsimikizira iye kuti ngati achita mogwirizana ndi chikumbumtima chophunzitsidwa ndi Baibulo, Mulungu akam’chirikiza iye mosasamala kanthu za chotulukapo. Mtumwi Paulo analongosola chikhulupiriro chake ndi mawu awa: “Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo.”​—Afilipi 4:13.

Baibulo limapereka zitsanzo zambiri za amuna ndi akazi amene anali okhulupirika kwa Yehova pansi pa ngakhale ziyeso zowopsya koposa. Iwo “anayesedwa ndi matonzo ndi zokwapulira, . . . ndi kuwatsekera m’ndende; anaponyedwa miyala, anachekedwa pakati, anayesedwa, anaphedwa ndi lupanga.” (Ahebri 11:36, 37) Koma iwo sanalole kuwopa munthu kulamulira maganizo awo. M’malomwake, iwo anatsatira njira yanzeru imodzimodziyo imene Yesu pambuyo pake anapatsa ophunzira ake: “Ndipo musamawopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuwupha; koma makamaka muwope iye [Mulungu], wokhoza kuwononga moyo ndi thupi lomwe mu Gehena.”​—Mateyu 10:28.

Kutsatira uphungu wa Yesu umenewu kuwopa Mulungu m’malo mwa munthu kunatheketsanso Akristu oyambirira kupirira zovuta za mtundu uliwonse, ziyeso, ndi zizunzo “kaamba ka chifukwa cha mbiri yabwino.” (Filemoni 13, NW) Mtumwi Paulo ali chitsanzo chofunikira kuzindikira cha ichi. M’kalata yake yachiŵiri kwa Akorinto, iye akusonyeza mmene kuwopa Mulungu kunamulimbitsira iye kupirira zilango za m’ndende, kumenyedwa, kuponyedwa miyala, kutaika posweka chombo, ngozi zosiyanasiyana za pa misewu, masiku opanda tulo, njala, ludzu, mphepo, ndi umaliseche.​—2 Akorinto 11:23-27.

Kuwopa Mulungu kunalimbitsanso Akristu oyambirira aja kuima nji m’chizunzo chowopsya pansi pa Ulamuliro wa Chiroma, pamene ngakhale ena anaponyedwa ku zirombo zolusa pa bwalo loseŵerera. Mu Nyengo Zapakati, okhulupirira olimba mtima anawotchedwa mwapoyera kufikira imfa chifukwa chakuti sanakhoze kugonjetsa chikhulupiriro chawo. Mkati mwa nkhondo yadziko yomalizira, Akristu anakonda kuvutika ndi kufa m’misasa yachibalo m’malo mwa kuchita zinthu zimene sizinakondweretse Mulungu. Kuwopa kwaumulungu kuli mphamvu yolimba chotani nanga! Motsimikizirika, ngati iko kunalimbitsa Akristu kulaka kuwopa munthu pansi pa mikhalidwe yoyesa chotero, iko kungatilimbitse ife m’mkhalidwe uliwonse umene tingadzipezemo.

Lerolino, Satana Mdyerekezi akuchita zonse zomwe angathe kutididikiza m’kusakondweretsa Mulungu. Akristu owona ayenera chotero kukhala ndi chigamulo chofananacho monga chija cholongosoledwa ndi mtumwi Paulo pamene analemba kuti: “Koma ife sindife a iwo akubwerera kuloŵa chitaiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.” (Ahebri 10:39) Kuwopa Yehova kuli magwero enieni a nyonga. Ndi thandizo lake, tiyeni “tinene molimbika mtima kuti Mthandizi wanga ndiye [Yehova, NW]; sindidzawopa; Adzandichitira chiyani munthu?”​—Ahebri 13:6.

[Chithunzi patsamba 7]

Kuwopa Mulungu kunalimbitsa Paulo kupirira zinthu zonse, kuphatikizapo kumenyedwa, kuponyedwa m’ndende, ndipo ngakhale kutaika posweka chombo.​—2 Akorinto 11:23-27

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena