Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • kr mutu 17 tsamba 182-191
  • Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu
  • Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Ndimalankhula . . . Ndendende Mmene Atate Anandiphunzitsira”
  • Kuphunzitsa Atumiki Kuti Azilalikira
  • Maphunziro Omwe Amathandiza Abale Kusamalira Maudindo Apadera
  • Sukulu Zophunzitsa Atumiki a Mulungu Zimasonyeza Kuti Yehova Amatikonda
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Kodi Mukuchita Zonse Zimene Mungathe Kuti Muphunzire Zambiri Kwa Yehova?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Kodi Apainiya Ali Ndi Mwayi Wochita Maphunziro Otani?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
  • Sukulu Yophunzitsa Utumiki—Khomo Lalikulu Loloŵera M’ntchito Yochuluka
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
Onani Zambiri
Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
kr mutu 17 tsamba 182-191

MUTU 17

Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu

CHOLINGA CHA MUTUWU

Kuona mmene masukulu a gulu athandizira atumiki a Ufumu kuti azisamalira bwino maudindo awo

1-3. Kodi Yesu anawonjezera bwanji ntchito yolalikira, nanga zimenezi zikutichititsa kukhala ndi mafunso ati?

KWA ZAKA ziwiri, Yesu analalikira dera lonse la Galileya. (Werengani Mateyu 9:35-38.) Anafika m’mizinda ndi midzi yambiri ndipo ankaphunzitsa m’masunagoge komanso kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Kulikonse kumene ankapita kukalalikira, anthu ambiri ankamutsatira. Ataona zimenezi, Yesu ananena kuti “zokolola n’zochuluka” ndipo pakufunika kuwonjezera antchito ena.

2 Yesu anakonza zowonjezera ntchito yolalikirayi. Anachita zimenezi potumiza atumwi ake 12 “kukalalikira ufumu wa Mulungu.” (Luka 9:1, 2) N’kutheka kuti atumwiwo anali ndi mafunso ambiri okhudza mmene angagwirire ntchitoyi. Koma asanawatumize Yesu mwachikondi anawaphunzitsa ngati mmene Atate ake akumwamba anamuphunzitsira.

3 Pamenepa tikhoza kukhala ndi mafunso angapo: Kodi Yesu anaphunzitsidwa chiyani ndi Atate ake? Kodi Yesu anawaphunzitsa chiyani atumwi ake? Nanga bwanji masiku ano, kodi Mfumu yomwenso ndi Mesiya yaphunzitsa ophunzira ake kugwira ntchito yolalikira? Ngati yawaphunzitsa, kodi yawaphunzitsa bwanji?

“Ndimalankhula . . . Ndendende Mmene Atate Anandiphunzitsira”

4. Kodi Yesu anaphunzitsidwa liti ndipo anaphunzitsidwira kuti?

4 Yesu anavomereza kuti anaphunzitsidwa ndi Atate ake. Pamene ankachita utumiki wake, Yesu ananena kuti: “Ndimalankhula zinthu izi ndendende mmene Atate anandiphunzitsira.” (Yoh. 8:28) Kodi Yesu anaphunzitsidwa liti ndipo anaphunzitsidwira kuti? N’zachidziwikire kuti Yesu, yemwe ndi Mwana woyamba kubadwa wa Mulungu, anayamba kuphunzitsidwa atangolengedwa. (Akol. 1:15) Kwa zaka zambirimbiri, Mwanayu anakhala kumwamba pambali pa Atate ake akumvetsera komanso kuphunzira kwa ‘Mlangizi Wamkulu.’ (Yes. 30:20) Chifukwa cha zimenezi, Mwanayo anaphunzira makhalidwe, ntchito komanso cholinga cha Atate ake.

5. Kodi Yehova anaphunzitsa chiyani Mwana wake zokhudza utumiki umene anafunika kudzachita padziko lapansi?

5 Pa nthawi yake yoyenerera, Yehova anaphunzitsa Mwana wake za utumiki umene anafunika kudzachita padziko lapansi. Taonani ulosi umene umafotokoza mmene Mlangizi Wamkulu ankaphunzitsira Mwana wake woyamba kubadwa. (Werengani Yesaya 50:4, 5.) Ulosiwu unanena kuti Yehova ankadzutsa Mwana wake “m’mawa uliwonse.” Mawu amenewa akunena za mphunzitsi amene amadzutsa wophunzira wake m’mamawa kuti akamuphunzitse. Buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo linanena kuti: “Yehova . . . ankamutenga Yesu ngati mwana wasukulu ndipo ankamuphunzitsa mfundo zoyenera kukalalikira komanso mmene angalalikirire.” Pa sukulu imeneyi, Yehova anaphunzitsa Mwana wake ‘zimene ayenera kunena ndi zimene ayenera kulankhula.’ (Yoh. 12:49) Yehova anaphunzitsanso Mwana wake mmene angaphunzitsire anthu.a Ali padziko lapansi, Yesu anagwiritsa ntchito zimene anaphunzirazo, osati pochita utumiki wake wokha komanso pophunzitsa otsatira ake kukwaniritsa utumiki wawo.

6, 7. (a) Kodi ndi mfundo ziti zimene Yesu anauza atumwi ake, ndipo mfundo zimenezi zinawathandiza bwanji? (b) Kodi Yesu waonetsetsa kuti otsatira ake alandira maphunziro otani masiku ano?

6 Kodi Yesu anaphunzitsa chiyani atumwi ake? Malinga ndi Mateyu chaputala 10, anawaphunzitsa mfundo zomveka bwino zokhudza utumiki wawo kuphatikizapo mfundo zotsatirazi: kumene ayenera kukalalikira (vesi 5, 6), uthenga woti akalalikire (vesi 7), kufunika kodalira Yehova (vesi 9, 10), mmene angayambire kukambirana ndi munthu (vesi 11-13), zimene angachite ngati wina wakana kumvetsera uthenga wawo (vesi 14, 15), komanso zimene ayenera kuchita akamazunzidwa (vesi 16-23).b Mfundo zomveka zimene Yesu anauza atumwi ake zinawathandiza kuti atsogolere ntchito yolalikira za uthenga wabwino m’nthawi yawo.

7 Nanga bwanji masiku ano? Yesu, yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, wapatsa otsatira ake ntchito yofunika kwambiri yolalikira “uthenga wabwino uwu wa ufumu . . . padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.” (Mat. 24:14) Kodi Mfumu yatiphunzitsa mmene tingagwirire ntchito yofunikayi? Inde yatiphunzitsa. Ngakhale kuti ili kumwamba, Mfumuyi yaonetsetsa kuti otsatira ake alandira maphunziro omwe angawathandize kulalikira komanso kusamalira maudindo a mumpingo.

Kuphunzitsa Atumiki Kuti Azilalikira

8, 9. (a) Kodi cholinga chachikulu cha Sukulu ya Utumiki wa Mulungu chinali chiyani? (b) Kodi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu yakuthandizani bwanji inuyo pochita utumiki wanu?

8 Gulu la Yehova lakhala likugwiritsa ntchito misonkhano ikuluikulu komanso misonkhano ya pampingo, monga Msonkhano wa Utumiki, kuphunzitsa anthu a Mulungu mmene angagwirire ntchito yolalikira. Koma kuyambira m’zaka za m’ma 1940, abale amene ankatsogolera gulu lathu pa nthawiyo anayamba kuphunzitsa atumiki a Mulungu kudzera m’masukulu osiyanasiyana.

9 Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Monga taonera m’Mutu 16, sukuluyi inayamba mu 1943. Kodi cholinga cha sukuluyi chinali kungophunzitsa anthu kuti azikamba bwino nkhani pamisonkhano ya mpingo? Ayi. Cholinga chachikulu cha sukuluyi chinali kuphunzitsa anthu a Mulungu kuti azigwiritsa ntchito mphatso yawo ya kulankhula polemekeza Yehova mu utumiki, ndipo cholinga chimenechi sichinasinthe. (Sal. 150:6) Abale ndi alongo amene analembetsa m’sukuluyi ankaphunzitsidwa kugwira bwino ntchito yawo monga atumiki a Ufumu. Masiku ano abale ndi alongo amaphunzitsidwa kudzera mu msonkhano wa mkati mwa mlungu.

10, 11. Kodi ndani amene angalowe Sukulu ya Giliyadi panopa, ndipo kodi cholinga cha zinthu zimene amaphunzitsa kusukuluyi n’chiyani?

10 Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo. Sukuluyi inayamba Lolemba pa February 1, 1943, ndipo cholinga chake chinali kuphunzitsa apainiya komanso ena omwe anali mu utumiki wa nthawi zonse kuti akakhale amishonale m’mayiko ena. Koma kuyambira mu October 2011, panakhala kusintha pa nkhani ya anthu oyenera kulowa m’sukuluyi. Panopa omwe angalowe m’sukuluyi ndi okhawo amene ali kale mu utumiki wa nthawi zonse monga apainiya apadera, oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo, amene akutumikira pa Beteli komanso amishonale omwe sanalowepo m’sukuluyi.

11 Kodi cholinga cha zinthu zimene amaphunzitsa ku Sukulu ya Giliyadi n’chiyani? M’bale wina yemwe wakhala mlangizi kwa nthawi yaitali ananena kuti: “Cholinga chake ndi kulimbitsa chikhulupiriro cha ophunzirawo pophunzira mozama Mawu a Mulungu komanso kuwathandiza kuti akhale ndi makhalidwe abwino amene angawathandize kupirira mavuto omwe angakumane nawo pa utumiki wawo. Komanso, cholinga chachikulu cha zimene amaphunzirazo ndi kulimbikitsa ophunzirawo kuti akhale ndi mtima wofunitsitsa kulalikira.”​—Aef. 4:11.

12, 13. Kodi Sukulu ya Giliyadi yathandiza bwanji ntchito yolalikira? Perekani chitsanzo.

12 Kodi Sukulu ya Giliyadi yathandiza bwanji ntchito yolalikira padziko lonse? Kuyambira mu 1943, anthu oposa 8,500 alowa m’sukulu imeneyi,c ndipo amishonale omwe analowa sukulu ya Giliyadi atumikira m’mayiko oposa 170. Amishonalewa amagwiritsa ntchito bwino zimene aphunzira ndipo amachita zimenezi polalikira mwakhama komanso pophunzitsa ena kuti nawonso azilalikira mwakhama. Nthawi zambiri amishonale amayambitsa ntchito yolalikira m’madera amene kulibe ofalitsa Ufumu kapena kutsogolera ntchitoyi m’madera amene kuli ofalitsa ochepa.

13 Taganizirani zimene zinachitika ku Japan, komwe ntchito yolalikira monga gulu inasiyiratu pa nthawi imene nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inkachitika. Pofika mu August 1949, ku Japan kunali ofalitsa osapitirira 10. Koma kumapeto kwa chaka chimenechi, amishonale 13 oti analowapo Sukulu ya Giliyadi anayamba kulalikira ku Japan. Kenako amishonale ena anabweranso kudzagwira nawo ntchitoyi. Poyamba amishonalewa ankalalikira kwambiri m’mizinda ikuluikulu koma kenako anayamba kulalikiranso m’mizinda ina. Iwo ankalimbikitsa ophunzira awo komanso abale ndi alongo ena kuti ayambe upainiya. Khama la amishonalewa silinapite pachabe chifukwa panopa ku Japan kuli olengeza Ufumu oposa 216,000, ndipo olengeza Ufumu 40 pa 100 alionse akuchita upainiya.d

14. Kodi masukulu ophunzitsa atumiki a Mulungu amatipatsa umboni wa chiyani? (Onaninso bokosi lakuti, “Masukulu Amene Amaphunzitsa Atumiki a Ufumu,” patsamba 188.)

14 Masukulu ena ophunzitsa atumiki a Mulungu. Masukulu ngati Sukulu ya Utumiki Waupainiya, Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Akhristu Apabanja komanso Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira anathandiza ophunzira kukhala anthu auzimu komanso kuti azitsogolera ntchito yolalikira mwakhama.e Sukulu zimenezi ndi umboni wamphamvu wosonyeza kuti Mfumu yathu ikuphunzitsa mokwanira otsatira ake kuti akwanitse utumiki wawo.​—2 Tim. 4:5.

Maphunziro Omwe Amathandiza Abale Kusamalira Maudindo Apadera

15. Kodi abale amene ali ndi udindo amatsatira bwanji chitsanzo cha Yesu?

15 Kumbukirani ulosi wa Yesaya womwe unanena zoti Yesu adzaphunzitsidwa ndi Mulungu. Pa sukuluyi, Mwanayo anaphunzira ‘mmene angamuyankhire munthu wotopa.’ (Yes. 50:4) Yesu anagwiritsa ntchito malangizo amenewo atabwera padziko lapansi. Iye anatsitsimula “ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa.” (Mat. 11:28-30) Potsatira Yesu, abale amene ali ndi maudindo apadera afunika kumachita zinthu zotsitsimula abale ndi alongo. Pa chifukwa chimenechi, pakhazikitsidwa masukulu osiyanasiyana n’cholinga chothandiza abale amaudindo kuti azitha kuthandiza bwino okhulupirira anzawo.

16, 17. Kodi cholinga cha Sukulu ya Utumiki wa Ufumu n’chiyani? (Onaninso mawu a m’munsi.)

16 Sukulu ya Utumiki wa Ufumu. Kalasi yoyamba ya sukuluyi inayamba pa March 9, 1959, ku South Lansing, New York. Oyang’anira oyendayenda komanso atumiki a mipingo ankaitanidwa kukalowa m’sukuluyi yomwe inali ya mwezi umodzi. Patapita nthawi, zimene ankaphunzira m’sukuluyi anazimasulira m’zinenero zina ndipo sukuluyi inayamba kuchitika m’mayiko osiyanasiyana.f

Lloyd Barry akuphunzitsa anthu pa Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ku Japan mu 1970

M’bale Lloyd Barry akuphunzitsa mu Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ku Japan, m’chaka cha 1970

17 Pofotokoza cholinga cha Sukulu ya Utumiki wa Ufumu, Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 1962 linanena kuti: “M’dziko limene anthu tonsefe ndife otanganidwa, m’bale amene ali ndi udindo woyang’anira mpingo wa Mboni za Yehova ayenera kuchita zinthu mwadongosolo kuti azitha kusamalira zosowa za aliyense mumpingo komanso kuti akhale dalitso kwa abale ndi alongowo. Zimenezi sizikutanthauza kuti asamasamalire banja lake koma kuti ayenera kuchita zinthu moganiza bwino. Kunena zoona atumiki a mipingo padziko lonse ali ndi mwayi wophunzitsidwa mu Sukulu ya Utumiki wa Ufumu kuti akwanitse kuchita zimene Baibulo limanena pa utumiki wawo.”​—1 Tim. 3:1-7; Tito 1:5-9.

18. Kodi anthu onse a Mulungu amapindula bwanji ndi Sukulu ya Utumiki wa Ufumu?

18 Kodi anthu onse a Mulungu apindula bwanji ndi Sukulu ya Utumiki wa Ufumu? Akulu komanso atumiki othandiza akamagwiritsa ntchito zimene aphunzira m’sukuluyi amakhala olimbikitsa kwa okhulupirira anzawo ngati mmene Yesu anachitira. Kodi inuyo mumayamikira mkulu kapena mtumiki wothandiza akakuuzani mawu olimbikitsa, akamamvetsera mwatcheru kapena akabwera kunyumba kwanu kudzakulimbikitsani? (1 Ates. 5:11) Kukhala ndi abale amene analowa m’sukulu imeneyi m’mipingo ndi dalitso lalikulu kwambiri.

19. Kodi ndi masukulu ena ati amene Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa imayang’anira, nanga cholinga cha masukuluwo n’chiyani?

19 Masukulu ena ophunzitsa atumiki a Mulungu. Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa ya Bungwe Lolamulira imayang’anira masukulu ena amene amaphunzitsa abale omwe ali ndi udindo m’gulu la Yehova. Masukulu amenewa amakonzedwa n’cholinga chothandiza abale omwe ndi akulu mumpingo, oyang’anira oyendayenda ndiponso abale omwe ali m’Makomiti a Nthambi kuti azisamalira bwino maudindo awo. Maphunzirowa, omwe mfundo zake zimakhala zochokera m’Baibulo, amalimbikitsa abalewa kuti azikhala olimba mwauzimu. Amawalimbikitsanso kuti azitsatira mfundo za m’Baibulo pochita zinthu ndi nkhosa zimene Yehova anawapatsa kuti aziyang’anire.​—1 Pet. 5:1-3.

Kalasi yoyamba ya Sukulu Yophunzitsa Utumiki ku Malawi

Kalasi yoyamba ya Sukulu Yophunzitsa Utumiki imene inachitika ku Malawi, m’chaka cha 2007

20. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesu sanalakwitse pamene ananena kuti tonsefe ‘taphunzitsidwa ndi Yehova’? Kodi inuyo muziyesetsa kuchita chiyani?

20 Apa n’zoonekeratu kuti Mfumu yomwenso ndi Mesiya yaonetsetsa kuti otsatira ake aphunzitsidwa bwino. Maphunziro amenewa akhala akuchitika mwadongosolo chifukwa Yehova anaphunzitsa Mwana wake kenako Mwanayo waphunzitsa otsatira ake. Mpake kuti Yesu ananena kuti tonsefe ‘taphunzitsidwa ndi Yehova.’ (Yoh. 6:45; Yes. 54:13) Choncho, tiyeni tonsefe tizigwiritsa ntchito maphunziro amene Mfumu yathu ikutipatsa. Ndipo tizikumbukira kuti cholinga chachikulu cha maphunziro onsewa ndi kutithandiza kukhala olimba mwauzimu kuti tikwanitse kuchita utumiki wathu.

a Kodi tikudziwa bwanji kuti Atate anaphunzitsa Mwana mmene angalalikirire? Taganizirani izi: Pophunzitsa, Yesu ankagwiritsa ntchito kwambiri mafanizo ndipo zimenezi zinakwaniritsa ulosi umene unalembedwa zaka zambirimbiri asanabadwe. (Sal. 78:2; Mat. 13:34, 35) Apa n’zoonekeratu kuti amene ananena ulosi umenewu, yemwe ndi Yehova, anadziwiratu kuti Mwana wake azidzaphunzitsa anthu pogwiritsa ntchito mafanizo kapena miyambi.​—2 Tim. 3:16, 17.

b Patapita miyezi ingapo, Yesu “anasankha anthu ena 70 ndi kuwatumiza awiriawiri” kuti akalalikire. Koma asanawatumize anawaphunzitsa mmene angalalikirire.​—Luka 10:1-16.

c Ena analowa Sukulu ya Giliyadi maulendo angapo.

d Kuti mudziwe zambiri zokhudza mmene amishonale omwe analowa mu Sukulu ya Giliyadi athandizira anthu padziko lonse, onani mutu 23 wa buku lakuti Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom.

e Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Akhristu Apabanja komanso Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira zinaphatikizidwa kukhala sukulu imodzi ndipo ikudziwika ndi dzina lakuti Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu.

f Masiku ano akulu onse amalowa mu Sukulu ya Utumiki wa Ufumu. Sukuluyi imachitika pakapita zaka zingapo ndipo nthawi imene imatenga imakhala yosiyanasiyana. Kuyambira m’chaka cha 1984 atumiki othandiza anayambanso kulowa nawo sukuluyi.

Kodi Inuyo Mumaona Kuti Ufumu wa Mulungu Ndi Weniweni?

  • Kodi Yesu anaphunzitsidwa chiyani ndi Atate ake?

  • Kodi Mfumu yaphunzitsa bwanji ophunzira ake kuti azigwira ntchito yolalikira?

  • Kodi abale amene ali ndi maudindo aphunzitsidwa bwanji kuti azithandiza bwino okhulupirira anzawo?

  • Kodi inuyo mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira maphunziro amene Mfumu ikutipatsa?

MASUKULU AMENE AMAPHUNZITSA ATUMIKI A UFUMU

UTUMIKI KOMANSO MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Cholinga: Kuphunzitsa ofalitsa kuti azilalikira ndiponso kuphunzitsa mogwira mtima uthenga wabwino.

Nthawi: Siitha.

Malo: Pa Nyumba ya Ufumu.

Oyenera Kulowa: Onse amene amasonkhana ndi mpingo nthawi zonse ndipo amavomereza zimene Baibulo limaphunzitsa komanso amayesetsa kutsatira mfundo za m’Malemba. Kuti mulembetse m’sukuluyi kaonaneni ndi m’bale amene amayang’anira Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu.

Phindu Lake: Misonkhano ya mkati mwa mlungu imatiphunzitsa kufufuza zinthu ndiponso kuzifotokoza motsatirika. Imatithandizanso kuti tisamangoganizira za ife tokha koma tiziganiziranso za mmene tingathandizire ena kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu.

M’bale Arnie yemwe wakhala woyang’anira woyendayenda kwa nthawi yaitali anati: “Ndili mnyamata ndinali wachibwibwi ndipo sindinkayang’ana anthu ndikamalankhula nawo. Koma msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu wandithandiza kuti ndisamadzikayikire. Yehova wandithandiza kudziwa kupuma bwino polankhula ndiponso kuika maganizo pa zimene ndikuchita. Ndimasangalala kwambiri kuti panopa ndimatha kutamanda Mulungu mu mpingo ndiponso mu utumiki.”

Mwana akuwerenga Baibulo mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

SUKULU YA AKULUg

Cholinga: Kuthandiza akulu kuti azigwira bwino ntchito yawo mu mpingo komanso azikonda kwambiri Yehova.

Nthawi: Masiku 5.

Malo: Ofesi ya nthambi ndi imene imasankha. Koma nthawi zambiri imachitikira pa Nyumba ya Ufumu kapena pa Malo a Msonkhano.

Oyenera Kulowa: Ofesi ya nthambi ndi imene imadziwitsa akuluwo.

Phindu la Sukuluyi: Tamvani zimene ena mwa akulu amene analowa kalasi ya nambala 92 ku Patterson, New York, ku United States ananena:

“Sukuluyi yandithandiza kwambiri chifukwa yandilimbikitsa kudzifufuza komanso kuona mmene ndingasamalirire nkhosa za Yehova.”

“Mfundo zimene ndaphunzirazi zidzandithandiza kwa moyo wanga wonse.”

SUKULU YA UTUMIKI WAUPAINIYA

Cholinga: Kuthandiza apainiya kuti ‘akwaniritse mbali zonse za utumiki wawo.’​—2 Tim. 4:5.

Nthawi: Masiku 6.

Malo: Ofesi ya nthambi ndi imene imasankha koma nthawi zambiri imachitikira pa Nyumba ya Ufumu.

Oyenera Kulowa: Amene achita upainiya wokhazikika kwa chaka chimodzi kapena kuposerapo. Abale ndi alongowa amadziwitsidwa ndi woyang’anira dera. Abale ndi alongo amene achita utumikiwu kwa nthawi yaitali ndipo padutsa zaka 5 chilowereni m’sukuluyi amathanso kuitanidwa.

Phindu la Sukuluyi: Mlongo Lily anati: “Sukulu imeneyi yandithandiza kuti ndizithana ndi mavuto mu utumiki komanso pa moyo wanga. Panopa, ndasintha mmene ndimaphunzirira Baibulo ndiponso mmene ndimaphunzitsira ena. Ndine wokonzeka kuthandiza ena, kuchita zinthu mogwirizana ndi akulu ndiponso kuthandiza mpingo wonse kuti ukule.”

Brenda amene walowa sukuluyi kawiri anati: “Sukulu imeneyi yandithandiza kuti ndizikonda kwambiri choonadi, kulimbitsa chikumbumtima changa ndiponso kuti ndizikonda kuthandiza ena. Kunena zoona, Yehova ndi wabwino.”

SUKULU YA OTUMIKIRA PA BETELI ATSOPANO

Cholinga: Kuthandiza amene angofika kumene pa Beteli kuti azichita bwino utumiki wawo.

Nthawi: Masiku 4 kwa maola 4 tsiku lililonse.

Malo: Ku Beteli.

Oyenera Kulowa: Amene akutumikira pa Beteli nthawi zonse kapena amene wavomerezedwa kutumikira kwa chaka chimodzi kapena zingapo pa Beteli.

Phindu la Sukuluyi: M’bale Demetrius amene analowa sukuluyi m’ma 1980 anati: “Sukuluyi inandithandiza kuti ndiziphunzira bwino Baibulo ndiponso kuti ndikhale wokonzeka kutumikira nthawi yaitali pa Beteli. Alangizi ake, maphunziro ake ndiponso malangizo amene tinkapatsidwa zinandithandiza kuona kuti Yehova amandikonda ndiponso amafuna kuti ndizichita bwino utumiki wanga wa pa Beteli.”

SUKULU YA AKHRISTU OLALIKIRA ZA UFUMUh

Cholinga: Kuphunzitsa anthu amene ali mu utumiki wa nthawi zonse (apabanja, abale osakwatira komanso alongo osakwatiwa) maphunziro omwe angawathandize kuti athe kugwiritsidwa ntchito kwambiri ndi Yehova komanso gulu lake. Ambiri mwa anthu amene amaliza maphunzirowa amatumizidwa kumene kukufunikira thandizo m’dziko lawo lomwelo. Ena amene amaliza maphunzirowa ndipo sanakwanitse zaka 50 amatumizidwa monga apainiya apadera akanthawi kumadera kumene kulibe ofalitsa kapena kumene kuli ofalitsa ochepa.

Nthawi: Miyezi iwiri.

Malo: Ofesi ya nthambi ndi imene imasankha koma nthawi zambiri imachitikira pa Nyumba ya Ufumu kapena pa Malo a Msonkhano.

Mlongo ali mu utumiki

Abale ndi alongo amapindula ndi maphunziro amene Mulungu amatipatsa

Oyenera Kulowa: Atumiki a nthawi zonse a zaka zapakati pa 23 ndi 65 amene ali ndi thanzi labwino, omwe angathe kukatumikira kumene kukufunika thandizo ndipo ali ndi mtima wodzipereka wakuti: “Ine ndilipo! Nditumizeni.” (Yes. 6:8) Onse, abale osakwatira komanso alongo osakwatiwa, kuphatikizapo anthu amene ali pabanja, akhale oti atha zaka ziwiri akuchita utumiki wa nthawi zonse mosalekeza. Anthu amene ali pabanja akhale oti papita zaka zosachepera ziwiri atakwatirana. Abale amene angalowe sukuluyi ndi amene akhala mkulu kapena mtumiki wothandiza kwa zaka zosachepera ziwiri mosalekeza. Ngati sukulu imeneyi imachitika m’gawo la nthambi yanu, ndiye kuti pa nthawi ya msonkhano wachigawo padzakhala msonkhano wa ofuna kulowa sukuluyi ndipo padzaperekedwa malangizo ofunikira.

Phindu la Sukuluyi: Anthu amene analowa Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira ndiponso Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Akhristu Apabanja ananena zinthu zambiri zoyamikira sukuluyi. Mu 2013, Bungwe Lolamulira linavomereza zophatikiza masukulu awiriwa kuti ikhale sukulu imodzi ya dzina lakuti Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. Zimenezi zichititsa kuti apainiya ambiri okhulupirika, kuphatikizapo alongo osakwatiwa, apindule ndi sukuluyi.

SUKULU YA GILIYADI YOPHUNZITSA BAIBULO

Cholinga: Amene amaliza maphunzirowa amaikidwa kukhala oyang’anira oyendayenda, amishonale kapena amakatumikira pa Beteli. Akamagwiritsa ntchito zimene aphunzira m’sukuluyi amalimbikitsa anthu a m’dera limene akutumikira komanso amathandiza kuti zinthu ziziyenda bwino pa ofesi ya nthambi.

Nthawi: Miyezi 5.

Malo: Likulu la Maphunziro la Watchtower ku Patterson, New York.

Mlangizi wa sukulu ya Giliyadi akuphunzitsa ana a sukulu

Sukulu ya Giliyadi, ku Patterson, New York

Oyenera Kulowa: Mabanja, abale osakwatira komanso alongo osakwatiwa omwe akuchita kale utumiki wa nthawi zonse. Komiti ya Nthambi imasankha amishonale omwe sanalowepo sukulu ya Giliyadi, apainiya apadera, amene akutumikira pa Beteli kapena oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo kuti alembetse m’sukuluyi. Amene akufuna kulowa sukuluyi ayenera kukhala kuti amatha kulemba ndi kulankhula Chingelezi.

Phindu la Sukuluyi: Lade ndi mkazi wake Monique omwe kwawo ndi ku United States akhala akutumikira kwa zaka zambiri.

Lade ananena kuti: “Sukulu ya Giliyadi inatikonzekeretsa kukatumikira kwina kulikonse padziko lapansi. Sukuluyi inatithandizanso kuti tizigwira ntchito iliyonse mwamphamvu limodzi ndi abale athu.”

Monique anawonjezeranso kuti: “Ndimasangalala kwambiri ndi utumiki wanga ndikamagwiritsa ntchito zimene ndaphunzira m’Mawu a Mulungu. Ndimaona kuti chisangalalo chimenechi ndi umboni wakuti Yehova amandikonda.”

SUKULU YA UTUMIKI WA UFUMU

Cholinga: Kuphunzitsa oyang’anira oyendayenda, akulu ndiponso atumiki othandiza kusamalira maudindo awo m’gulu. (Mac. 20:28) Amaphunziranso mmene angathandizire abale awo pa nkhani zimene zikuchitika pa nthawiyo. Sukuluyi imachitika pambuyo pa zaka zingapo zilizonse ndipo Bungwe Lolamulira ndi limene limakonza sukuluyi.

Nthawi: Masiku ano sukuluyi imakhala yotalika mosiyanasiyana.

Malo: Nthawi zambiri imachitikira pa Nyumba ya Ufumu kapena pa Malo a Msonkhano.

Oyenera Kulowa: Ofesi ya nthambi ndi imene imaitana oyang’anira oyendayenda ndipo woyang’anira dera ndi amene amadziwitsa akulu ndi atumiki othandiza.

Phindu la Sukuluyi: Quinn anati: “Ngakhale kuti abale amene amalowa m’sukuluyi amaphunzira zinthu zambiri zozama pa nthawi yochepa, amalimbikitsidwa kukhala osangalala komanso kupitiriza kuchita mwakhama utumiki umene Yehova wawapatsa. Akulu atsopano komanso amene akhala akutumikira kwa nthawi yaitali amaphunzira kuweta bwino nkhosa komanso kuti azichita zinthu mogwirizana pokhala ndi maganizo amodzi.”

Michael anati: “Sukuluyi inatithandiza kuti tiziyamikira kwambiri zinthu zauzimu, inatiphunzitsa zinthu zimene zikhoza kutiwononga mwauzimu komanso inatithandiza kudziwa zimene tiyenera kuchita posamalira nkhosa.”

SUKULU YA OYANG’ANIRA MADERA NDI AKAZI AWOi

Cholinga: Kuthandiza oyang’anira madera kuti azithandiza mipingo, ‘azichita khama kulankhula ndi kuphunzitsa’ komanso kutsogolera abale amene ali ndi maudindo.​—1 Tim. 5:17; 1 Pet. 5:2, 3.

Nthawi: Mwezi umodzi.

Malo: Imasankha ndi ofesi ya nthambi.

Oyenera kulowa: Ofesi ya nthambi ndi imene imaitana oyang’anira madera ndi akazi awo.

Phindu la Sukuluyi: Joel ndi Connie, amene analowa kalasi yoyamba m’chaka cha 1999, ananena kuti: “Tinayamba kuyamikira kwambiri udindo umene Yesu ali nawo potsogolera gulu. Tinaona kufunika kolimbikitsa abale amene tikuwatumikira komanso kulimbikitsa mgwirizano wa mumpingo. Sukuluyi inatsindikanso mfundo yoti ngakhale kuti woyang’anira woyendayenda amapereka malangizo komanso nthawi zina amakonza zimene zalakwika, cholinga chake chachikulu ndi kuthandiza abale kudziwa kuti Yehova amawakonda.”

SUKULU YA ABALE A M’KOMITI YA NTHAMBI NDI AKAZI AWO

Cholinga: Kuthandiza abale amene ali mu Komiti ya Nthambi kuti azisamalira bwino udindo wawo woyang’anira nyumba za Beteli, kusamalira nkhani zokhudza mipingo ndiponso kuyang’anira mmene ntchito ikuyendera m’madera komanso zigawo za m’dera la nthambi yawo.​—Luka 12:48b.

Nthawi: Miyezi iwiri.

Malo: Likulu la Maphunziro la Watchtower ku Patterson, New York.

Oyenera kulowa: Komiti ya Utumiki ya Bungwe Lolamulira ndi imene imaitana abale amene ali m’Makomiti a Nthambi kapena m’Makomiti a Dziko limodzi ndi akazi awo.

Phindu la Sukuluyi: Lowell ndi Cara analowa kalasi ya nambala 25 ndipo panopa akutumikira ku Nigeria.

Lowell ananena kuti: “Sukuluyi inandikumbutsa kuti ngakhale nditamachita zinthu zambiri kapena nditapatsidwa ntchito inayake yapadera, Yehova sangasangalale nane pokhapokha ngati ndili munthu wokonda zinthu zauzimu.”

Cara amakumbukira phunziro limene linamugwira mtima. Iye ananena kuti: “Ngati ndikulephera kufotokoza mfundo inayake mosavuta kumva ndiye kuti nkhaniyo sindinaimvetse ndipo ndikufunika kuiphunzira bwinobwino ndisanayambe kuphunzitsa ena.”

g Panopa sukuluyi siinayambe kuchitika m’mayiko onse.

h Panopa sukuluyi siinayambe kuchitika m’mayiko onse.

i Panopa sukuluyi siinayambe kuchitika m’mayiko onse.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena