Nchifukwa Ninji Tiyenera Kuwopa Mulungu?
“OPANI Mulungu mpatseni ulemerero, pakuti yafika nthaŵi ya chiŵeruzo chake.” (Chibvumbulutso 14:7) Mawu ochititsa nthumanzi amenewa anamvedwa choyamba ndi mtumwi wachikulire Yohane m’masomphenya. Onenedwa ndi mngelo wowuluka pakati pa mlengalenga, iwo analunjikitsidwa mwachindunji kwa anthu okhala mkati mwa nthaŵi ino yamapeto, nyengo yotsegulira ya “tsiku la Ambuye.”—Chibvumbulutso 1:10.
Komabe ndi mosayenerera chotani nanga mmene mawu amenewa angawonekere kwa ena! Ena amafikira pa kukaikira kukhalapo kwa Mulungu, ndipo osanena za kumuwopa iye. Kwa ambiri a awo omwe amadzinenera kukhala Akristu, lingaliro la kuwopa Mulungu limawoneka lachikale. Chikondi cha Mulungu iwo angachilandire. Koma kumuwopa iye kumawoneka kukhala kopanda pake mokulira ku Mibadwo Yapakati. Kodi mmenemu ndi mmene mumawonera nkhaniyo?
Kuwopa Mulungu kwa Yesu
Ngati ndi tero, lingalirani chomwe chimatanthauza kukhala Mkristu. Mogwirizana ndi Baibulo, kukhala Mkristu kumaphatikizapo kutsatira mosamalitsa m’mapazi a Yesu Kristu. (1 Petro 2:21) Tsopano, pamene kuli kwakuti palibe kukaikira kuti Yesu anakonda Mulungu, Baibulo limachipangitsa icho kukhala chomvekera kuti iye anamuwopanso iye. Yesaya, akumalankhula mwaulosi ponena za Yesu, ananena kuti adzakhala ndi “mzimu wa kudziŵa ndi kuwopa Yehova.” (Yesaya 11:2) Mosangalatsa, ngakhale ndi tero, kuwopa kumeneku sikunali katundu wolemetsa pa Yesu. Sitiyenera kulingalira za uko kukhala njira mu imene mwana amawopera tate wa nkhalwe kapena unyinji wa anthu osautsidwa ndi wolamulira wotsendereza. M’chenicheni, Yesaya analoseranso ponena za Yesu: “Ndipo adzakondwera nako kumuwopa Yehova.” (Yesaya 11:3) Ndimotani mmene mungasangalalire ndi kuwopa winawake?
Chenicheni chiri chakuti, m’Baibulo liwu lakuti “kuwopa” liri ndi unyinji wa matanthauzo. Pali kuwopa kwa kuthupi kapena mantha omwe timamva pamene winawake afuna kutivulaza ife. Chotero, magulu ankhondo a Chiisrayeli “anamuwopa kwambiri” Goliati. (1 Samueli 17:23, 24) Kenaka pali kuwopa kwa kudzidzimutsa kosayembekezereka kapena kosadziŵika, monga ngati mmene Zekariya anamverera pamene mwadzidzidzi anakumanizana ndi mngelo wa Yehova m’kachisi. (Luka 1:11, 12) Ngakhale kuli tero, kuwopa kumene Yesu anakumva kaamba ka Atate wake sikunali kofanana ndi kulikonse kwa uku.
M’malomwake, mawu oyambirira a Chihebri ndi Chigriki ogwiritsidwa ntchito m’Baibulo kaamba ka “kuwopa” kaŵirikaŵiri amalozera ku ulemu wakuya ndi mantha a Mulungu. Kumeneko kunali kuwopa kwaumulungu kumene Yesu anali nako ndi kumene mngelo anali kulimbikitsa aliyense kukulitsa lerolino. Mantha a ulemu amenewa, kapena kuwopa, kumayambika m’mitima mwathu pamene tisinkhasinkha pa nyonga ndi mphamvu ya Yehova ndi kulinganiza iyo ndi kuchepera kwathu kotheratu. Kumakula pamene tilingalira ntchito zake zamphamvu, ndipo kumakulitsidwanso mwakukumbukira mwa pemphero chenicheni chakuti ali Woŵeruza Wamkulu, wokhala ndi mphamvu ya kupatsa moyo limodzinso ndi kulanga ndi imfa yosatha.
Kuwopa koteroko kuli koyenerera chifukwa chakuti kumatiletsa ife kuchita choipa ndi kusatenga Mulungu mosasamala, monga momwe kunaliri. Kumatithandiza ife kupewa mkhalidwe wonga ngati: ‘Mulungu adzandikhululukira ine. Amadziŵa kuti ndine wofooka,’ pamene tiyang’anizana ndi chiyeso ndipo chotero tingalole kugonjera m’malo mwa kulimbikira. Monga momwe Miyambo 8:13 imatiuzira ife: “Kuwopa Yehova ndiko kuda zoipa.” Ndipo Miyambo 16:6 imawonjezera kuti: “Apatuka pa zoipa poopa Yehova.” Adamu ndi Hava analephera kusonyeza kwa Yehova kuwopa koyenera, kwa umoyo kumeneku pamene sanamvere iye. Chotulukapo chake? Iwo anamva kuwopa kwina, mtundu woipa ndipo anabisala kuchoka pamaso pake. Adamu ananena kuti: “Ndinamva mawu anu m’mundamu, ndipo ndinawopa.”—Genesis 3:10.
Mosiyana ndi Adamu ndi Hava, Yobu anali munthu yemwe anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova mosasamala kanthu ndi kuyesedwa kowopsya koposa. Nchifukwa ninji? Yehova iyemwini ananena kuti Yobu anali ‘munthu yemwe anamuwopa iye ndipo chotero kupewa zoipa.’ (Yobu 1:8; 2:3) Lerolino tiyenera kukhala otsimikizira kuti Yehova anganene chinthu chofananacho ponena za ife! Kuwopa Mulungu kuli koyenera, ndipo kuyenera kukhala mbali ya kulingalira kwathu.
Kuwopa Mulungu ndi Kuwopa Munthu
Kuwopa Mulungu kuli lingaliro lachibadwa lomwe limatipatsa ife mtundu umodzimodziwo wa chisungiko umene tate yemwe amauzira ulemu wakuya amapereka kwa ana ake. Kuwopa koteroko kumathandizanso kuchotsa kuwopa munthu kosakondweretsa, koipa, komwe kuli chinyengo. (Miyambo 29:25) Mmodzi yemwe sanaphunzire phunziro limeneli anali Uriya, mwana wa Semaya, yemwe analalikira m’Yerusalemu limodzi ndi Yeremiya isanafike 607 B.C.E. Mosiyana ndi Yeremiya, Uriya analola kuwopa mfumu kumutchera msampha. Iye analeka kulalikira ndi kuthaŵa pa ntchito yake. Kenaka, mfumuyo inamugwira iye ndi kumpangitsa iye kuphedwa. (Yeremiya 26:20-23) Ndimotani mmene Uriya akanapewera chotulukapo chomvetsa chisoni chimenecho? Mwa kukulitsa kuwopa Yehova komwe kunali kwamphamvupo kuposa kuwopa kwake munthu.
Yesu, pambuyo pa kuwukitsidwa kwake ndi kukwera kumwamba, anachenjeza otsatira ake kuti: “Usawope zimene uti udzamve kuwawa.” (Chibvumbulutso 2:10) Mbiri yakale imachitira chitsanzo kufunika kwa uphungu umenewo, popeza kuti Akristu—kuchokera ku mabwalo a maseŵera a Chiroma kupita ku misasa ya chibalo ya Nazi—ayang’anizana ndi mikhalidwe yowopsya. Ndimotani mmene iwo akhala okhoza kugonjetsa mantha amene adani awo ayesera kuwuzira? Mwa kugwiritsira ntchito mawu a Yesu: “Musawope iwo akupha thupi ndipo akatha ichi alibe kanthu kena angathe kuchita. Koma ndidzakulangizani amene mudziwopa: Tawopani iye amene atatha kupha ali ndi mphamvu ya kutaya ku Gehena.”—Luka 12:4, 5.
Pa Salmo 19:9 tikuphunzitsidwa kuti: “Kuwopa Yehova kuli mbe, kwakukhalabe nthaŵi zonse. Maŵeruzo a Yehova ali owona; alungama konsekonse.” Chotero palibe china chirichonse choipa ponena za kuwopa Mulungu. Kuli koyera ndi kochinjiriza ndipo kumapangitsa mtumiki wa Mulungu kukhala wamphamvu kuposa adani ake. Mofanana ndi Yesu, Mkristu amapeza chikhutiritso m’kuwopa kumeneku m’njira imodzimodzi ndi imene iye amasangalalira ndi madalitso ena onse ochokera kwa Yehova.—Yesaya 11:3.
Chotero, chiri choyenerera kotheratu kwa mngelo kufulumiza mtundu wonse wa anthu lerolino kuwopa Mulungu. Popanda kuwopa kwa umulungu koyenera, ife mothekera tikagonjera ku zisonkhezero zoipa kapena kugonjera ku kuwopa munthu. Ngati tikulitsa mtundu woyenera wa kuwopa, tidzathandizidwa kuchita mwanzeru. “Chiyambi chanzeru ndicho kuwopa Yehova.” (Miyambo 9:10; Salmo 111:10) Zowona, tiyenera kuwopa Mulungu ndi mtima wathu wonse, moyo, maganizo, ndi mphamvu. (Marko 12:30) Ndipo tiyeneranso kukhala a mantha ndi iye, kumulemekeza iye, kapena, m’mawu a mngelo, “opani Mulungu mpatseni ulemerero, pakuti yafika nthaŵi ya chiŵeruzo chake.”—Chibvumbulutso 14:7.
[Chithunzi patsamba 30]
Ngati Uriya anali ndi kuwopa kozama kwa Yehova, kuwopa munthu sikukanakhala msampha kwa iye