Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 3/15 tsamba 4-6
  • Mungakhale ndi Maubwenzi Okhalitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mungakhale ndi Maubwenzi Okhalitsa
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zitsanzo za Maubwenzi a m’Baibulo
  • Mmene Tingakulitsire Maubwenzi
  • Kusunga Ubwenzi Wosagwedera
  • Mungathe Kukhalabe ndi Mabwenzi M’dziko Lopanda Chikondi Lino
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Nchifukwa Ninji Sindimakhala ndi Mabwenzi?
    Galamukani!—1996
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yokhala Ndi Anzathu?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Muzisankha Mwanzeru Anthu Ocheza Nawo
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 3/15 tsamba 4-6

Mungakhale ndi Maubwenzi Okhalitsa

MAUBWENZI amakhala ndi zopinga. Kwenikweni, Baibulo linaneneratu kuti mu “masiku otsiriza” ano padzakhala kusoŵeka kwa chikondi, chikondi chachibadwa, ndi kukhulupirika. (2 Timoteo 3:1-5; Mateyu 24:12) Mikhalidwe imeneyi yadzetsa mliri wosayerekezereka ndi wakale uliwonse wa kusungulumwa. Munthu wina anati: “Zili ngati chingalawa cha Nowa kumene ndimakhala. Ngati suli wokwatira, sungakweremo.” Sitinganene kuti zimenezi zimachititsidwa ndi munthu aliyense wosungulumwa. M’mbali zina za dziko, zopinga maubwenzi okhalitsa zimaphazikizapo zinthu zonga kusamukasamuka kwa anthu, kusweka kwa mabanja, mizinda yopandamo chifundo ndi yaupandu, ndi kuchepa kwakukulu kwa nthaŵi yomasuka.

Munthu wa m’tauni wamakono angadziŵane ndi anthu ambiri pamlungu umodzi kuposa anthu amene munthu wa kumudzi wa m’zaka za zana la 18 anadziŵana nawo pachaka ngakhale m’nthaŵi yonse ya moyo wake! Komabe, maunansi lerolino kaŵirikaŵiri amakhala achiphamaso chabe. Ambiri amangokala ndi mayanjano ndi kungofuna kukhala ndi nthaŵi yakusanguluka. Komabe, tiyenera kuvomereza kuti kuyanjana ndi mabwenzi osayenera kuli ngati kugwiritsira ntchito minga monga nkhuni. Mlaliki 7:5, 6 amati: “Kumva chidzudzulo cha anzeru kupambana kumva nyimbo ya zitsiru. Pakuti kuseka kwa chitsiru kunga minga ilikutetheka pansi pa mphika; ichinso ndi chabe.” Minga imayaka moto woŵala ndi waphokoso kwa nthaŵi yochepa chabe, koma ilibe moto weniweni umene ungatifunditse. Mofananamo, mabwenzi omaseka mwaphokoso angaticheukitse kwakanthaŵi, koma sadzathetsa kusungulumwa konse ndi kukwaniritsa chosoŵa chathu cha mabwenzi enieni.

Kukhala wekha kumasiyana ndi kusungulumwa. Nthaŵi zina kukhala wekha kumakhala kofunika kuti tilingalire bwino kotero kuti tikhale wothandiza kwambiri monga bwenzi. Pamene ambiri ayang’anizana ndi kusungulumwa, amathamangira ku zosangulutsa zamagetsi. Kufufuza kwina kunapeza kuti chinthu chofala chimene anthu amachita akasungulumwa ndicho kuonerera wailesi yakanema. Komabe, ofufuzawo ananena kuti kuonerera wailesi yakanema kwa nthaŵi yaitali ndiko chimodzi cha zinthu zoipitsitsa zimene sitiyenera kuchita pamene tasungulumwa. Kumakulitsa kugodomala, kusukidwa, ndi kuyerekezera zinthu, kumakhala chinthu cholepheretsa kuchita zinthu ndi anthu ena.

Kwenikweni, kukhala tokha kungakhale kothandiza kwambiri ngati tigwiritsira ntchito nthaŵi yathu mwanzeru. Tingachite zimenezi mwa kuŵerenga, kulemba makalata, kupanga zinthu, ndi kupumula. Kukhala wekha kothandiza kumaphatikizapo kupemphera kwa Mulungu, kuphunzira Baibulo, ndi kusinkhasinkha pa ilo. (Salmo 63:6) Izi ndizo njira zoyandikirira kwa Yehova Mulungu, amene angakhale Bwenzi lathu lalikulu koposa.

Zitsanzo za Maubwenzi a m’Baibulo

Ngakhale kuti nkwabwino kukhala waubwenzi kwa anthu ambiri, Baibulo limatikumbutsa kuti “lilipo bwenzi lipambana ndi mbale kuumirira.” (Miyambo 18:24) Tonsefe timafunikira kukhala ndi mabwenzi apamtima angapo amene amatisamaladi, amene ubwenzi ndi iwo umatipatsa chisangalalo, nyonga, ndi mtendere. Pamene kuli kwakuti mabwenzi enieni otero angakhale osapezekapezeka lerolino, tili ndi zitsanzo zakale zapadera m’Baibulo. Mwachitsanzo, panali ubwenzi wapadera pakati pa Davide ndi Jonatani. Kodi tingaphunzirepo chiyani pa ubwenziwo? Kodi nchifukwa ninji ubwenzi wawo unakhalitsa?

Choyamba, Davide ndi Jonatani anakonda zinthu zofunika zofanana. Chofunika koposa, onse anali odzipereka mochokera pansi pamtima kwa Yehova Mulungu. Ataona chikhulupiriro cha Davide mwa Mulungu ndi zochita zake pakutetezera anthu a Yehova, “mtima wa Jonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Jonatani anamkonda iye monga moyo wa iye yekha.” (1 Samueli 18:1) Chotero, kugwirizana pakukonda Mulungu kumathandiza kumangirira mabwenzi pamodzi.

Jonatani ndi Davide anali anthu olimba amene moyo wawo unazikidwa pa mapulinsipulo aumulungu. Chotero anakhoza kulemekezana. (1 Samueli 19:1-7; 20:9-14; 24:6) Tilidi odala ngati tili ndi mabwenzi aumulungu omwe amatsogozedwa ndi mapulinsipulo a Malemba.

Palinso zinthu zina zimene zinalimbitsa ubwenzi wa Davide ndi Jonatani. Unansi wawo unali woona mtima ndi wosabisa kanthu, ndipo aliyense anali ndi chidaliro mwa mnzake. Jonatani mokhulupirika anaika maubwino a Davide patsogolo pa ake. Sanachite kaduka chifukwa chakuti Davide analonjezedwa ufumu; m’malo mwake, Jonatani anamchirikiza mwa kuthupi ndi kuuzimu. Ndipo Davide analandira chithandizo chake. (1 Samueli 23:16-18) M’njira zoyenera za Malemba, Davide ndi Jonatani anauzana malingaliro awo ponena za wina ndi mnzake. Ubwenzi wawo waumulungu unazikidwa pa kudziŵana bwino lomwe ndi kukondana. (1 Samueli 20:41; 2 Samueli 1:26) Unali wosasweka chifukwa chakuti amuna aŵiriwo anakhalabe okhulupirika kwa Mulungu. Kugwiritsira ntchito mapulinsipulo otero kungatithandize kumanga maubwenzi enieni ndi kuwasunga.

Mmene Tingakulitsire Maubwenzi

Kodi mukufunafuna mabwenzi enieni? Mwinamwake simufunikira kukafuna kutali. Pakati pa amene muonana nawo nthaŵi zonse pangapezeke mabwenzi anu, ndipo iwonso angafunikire ubwenzi wanu. Makamaka ponena za Akristu anzanu, kuli kwanzeru kugwiritsira ntchito uphungu wa mtumwi Paulo wa ‘kufutukuka.’ (2 Akorinto 6:11-13, NW) Komabe, musavutike mtima ngati kuyesayesa konse kwa kupeza bwenzi sikuchititsa unansi wozama. Kaŵirikaŵiri kumatenga nthaŵi kupanga ubwenzi, ndipo si unansi uliwonse umene ungakhale wozama mofanana. (Mlaliki 11:1, 2, 6) Ndithudi, kuti tisangalale ndi ubwenzi weniweni, tiyenera kukhala opanda dyera, ndipo tiyenera kutsatira uphungu wa Yesu wakuti: “Zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.”​—Mateyu 7:12.

Kodi ndani amene akufunikira ubwenzi wanu? Kuwonjezera pa amsinkhu wanu, bwanji za achichepere kapena achikulire? Maubwenzi a Davide ndi Jonatani, Rute ndi Naomi, ndi Paulo ndi Timoteo onse anali ndi misinkhu yosiyanasiyana. (Rute 1:16, 17; 1 Akorinto 4:17) Kodi mungafutukulire ubwenzi wanu kwa akazi amasiye ndi mbeta zina? Lingaliraninso za anthu atsopano kwanuko. Mwina anasiya anansi ochuluka kapena mabwenzi ambiri mwa kusamuka kapena mwa kusintha njira yawo ya moyo. Musayembekezere ena kukufunafunani. Ngati ndinu Mkristu, pangani maubwenzi okhalitsa mwa kugwiritsira ntchito uphungu wa Paulo wakuti: “M’chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mtsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu.”​—Aroma 12:10.

Tingalingalire za maubwenzi kukhala mtundu wina wa kupatsa. Yesu ananena kuti ngati tipatsa, anthu adzatipatsa. Ananenanso kuti muli chimwemwe chochuluka m’kupatsa kuposa chimene chili m’kulandira. (Luka 6:38; Machitidwe 20:35) Kodi mwakumanapo ndi anthu amakulidwe osiyanasiyana? Misonkhano yamitundu yonse ya Mboni za Yehova yasonyeza kuti anthu amitundu yosiyanasiyana akhoza kupalana maubwenzi enieni ndi okhalitsa pamene onse alambira Mulungu.

Kusunga Ubwenzi Wosagwedera

Mwachisoni, amene amaoneka kukhala mabwenzi nthaŵi zina amapwetekana mitima. Miseche yovulaza, kuulula zinsinsi, kusayamikira​—izi zili pakati pa zinthu zopweteka kwambiri pamene zichitidwa ndi munthu amene mwamlingalira kukhala bwenzi lenileni. Kodi mungachitenji m’mikhalidwe yoteroyo?

Perekani chitsanzo chabwino. Chitani zonse zimene mungathe kuti mupeŵe kupweteka wina kosafunikira. M’malo ena kuli kofala kwa mabwenzi kuseka zolakwa za wina. Koma kuchitirana mwaukali kapena mwachinyengo kudzalepheretsa mabwenzi kuyandikana kwambiri, ngakhale ngati akuoneka kuti ‘akuseŵera.’​—Miyambo 26:18, 19.

Yesani zolimba kusunga maubwenzi anu. Nthaŵi zina pamakhala kumvana molakwa pamene mabwenzi ayembekezera zopambanitsa kwa wina ndi mnzake. Bwenzi limene likudwala kapena lokhala ndi nkhaŵa chifukwa cha vuto lalikulu mwinamwake silingakhoze kusonyeza chisangalalo chachikulu cha masiku onse. Panthaŵi zoterozo, yesani kukhala womvetsetsa ndi wochirikiza.

Thetsani mavuto mwamsanga ndi mokoma mtima. Chitani zimenezo mwamseri ngati kuli kotheka. (Mateyu 5:23, 24; 18:15) Sonyezani kwa bwenzi lanulo kuti mukufuna kukhala naye ndi unansi wabwino. Mabwenzi oona mtima amakhululukirana. (Akolose 3:13) Kodi mudzakhala bwenzi la mtundu umenewo​—loumirira kupambana mbale?

Kuŵerenga ndi kulingalira ponena za maubwenzi kwangokhala poyambira chabe. Ngati timasungulumwa, tiyeni tichitepo kanthu koyenera ndipo sitidzakhala osungulumwa kwa nthaŵi yaitali. Ngati tilimbikira, tikhoza kupanga mabwenzi enieni. Ena a iwo tidzakhala nawo paunansi wapadera. Koma palibe amene angatenge malo a Mulungu, monga Bwenzi lalikulu koposa. Yehova yekha ndiye adziŵa bwino za ife, kutimvetsetsa, ndi kutichirikiza kwenikweni. (Salmo 139:1-4, 23, 24) Ndiponso, Mawu ake amapereka chiyembekezo chabwino kwambiri cha mtsogolo​—dziko latsopano mmene kudzakhala kotheka kukhala ndi mabwenzi enieni kosatha.​—2 Petro 3:13.

[Zithunzi patsamba 5]

Davide ndi Jonatani anali ndi ubwenzi weniweni, ifenso tikhoza kukhala nawo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena