Chizindikiro Chachiungwe cha Mbali Zambiri
Mapeto a Dziko—Kodi Ali Pafupi Motani?
NTHANO ina ya ku India imasimba za anthu akhungu asanu ndi mmodzi a ku Indostan amene anapita kukawona njovu. Woyamba anakhudza m’mbali mwake nafuula kuti: “Kalanga ine! njovu njofanana ndi chipupa!” Wachiŵiri anakhudza mnyanga wake nati: “Njovu njofanana ndi mkondo!” Wachitatu anakhudza chitamba chake nati: “Njovu njofanana ndi njoka!” Wachinayi ananyanyamphira nakhudza bondo lake nati: “Nkowonekeratu kuti njovu njofanana ndi mtengo!” Wachisanu anakhudza khutu lake nati: “Njovu yodabwitsayi njofanana ndi chokupizira mphepo!” Wachisanu ndi mmodzi anagwira mchira wake nati: “Aha, njovu njofanana ndi chingwe!” Akhungu asanu ndi mmodziwo anakangana kwanthaŵi yaitali ndipo mwamphamvu ponena za mawonekedwe a njovu, koma palibe amene anapereka malongosoledwe olondola. Chidziŵitso chosakwaniracho sichinapereke chithunzi chokwanira.
Vuto lofananalo limabuka pozindikira chizindikiro cha kubweranso kwa Kristu. Poyankha funso la ophunzira ake lakuti: “Chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?” Yesu anayankha kuti: “Mtundu wa anthu udzaukira pa mtundu wina, ndipo ufumu pa ufumu wina: ndipo kudzakhala zivomezi zazikulu, ndi njala ndi miliri m’malo akutiakuti.” (Mateyu 24:3; Luka 21:10, 11) Koma ngati zinthu zokhazi zitchulidwa monga umboni wa kubweranso kwa Kristu mu 1914, anthu amatsutsa kuti: “Takhala tikuwona nkhondo, njala, miliri, ndi zivomezi!” Ndipo amanena zowona.
Zinthu zoŵerengeka zimenezi—ngakhale kuti zimapangitsa chipsinjo chosayerekezeka—sizili zokwanira kwa anthu ambiri kuzindikiritsa kubweranso kwa Kristu; zambiri zimafunikira kuti chizindikirocho chikhale chokwanira, chosakaikirika. Pamene zilengezo zakuti mapeto adziko ayandikira ziperekedwa pa umboni wosakwanira, pa mbali imodzi yokha kapena zoŵerengeka za chizindikiro chimene chimawonedwa, machenjezo abodza ndiwo amakhala zotulukapo zake. Zofunika ndimbali zonse zimene Yesu anapereka zokhudza kubweranso kwake, osati imodzi yokha kapena zoŵerengeka. Chimene iye anapereka kuzindikiritsa kukhalapo kwake chinali chizindikiro chachiungwe, chokhala ndi mbali zokwanira kutsimikiziritsa chizindikirocho, chophatikiza mbali zosiyanasiyana, zimene zitaikidwa pamodzi, zimakhala zosakaikirika.
Monga chitsanzo cha chizindikiro chachiungwe, talingalirani chimene chaperekedwa m’Baibulo kuzindikiritsa Yesu monga Mesiya pakubwera kwake koyamba. Chinaphatikizapo zochitika zambiri zokhudza Mesiya zimene zinaperekedwa m’Malemba Achihebri. Yesu anauza ophunzira ake ponena za ena amalemba ameneŵa, koma iwo sanamvetsetse tanthauzo lawo. Ophunzirawo, mofanana ndi Ayuda onse, anafuna Mesiya amene akagwetsa ulamuliro wa Roma ndi kulamulira dziko pamodzi nawo monga atsamwali ake. Chotero pamene anafa, iwo anasokonezeka maganizo ndi kukhwethemuka. Yesu ataukitsidwa, anakumana nawo nati: “Awa ndi mawuwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za ine m’chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi masalmo. Ndipo anawatsegulira mitima yawo, kuti adziŵitse malembo.”—Luka 24:44, 45.
Malinga ndi matembenuzidwe a Kingdom Interlinear a vesi 45, Yesu anachita zimenezi “mwakugwirizanitsa Malemba” kuchokera ku mbali ya Chihebri ya Baibulo imene inaneneratu za zochitika ndi mikhalidwe ya moyo wa Mesiya wolonjezedwayo amene anali nkudza, ndipo anawaika pambali pa zochitika za moyo wa Yesu zimene zinawakwaniritsa. Pambuyo pake, mtumwi Paulo anagwiritsira ntchito njira imodzimodziyi pamene ‘anatanthauzira, natsimikiza’ kuti Yesu anali Mesiyayo. (Machitidwe 17:3) Kachiŵirinso, Kingdom Interlinear ndiyo imamveketsa dongosolo limenelo mwakunena kuti anachita tero “mwakutsegula mokwanira ndi kuika kumbali kwa” maulosi Aumesiya a m’Malemba Achihebri zochitika za moyo wa Yesu zimene zinawakwaniritsa. Bokosilo limapereka umboni wa ambiri a maulosi Achihebri ameneŵa amene anakwaniritsidwa ndi zochitika za moyo wa Yesu zimene zimatsimikizira kuti anali Mesiya wonenedweratuyo. Limasonyeza chimene chimapanga chizindikiro chachiungwe.
Chizindikiro Chachiungwe cha Kukhalapo kwa Kristu
Chizindikiro chachiungwe chimenecho ndicho chimazindikiritsa nthaŵi ya kubweranso kwa Yesu, kapena, molongosoka kwenikweni, kukhalapo kwake. Liwu Lachigiriki lakuti pa·rou·siʹa limene matembenuzidwe ambiri amalimasulira kukhala “kudza” pa Mateyu 24:3 silimatanthauza nthaŵi pamene iye akabwera kapena kufika koma limatanthauza kuti iye anafika kale, alipo. M’nkhani ya Yesu kumatanthauza kuti iye alipo mosawoneka monga Mfumu yoikidwa pampando wachifumu ya Yehova ndipo akulamulira ali kumwamba. Zimenezi zimagwirizana ndi ndemanga ya Yesu pa Yohane 14:19 yakuti: “Katsala kanthaŵi, ndipo dziko lapansi silindiwonanso ine.” Popeza kuti sakawoneka mwakuthupi, iye anapereka chizindikiro chimene chikasonyeza kubweranso kwake ndi kukhalapo kwake kosawoneka monga Mfumu yolamulira ya Yehova.
Chizindikiro chimene anapereka sichinali cha mbali imodzi yokha kapena mbali zoŵerengeka zokha. Chinali ndi mbali zambiri zomwe zinafunikira kuikidwa pamodzi monga chizindikiro chachiungwe, monga momwe zinaliri ndi chizindikiro chachiungwe panthaŵi ya kubwera kwake koyamba monga Mesiya. Chotero, pokhala ndi mbali zambiri kapena zochitika, iye akuzindikiritsa mosakaikirika kukhalapo kwake kosawoneka panthaŵi ino monga Mfumu yolamulira ya Yehova yokhala pampando wachifumu kumwamba koma akufutukulira mphamvu zake ndi chisonkhezero ku zochitika za padziko lapansi. Machenjezo abodza ambiri angachitike pamene mbali imodzi kapena ziŵiri zokha zagogomezeredwa, m’malo mwa mbali zambiri zimene zimapanga chizindikiro chachiungwecho. Nkofanana ndi akhungu asanu ndi mmodzi a ku Indostan aja, amene aliyense wa iwo anapereka chigamulo cholakwika chifukwa chokhudza mbali imodzi yokha ya thupi la njovu.
Kukwaniritsidwa kwa chizindikiro chachiungwe choperekedwa ndi Yesu chimenechi, kuphatikizapo mikhalidwe ina yowonjezereka yoperekedwa ndi atumwi atatu, zinayamba mwapadera mu 1914 kumka mtsogolo. Zotsatirazi ndizo chidule cha mbali zosiyanasiyana zimenezi limodzi ndi kukwaniritsidwa kwawo.
“Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina.” (Mateyu 24:7) Nkhondo Yadziko I inayamba mu 1914 ndi maiko 28 oloŵetsedwamo, anthu 14 miliyoni anaphedwa. Nkhondo Yadziko II inatsatira ndi maiko 59 oloŵetsedwamo, ndipo anthu 50 miliyoni anaphedwa.
“Miliri m’malo akutiakuti.” (Luka 21:11) Pamene Nkhondo Yadziko I inatha, anthu 21 miliyoni anaphedwa ndi flu Yachispanya. Chiyambire pamenepo, matenda a mtima, kansa, AIDS, ndi miliri ina yapha anthu mamiliyoni mazana ambiri.
“Kudzakhala njala.” (Mateyu 24:7) Njala yowopsa kwambiri m’mbiri yonse inakantha pambuyo pa Nkhondo Yadziko I. Njala ina yowopsa inadza pambuyo pa Nkhondo Yadziko II, ndipo tsopano manyutirishoni ikuyambukira mbali imodzi mwa zisanu za anthu okhala m’dziko. Chaka ndi chaka, pafupifupi ana 14 miliyoni amafa ndi manyutirishoni.
“Kudzakhala zivomezi zazikulu.” (Luka 21:11) Talingalirani za zivomezi zazikulu zoŵerengeka zimene zinachitika itapita 1914. Mu 1915, ku Italy, anthu 32,610 anafa; 1920, ku China, anthu 200,000 anafa; 1923, ku Japan, 143,000 anafa; 1939, ku Turkey, 32,700 anafa; 1970, ku Peru, 66,800 anafa; 1976, ku China, 240,000 (ena amati 800,000) anafa; 1988, ku Armenia, 25,000 anafa.
“Kuchuluka kwa kusayeruzika.” (Mateyu 24:12) Kusayeruzika kwachuluka chiyambire 1914; lerolino kukuwonjezeka mofulumira. Mbanda, kugwirira chigololo, kuba, kukangana kwatimagulu—ndizo mitu yankhani yochuluka m’manyuzipepala ndi nkhani zoulutsidwa. Atsogoleri andale zadziko amabera unyinji, achichepere amanyamula mfuti ndi kupha, ana asukulu amaukirana. M’madera ambiri kumakhala kowopsa kuyenda m’makwalala ngakhale masana.
“Chisauko cha mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru . . . anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zilinkudza ku dziko lapansi.” (Luka 21:25, 26) Upandu, chiwawa, kumwerekera ndi mankhwala ogodomalitsa, kusweka kwamabanja, kusakhazikika kwachuma, ulova—ndandandayo njaitali ndipo ikuwonjezereka. Wasayansi wina wotchuka analemba kuti: “Tidzadya mantha, kugona m’mantha, kukhala m’mantha ndi kufa m’mantha.”
“Masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa.” (2 Timoteo 3:1) Mtumwi Paulo analankhula za anthu kukhala ‘osazindikiranso kanthu konse.’ (Aefeso 4:19) Komabe, iye anafotokoza kusweka kwa makhalidwe kumene ananeneratu kwa “masiku otsiriza.” Zimamveka ngati nkhani zoulutsidwa masiku ano: “Koma zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nawo mawonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.”—2 Timoteo 3:1-5.
“Masiku otsiriza adzafika onyoza.” (2 Petro 3:3) Manyuzipepala, nkhani zoulutsidwa, magazini, mabuku, ndi akanema amatsutsa monyoza Baibulo ndi kuliloŵa m’malo ndi nthanthi zawo zaumunthu, akumanena monga momwe ananeneratu Petro kuti: “Lili kuti lonjezano la kudza kwake? pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe.”—2 Petro 3:4.
“Anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani.” (Luka 21:12) Kuyambira mu 1914 mpaka zaka zonsezi, zikwi za Mboni za Yehova zamangidwa mwakhalwe, kupatsidwa milandu yabodza, kumenyedwa, ndi kuponyedwa m’misasa yachibalo ya Hitler, kumene anazunzidwa, ambiri anaphedwa, ena anaphedwa mwankhalwe mwakudulidwa mutu. M’maiko ena, ponse paŵiri opondereza ufulu ndi ademokrase, ntchito yawo yochitira umboni Yehova ndi Ufumu wake inaletsedwa ndipo Mboni zinaponyedwa m’ndende. Zonsezi zikukwaniritsa mawu a Yesu onena za masiku otsiriza.—Mateyu 5:11, 12; 24:9; Luka 21:12; 1 Petro 4:12, 13.
“Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu.” (Mateyu 24:14, NW) Mbiri yabwino yachiyani? Mbiri yabwino ya Ufumu wolamulira kumwamba wa Kristu, popeza limenelo ndifunso limene Yesu anafunsidwa limene linatulutsa ulosi wake wonena za chizindikiro chachiungwe cha chochitikacho. Mbiriyo yalalikidwa ndi Mboni za Yehova chiyambire 1914. Zikwi zinayi zinali kuchita ntchitoyo mu 1919, oposa mamiliyoni anayi pofika 1990, ndipo mu 1992 m’mwezi umodzi anali okwanira 4,472,787. Mabuku ofotokoza Baibulo anagaŵiridwa m’zinenero 200 m’maiko 229. Palibe ndi kale lonse pamene mbali imeneyi ya chizindikiro chachiungwe inakwaniritsidwa.
“Kuwononga iwo akuwononga dziko.” (Chivumbulutso 11:18) Nthaŵi zonse anthu aumbombo akhala ofunitsitsa kuwononga dziko chifukwa cha phindu ladyera, koma kulibe mbadwo wina kumbuyoko umene unali ndi mphamvu zakuwononga zimenezo. Tsopano, kuyambira 1914, luso lazopangapanga lamakono lawapatsa mphamvu zimenezo, ndipo akuzigwiritsira ntchito molakwa. Iwo akuwononga dziko.
Nazi zoŵerengeka za nkhalwe zotulukapo: mvula ya acid, kutentha kwa dziko, mbereŵere za m’muyalo wa ozone, mankhwala ophera tizilombo owopsa, zapadzala zaululu, kuunjikana kwa zinyalala, zotaidwa za nyukliya, kutaikira kwa mafuta, kutaya zonyansa zosakonzedwa ndi mankhwala, nyanja zopanda zamoyo, nkhalango zowonongedwa, madzi apansi panthaka oipitsidwa, zinyama zoikidwa paupandu, kuwonongedwa kwa umoyo wa anthu.
Wasayansi Barry Commoner anati: “Ndikhulupirira kuti kuipitsidwa kopitirizabe kwa dziko lapansi, ngati sikuletsedwa, kudzawononga kuthekera kwa pulaneti lino kukhala malo a moyo wa anthu. . . . Vuto sindilo umbuli wa zasayansi, koma umbombo wadala.” State of the World 1987 imati: “Ukulu wa zochita za anthu wayamba kuwopseza kukhalika kwa dziko lapansi lenilenilo.” Mpambo wa pa wailesi yakanema woulutsidwa mu 1990 unali ndi mutu wosangalatsa wakuti “Race to Save the Planet” (Mpikisano Wakupulumutsa Pulaneti).
Zochitika zambiri zimenezi zitaikidwa pamodzi monga chizindikiro chimodzi mkati mwa mbadwo umodzi sizingakanidwe kukhala zongochitika mwadzidzidzi. Ukulu wawo umawonjezera umboni wake. Ndipo pali zina za zochitika zimenezi, monga ngati kulalikidwa kwapadziko lonse kwa uthenga umenewu wa mbiri yabwino ndi kuwonongedwa kwa dziko, zimene sizinachitikepo kuyambira chilengedwe. Chizindikiro chachiungwe cha kukhalapo kwa Kristu Yesu nchokhutiritsa.
“Ngati munthu ali nawo makutu akumva, amve.”—Marko 4:23.
[Bokosi patsamba 22]
Umboni Wachiungwe wa Kubwera Koyamba kwa Yesu Monga Mesiya
Anabadwira M’fuko La Yuda (Genesis 49:10); Anadedwa, Kuperekedwa Ndi Mmodzi Wa Atumwi Ake; Akachita Maere Pa Zovala Zake; Kupatsidwa Vinyo Wa Mure; Kutonzedwa Pamtengo Wozunzirapo; Fupa Lake Silikathyoledwa; Sanawone Chivundi; Anaukitsidwa (Salmo 69:4; 41:9; 22:18; 69:21; 22:7, 8; 34:20; 16:10); Akabadwa Kwa Namwali; Banja La Davide; Akakhala Mwala Wokhumudwitsa; Anakanidwa; Anali Du Pamaso Pa Omzenga Mlandu; Ananyamula Nthenda Za Anthu; Anaŵerengeredwa Ndi Ochimwa; Imfa Yansembe; Kulasidwa M’nthiti; Anaikidwa M’manda Ndi Olemera (Yesaya 7:14; 11:10; 8:14, 15; 53:3; 53:7; 53:4; 53:12; 53:5; 53:9); Anaitanidwa Kuchoka Ku Igupto (Hoseya 11:1); Anabadwira Ku Betelehemu (Mika 5:2); Anaperekedwa Monga Mfumu; Anakwera Pa Bulu; Anaperekedwa Ndi Ndalama 30 Zasiliva; Otsatira Ake Anabalalitsidwa.—Zekariya 9:9; 11:12; 13:7.
[Bokosi patsamba 23]
Chizindikiro Chachiungwe cha Kukhalapo Kwaufumu kwa Yesu pa Kubweranso Kwake
Nkhondo Yadziko; Njala; Miliri; Zivomezi (Mateyu 24:7; Luka 21:10, 11; Chivumbulutso 6:1-8); Kuchuluka Kwa Kusayeruzika; Kupereka Ndi Kudana Wina Ndi Mnzake; Kusamvera Makolo; Kupanda Chikondi Chachibadwidwe; Kusadziletsa; Kusayanjanitsika; Okonda Ndalama; Kukonda Zokondweretsa Koposa Mulungu; Kukhala Ndi Mawonekedwe Achipembedzo Koma Kuikana Mphamvu Yake; Amwano; Aukali; Kuzunza Otsatira A Kristu; Kupereka Otsatira Ku Mabwalo Amilandu, Ndi Kupha Otsatira A Kristu (Mateyu 24:9, 10, 12; Luka 21:12; 2 Timoteo 3:1-5); Onyoza Kukhalapo Kwa Yesu; Namanena Kuti Zinthu Zonse Zikupitiriza Kuyambira Pa Chilengedwe (2 Petro 3:3, 4); Owononga Malo A Dziko Lapansi.—Chivumbulutso 11:18.