“Yehova Sadzasiya Anthu Ake”
“Masautso a wolungama mtima achuluka: koma Yehova amlanditsa mwa onsewa.”—SALMO 34:19.
1, 2. (a) Kodi Yehova akuwadalitsa motani anthu ake lerolino? (b) Kodi Akristu ambiri akuyang’anizana ndi chiyani, ndipo pamabuka mafunso otani?
MOGWIRIZANA ndi ulosi wa Baibulo, olambira a Yehova akukhala m’paradaiso wauzimu. (2 Akorinto 12:1-4) Mboni za Yehova zili paubale wa padziko lonse wodziŵika chifukwa cha chikondi chawo ndi umodzi. (Yohane 13:35) Izo zili ndi chidziŵitso chakuya ndipo chokwana bwino cha choonadi cha Baibulo. (Yesaya 54:13) Zimayamikira chotani nanga Yehova kuti akuzipatsa mwaŵi wokhala m’hema wake wauzimu!—Salmo 15:1.
2 Pamene kuli kwakuti onse m’gulu la Yehova akusangalala ndi kulemera kwauzimu, ena amaoneka kuti aliko pamtendere pamene kuli kwakuti ena ali m’mavuto osiyanasiyana. Akristu ambiri amakhala mumkhalidwe womvetsa chisoni nthaŵi yaitali opanda chiyembekezo cha mpumulo uliwonse wamwamsanga. Mwachibadwa, iwo amalefulidwa m’mikhalidwe imeneyi. (Miyambo 13:12) Kodi masoka ali umboni wakuti Mulungu sakukondwera nawo? Kodi Yehova akupereka chitetezo chapadera kwa Akristu ena koma nkusiya ena?
3. (a) Kodi Yehova ndiye akuchititsa nsautso za anthu ake? (b) Kodi nchifukwa ninji ngakhale olambira okhulupirika a Yehova amakhala ndi mavuto aumunthu?
3 Baibulo limayankha kuti: “Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu.” (Yakobo 1:13) Yehova ndiye Wotetezera ndi Wochirikiza anthu ake. (Salmo 91:2-6) “Yehova sadzasiya anthu ake.” (Salmo 94:14) Zimenezi sizikutanthauza kuti olambira okhulupirika sadzavutika. Dongosolo la dziko la zinthu lilipoli likulamulidwa ndi anthu opanda ungwiro mwachibadwa. Ambiri ngokhota maganizo, ndipo angapo ngoipiratu. Palibe aliyense wa iwo amene akufuna kupeza nzeru kuchokera kwa Yehova. Izi zimachititsa mavuto ambiri a anthu. Baibulo limanena momveka kuti si nthaŵi zonse kuti anthu a Yehova angapeŵe zotsatirapo zomvetsa chisoni za kupanda ungwiro ndi kuipa kwa anthu.—Machitidwe 14:22.
Akristu Okhulupirika Amadziŵa Kuti Adzavutika
4. Kodi Akristu onse ayenera kuyembekezera chiyani malinga ngati akukhala m’donsogolo loipali la zinthu, ndipo nchifukwa ninji?
4 Ngakhale saali mbali ya dziko, otsatira a Yesu akukhala pakati pa dongosololi la zinthu. (Yohane 17:15, 16) Baibulo limamvumbula Satana kuti ndiye mphamvu yolamulira dziko lonse lino. (1 Yohane 5:19) Ndiye chifukwa chake Akristu onse amadziŵa kuti nthaŵi iliyonse akhoza kukumana ndi mavuto aakulu. Poganizira zimenezo, mtumwi Petro akuti: “Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu Mdyerekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire; ameneyo mumkanize okhazikika m’chikhulupiriro, podziŵa kuti zoŵaŵa zomwezo zilimkukwaniridwa pa abale anu ali m’dziko.” (1 Petro 5:8, 9) Inde, gulu lonse la Akristu limayembekeza kuvutika.
5. Kodi Yesu anafotokoza bwino motani kuti Akristu okhulupirika adzakhala ndi zinthu zomvetsa chisoni m’moyo?
5 Ngakhale timamkonda kwambiri Yehova ndipo ndife okhulupirika pamapulinsipulo ake, tidzakhala ndi zinthu zochititsa chisoni m’moyo. Yesu anazifotokoza bwino zimenezi m’fanizo lake lolembedwa pa Mateyu 7:24-27, pamene anasonyeza kusiyana kwa awo amene amamvera mawu ake ndi awo amene samawamvera. Anayerekezera ophunzira omvera ndi munthu wochenjera amene wamanga nyumba yake pathanthwe. Awo amene samvera mawu ake anawayerekezera ndi munthu wopusa amene wamanga nyumba yake pamchenga. Mkuntho waukulu utawomba, nyumba ija yomangidwa pathanthwe ndiyo imene inapulumuka. Ponena za nyumba ya munthu wanzeru, taonani kuti “inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinawomba mphepo, zinagunda panyumbayo; koma siinagwa.” Yesu sanalonjeze kuti munthu wochenjerayo adzangokhala pamtendere ndi bata nthaŵi zonse. M’malo mwake, kuchenjera kwa munthuyo kudzamkonzekeretsa kulimbana ndi mkuntho. Ndilo lingaliro limene likuperekedwanso ndi fanizo la wofesa mbewu. M’fanizolo Yesu akufotokoza kuti ngakhale olambira omvera ‘a mtima woona ndi wabwino, adzabala zipatso ndi kupirira.’—Luka 8:4-15.
6. M’fanizo la Paulo la zinthu zosatha kunyeka ndi moto, kodi ndani amayesedwa m’mayesero onga moto?
6 Polembera Akorinto, mtumwi Paulo anagwiritsira ntchito mafotokozedwe ophiphiritsa kuti asonyeze kuti mikhalidwe yolimba imene ingatithandize kupirira mayesero ndi yofunika. Zinthu zosatha kunyeka ndi moto zimenezi monga golide, siliva, ndi miyala ya mtengo wake zimaimira mikhalidwe yaumulungu. (Yerekezerani ndi Miyambo 3:13-15; 1 Petro 1:6, 7.) Komabe, mikhalidwe yakuthupi anaiyerekezera ndi zinthu zotha kunyeka ndi moto. Ndiyeno Paulo akuti: “Ntchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbuluka m’moto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani. Ngati ntchito ya munthu aliyense ikhala imene anaimangako, adzalandira mphotho.” (1 Akorinto 3:10-14) Panonso, Baibulo likufotokoza kuti tonsefe mpaka tidzakhala ndi mtundu winawake wa mayesero onga moto.
7. Malinga ndi Aroma 15:4, kodi Malemba angatithandize motani kupirira mayesero?
7 Muli nkhani zambiri m’Baibulo za atumiki okhulupirika a Mulungu amene anapirira masoka, nthaŵi zina kwa nthaŵi yaitali. Komabe, Yehova sanawasiye. Mtumwi Paulo ayenera kuti ankaganiza zitsanzo zimenezi pamene anati: “Zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.” (Aroma 15:4) Talingalirani zitsanzo za anthu atatu amene anavutika ndi masoka ngakhale anali mu unansi wapafupi ndi Mulungu.
Zimene Timaphunzira Pankhani za m’Baibulo
8. Kodi Yehova analola zotani kumchitikira Yosefe, ndipo kwautali wotani?
8 Yosefe mwana wa Yakobo anayanjidwa ndi Yehova kuyambira paubwana. Komabe, popanda kulakwitsa kalikonse, anavutika ndi masoka otsatizana. Anabedwa ndi kuzunzidwa ndi abale ake. Anamgulitsa monga kapolo kudziko lachilendo kumene anamnamizira ndi kumuika “m’dzenje.” (Genesis 40:15) Mmenemo “anapweteka miyendo yake ndi matangadza; anamgoneka mu unyolo.” (Salmo 105:17, 18) Mu ukapolo wake ndi ukaidi, mosakayikira Yosefe anapempha Yehova mobwerezabwereza kuti ammasule. Komabe, pafupifupi zaka 13, ngakhale kuti Yehova anamlimbitsa m’njira zosiyanasiyana, anakhalabe kapolo kapena mkaidi masiku onsewo.—Genesis 37:2; 41:46.
9. Kodi Davide anapiriranji zaka zingapo?
9 Ndi mmenenso zinalili ndi Davide. Pamene Yehova anali kusankha munthu woyenera kulamulira Israyeli, anati: “Ndapeza Davide, mwana wa Jese, munthu wa pamtima panga.” (Machitidwe 13:22) Ngakhale anayanjidwa ndi Yehova, Davide anavutika kwambiri. Poopa kufa, anabisala zaka zingapo m’chipululu, m’mapanga, m’mindala, ndi m’dziko la eni. Posakidwa monga nyama yakuthengo, analefulidwa ndi kuvutika ndi mantha. Komabe, anapirira m’mphamvu ya Yehova. Pazimene anakumana nazo Davide ananena moona kuti: “Masautso a wolungama mtima achuluka: koma Yehova amlanditsa mwa onsewa.”—Salmo 34:19.
10. Kodi ndi tsoka lalikulu lotani limene linagwera Naboti ndi banja lake?
10 M’tsiku la mneneri Eliya, kunali 7,000 okha m’Israyeli amene sanagwadire Baala mulungu wonyenga. (1 Mafumu 19:18; Aroma 11:4) Naboti, amene ayenera kuti anali mmodzi wa iwo, anachitidwa chisalungamo choopsa. Iye anavutika ndi chinenezo chakuti wachita mwano. Atampeza ndi mlandu, mfumu inamweruza kuti afe mwa kumponya miyala, ndipo agalu ananyambita mwazi wake. Ngakhale ana ake anaphedwa! Komabe, chinenezocho chinali chabodza. Mboni zomtsutsa zinali zonyenga. Chochitika chonsecho chinali chiŵembu cha Mfumukazi Yezebeli kuti mfumu itenge munda wampesa wa Naboti.—1 Mafumu 21:1-19; 2 Mafumu 9:26.
11. Kodi mtumwi Paulo akutiuzanji ponena za amuna ndi akazi a m’mbiri ya Baibulo?
11 Yosefe, Davide, ndi Naboti ndi atatu chabe mwa amuna ndi akazi ambiri okhulupirika otchulidwa m’Baibulo amene anavutika ndi masoka. Mtumwi Paulo analemba mbiri yopenda atumiki a Yehova m’mibadwo yonseyo. Mmenemo ananena za awo amene “anayesedwa ndi matonzo ndi zokwapulira, ndiponso nsinga, ndi kuwatsekera m’ndende; anaponyedwa miyala, anachekedwa pakati, anayesedwa, anaphedwa ndi lupanga, anayendayenda ovala zikopa zankhosa, ndi zikopa zambuzi, nakhala osoŵa, osautsidwa, ochitidwa zoipa, (amenewo dziko lapansi silinayenera iwo), osokerera m’mapululu, ndi m’mapiri, ndi m’mapanga, ndi m’mauna a dziko.” (Ahebri 11:36-38) Koma Yehova sanawasiye.
Yehova Amasamalira Ovutika
12. Kodi ndi mavuto ena ati amene Mboni za Yehova zimakumana nawo lerolino?
12 Bwanji nanga za anthu a Yehova lerolino? Monga gulu, tingadalire chitetezo cha Mulungu ndi kupulumuka masiku otsiriza ndi chisautso chachikulu. (Yesaya 54:17; Chivumbulutso 7:9-17) Komabe, aliyense payekha, timadziŵa kuti “nthaŵi ndi zochitika zosadziŵika” zimagwera anthu onse. (Mlaliki 9:11, NW) Lerolino pali Akristu ambiri okhulupirika amene akuvutika ndi masoka. Ena akupirira umphaŵi wadzaoneni. Baibulo limanena za “ana amasiye ndi akazi amasiye” achikristu amene ali mu nsautso. (Yakobo 1:27) Ena amavutika chifukwa cha masoka achilengedwe, nkhondo, upandu, kugwiritsira ntchito ulamuliro molakwa, kudwala, ndi imfa.
13. Kodi ndi mavuto ena ati amene achitiridwa lipoti?
13 Mwachitsanzo, maofesi a nthambi a Watch Tower m’malipoti awo a 1996 opita ku Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova anasimba kuti abale ndi alongo athu ena akuvutika kwadzaoneni m’ndende chifukwa chomamatira ku mapulinsipulo a Baibulo. Mipingo itatu m’dziko lina la ku South America inapasuka magulu a zigaŵenga atakakamiza Mboni mazana ambiri kuchoka kumalowo. M’dziko lina la ku West Africa, Mboni zina zimene zinatsekeredwa pakati pa omenyana m’nkhondo yachiŵeniŵeni zinaphedwa. M’dziko lina la ku Central America, kusoŵa kwa ndalama kwakukulu kale kwa abale ena kunanyanyirako mkuntho utasakaza malowo. Kumalo ena kumene mwina kulibe kwambiri umphaŵi ndi njala, zinthu zina zoipa zingathetse chimwemwe cha ena. Ena amalemedwa ndi mavuto a moyo wamakono. Chifukwa cha mphwayi ya anthu, enanso angalefulidwe polalikira uthenga wabwino wa Ufumu.
14. (a) Kodi chitsanzo cha Yobu chikutiphunzitsanji? (b) M’malo moganiza zoipa, kodi tiyenera kuchitanji titapsinjika mtima?
14 Sitiyenera kuona mikhalidwe imeneyi monga umboni wakuti Mulungu sakukondwera nafe. Kumbukirani nkhani ya Yobu ndi masoka ambiri amene anavutika nawo. Anali “munthu wangwiro ndi woongoka.” (Yobu 1:8) Yobu ayenera kuti analefulidwa chotani nanga Elifazi atamuuza kuti pali zina zimene analakwa! (Yobu, machaputala 4, 5, 22) Sitiyenera kuthamangira kunena kuti tikuvutika ndi masoka chifukwa chakuti sitinamkondweretse Yehova pazinthu zina kapena chifukwa chakuti Yehova wachotsa dalitso lake. Kuganiza zoipa pamene tili mu nsautso kungafooketse chikhulupiriro chathu. (1 Atesalonika 3:1-3, 5) Titapsinjika mtima, kuli bwino kusinkhasinkha za choonadi chakuti Yehova ndi Yesu ali pafupi ndi olungama kaya kuchitike zotani.
15. Kodi timadziŵa motani kuti Yehova amasamala zedi za masoka a anthu ake?
15 Mtumwi Paulo akutitsimikizanso pamene akuti: “Adzatisiyanitsa ndani ndi chikondi cha Kristu? Nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiwa, kapena zoopsa kapena lupanga kodi? . . . Ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 8:35, 38, 39) Yehova akusamala zedi za ife ndipo akudziŵa bwino lomwe za kuvutika kwathu. Pamene anali wothaŵa kwawo, Davide analemba kuti: “Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake achereza kulira kwawo. Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka.” (Salmo 34:15, 18; Mateyu 18:6, 14) Atate wathu wakumwamba amatisamalira ndipo ovutika amawamvera chisoni. (1 Petro 5:6, 7) Amatipatsa zimene tifunika kuti tipirire, kaya tivutike motani.
Mphatso za Yehova Zimatichirikiza
16. Kodi nchogaŵira chotani cha Yehova chimene chimatithandiza kupirira, ndipo motani?
16 Ngakhale sitingayembekezere kukhala ndi moyo wopanda nsautso m’dongosolo la zinthu lino lakale, ‘sititayika.’ (2 Akorinto 4:8, 9) Yesu analonjeza kuti otsatira ake adzawapatsa mthandizi. Iye anati: “Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe ina, kuti akhale ndi inu ku nthaŵi yonse, ndiye Mzimu wa choonadi.” (Yohane 14:16, 17) Pa Pentekoste wa 33 C.E., mtumwi Petro anauza omvetsera ake kuti angalandire “mphatso ya Mzimu Woyera.” (Machitidwe 2:38) Kodi mzimu woyera ukutithandiza lerolino? Inde! Mphamvu yogwira ntchito ya Yehova imatipatsa zipatso zabwino kwambiri: “Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.” (Agalatiya 5:22, 23) Yonseyi ndi mikhalidwe yabwino kopambana imene imatithandiza kupirira.
17. Kodi ndi choonadi china chotani cha m’Baibulo chimene chimalimbitsa chikhulupiriro chathu ndi kutsimikiza mtima kwathu kuti tidzayembekeza pa Yehova modekha?
17 Mzimu woyera umatithandizanso kumvetsa kuti nsautso zilipozi ndi ‘zopepuka ndi zakanthaŵi’ titaziyerekezera ndi mphotho ya moyo wosatha. (2 Akorinto 4:16-18) Timakhulupirira zedi kuti Mulungu sadzaiŵala ntchito zathu ndi chikondi chimene timamsonyeza. (Ahebri 6:9-12) Poŵerenga mawu ouziridwa a Baibulo, timatonthozedwa ndi zitsanzo za atumiki okhulupirika akale amene anapirira masoka ambiri koma amene ananenedwa kukhala achimwemwe. Yakobo akulemba kuti: “Tengani, abale, chitsanzo cha kumva zoŵaŵa ndi kuleza mtima, aneneri amene analankhula m’dzina la Ambuye. Taonani tiwayesera odala opirirawo.” (Yakobo 5:10, 11) Baibulo limatilonjeza “mphamvu yoposa yachibadwa” yotithandiza kupirira mayesero. Ndiponso Yehova amatidalitsa ndi chiyembekezo cha chiukiriro. (2 Akorinto 1:8-10; 4:7, NW) Mwa kuŵerenga Baibulo masiku onse ndi kusinkhasinkha za malonjezo ameneŵa, tidzalimbitsa chikhulupiriro chathu ndi kutsimikiza mtima kwathu kuti tidzayembekeza kwa Mulungu modekha.—Salmo 42:5.
18. (a) Pa 2 Akorinto 1:3, 4, kodi tikulimbikitsidwa kuchitanji? (b) Kodi oyang’anira achikristu angakhale motani otonthoza ndi otsitsimula?
18 Ndiponso, Yehova watipatsa paradaiso wauzimu mmene tikusangalala ndi chikondi chenicheni cha abale ndi alongo athu achikristu. Tonsefe tili ndi mbali yoichita pa kutonthozana wina ndi mnzake. (2 Akorinto 1:3, 4) Makamaka oyang’anira achikristu angakhale otonthoza ndi otsitsimula kwambiri. (Yesaya 32:2) Pokhala “mphatso mwa amuna,” iwo atumidwa kumangirira ovutika, ‘kulimbikitsa amantha mtima,’ ndi ‘kuchirikiza ofooka.’ (Aefeso 4:8, 11, 12, NW; 1 Atesalonika 5:14) Akulu akulimbikitsidwa kugwiritsira ntchito bwino magazini ya Nsanja ya Olonda ndi ya Galamukani!, limodzinso ndi zofalitsa zina zoperekedwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Zimenezi zili ndi chuma cha uphungu wa m’Baibulo umene ungatithandize kuthetsa—ndipo ngakhale kutetezera—mavuto ena amene angatidetse nkhaŵa. Titsanziretu Yehova mwa kutonthozana ndi kulimbikitsana wina ndi mnzake m’nthaŵi zovuta!
19. (a) Kodi nchiyani chimatithandiza kupeŵa nsautso zina? (b) Kodi tiyenera kukhulupirira kwambiri yani, ndipo nchiyani chidzatikhozetsa kupirira mayesero?
19 Pamene tikuloŵa mkati mwenimweni mwa masiku otsiriza ndi pamene mikhalidwe m’dongosolo lino la zinthu ikuipiraipira, Akristu amachita zomwe angathe kuti apeŵe masoka. (Miyambo 22:3) Kupenya bwino, maganizo abwino, ndi chidziŵitso cha mapulinsipulo a Baibulo zingatithandize kupanga zosankha zanzeru. (Miyambo 3:21, 22) Timamvetsera Mawu a Yehova ndi kuwalabadira kuti tipeŵe kulakwitsa zinthu mosayenera. (Salmo 38:4) Koma ngakhale zili choncho, tikudziŵa kuti ngakhale titayesa motani patokha sitingachotsepo kuvutika m’moyo wathu. M’dongosolo lino la zinthu, olungama ambiri ali mu nsautso zoopsa. Komabe, tingalimbane ndi mayesero athu ndi chidaliro chonse chakuti “Yehova sadzasiya anthu ake.” (Salmo 94:14) Ndipo tikudziŵa kuti dongosololi la zinthu ndi mavuto ake zonse zidzachoka. Motero, tiyeni titsimikize kuti “tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.”—Agalatiya 6:9.
Kodi Taphunziranji?
◻ Kodi ndi mayesero otani amene gulu lonse la Akristu limakhala nawo?
◻ Kodi ndi zitsanzo za m’Baibulo ziti zimene zimatithandiza kumvetsa kuti masoka saali umboni wakuti Yehova sakukondwera nafe?
◻ Kodi Yehova amamva bwanji ndi nsautso zimene anthu ake amavutika nazo?
◻ Kodi ndi mphatso zina zotani zochokera kwa Yehova zimene zimatithandiza kupirira mayesero?
[Zithunzi patsamba 10]
Davide, Naboti, ndi Yosefe ndi atatu amene anavutika ndi masoka