Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 9/15 tsamba 8-9
  • Petro Alalikira pa Pentekoste

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Petro Alalikira pa Pentekoste
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Aliyense Akumva Chinenero Chake
  • Zimene Tiphunzirapo
  • “Anadzazidwa ndi Mzimu Woyera”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
  • Kodi “Makiyi a Ufumu” N’chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Mbuye Wake Anam’phunzitsa Kufunika Kokhala Wokhululuka
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Anakhalabe Wokhulupirika pa Nthawi Yovuta
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 9/15 tsamba 8-9

Anachita Chifuniro cha Yehova

Petro Alalikira pa Pentekoste

MUNALI mmaŵa mwabwino m’ngululu ya chaka cha 33 C.E. Pamalo ponsepo panali chisangalalo! Piringupiringu wa Ayuda ndi otembenukira ku Chiyuda anadzaza makwalala a Yerusalemu. Anali atachokera ku malo monga Elamu, Mesopotamiya, Kapadokiya, Aigupto, ndi Roma. Zinali zosangalatsa chotani nanga kuwaona atavala zovala zakwawo ndi kumva zinenero zawo zosiyanasiyana! Ena anali atayenda mtunda wa makilomita pafupifupi zikwi ziŵiri kuti adzapezeke pa chochitika chapaderachi. Kodi chinali chiyani? Pentekoste​—phwando losangalatsa lachiyuda losonyeza kutha kwa kututa barele.​—Levitiko 23:15-21.

Utsi unakwera kumwamba kuchokera pa nsembe zoperekedwa pa guwa la m’kachisi, ndipo Alevi anali kuimba Hallalel (Masalmo 113 mpaka 118). Kutangotsala pang’ono kuti 9:00 a.m. ikwane, panachitika chinachake chodabwitsa. Kuchokera kumwamba, panamveka ‘mawu ngati mkokomo wa mphepo yolimba.’ Anadzaza nyumba yonse mmene ophunzira a Yesu Kristu ngati 120 anasonkhana. Nkhaniyo ya m’Malemba imati: “Anaonekera kwa iwo malilime ogaŵanikana, onga amoto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekhawayekha. Ndipo anadzazidwa onse ndi mzimu woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga mzimu [u]nawalankhulitsa.”​—Machitidwe 2:1-4.

Aliyense Akumva Chinenero Chake

Posapita nthaŵi, ophunzira ambiri anayamba kutuluka m’nyumbamo. Modabwitsa, anali kulankhula zinenero zosiyanasiyana za khamulo! Tangolingalirani za mmene zinalili zodabwitsa pamene mlendo wochokera ku Perisiya ndi wa ku Aigupto anamva zinenero zawo zikulankhulidwa ndi Agalileya. Nchifukwa chake khamulo linadabwa kwambiri. “Kodi ichi nchiyani?” anafunsa motero. Ena anayamba kunyodola ophunzirawo, akumati: “Akhuta vinyo walero.”​—Machitidwe 2:12, 13.

Ndiyeno mtumwi Petro anaimirira nalankhula ndi khamulo. Anafotokoza kuti mphatso yozizwitsa imeneyi ya malilime inali kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Mulungu kupyolera mwa mneneri Yoweli kuti: “Ndidzathira cha mzimu wanga pa thupi lililonse.” (Machitidwe 2:14-21; Yoweli 2:28-32) Inde, Mulungu anali atangothira kumene mzimu wake woyera pa ophunzira a Yesu. Umenewu unali umboni woonekera wakuti Yesu anaukitsidwa kwa akufa ndipo tsopano anali kumwamba kudzanja lamanja la Mulungu. “Pamenepo,” anatero Petro, “lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israyeli, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Kristu, Yesu amene inu munampachika.”​—Machitidwe 2:22-36.

Kodi omvetsera anachitanji? “Analaswa mtima,” nkhaniyo imatero, “natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, Tidzachita chiyani, amuna inu, abale?” Petro anayankha nati: “Lapani, batizidwani yense wa inu.” Anthu ngati 3,000 anachita zimenezo! Pambuyo pake, “anali chikhalire m’chiphunzitso cha atumwi.”​—Machitidwe 2:37-42.

Mwa kutsogolera pa chochitika chachikulu chimenechi, Petro anagwiritsira ntchito oyamba a “mafungulo a ufumu wakumwamba” amene Yesu analonjeza kumpatsa. (Mateyu 16:19) Mafungulo ameneŵa anatsegula mwaŵi wapadera kwa magulu osiyanasiyana a anthu. Mfungulo yoyamba imeneyi inatheketsa Ayuda kukhala Akristu odzozedwa ndi mzimu. Pambuyo pake, mfungulo yachiŵiri ndi yachitatu inachititsa mwaŵi umenewu kupezeka kwa Asamariya ndiyenonso kwa Akunja.​—Machitidwe 8:14-17; 10:44-48.

Zimene Tiphunzirapo

Ngakhale kuti khamu limeneli la Ayuda ndi otembenukira ku Chiyuda anali ndi mlandu wa onse wa imfa ya Mwana wa Mulungu, Petro analankhula nawo mwaulemu akumawatcha “abale.” (Machitidwe 2:29) Cholinga chake chinali kuwasonkhezera kulapa, osati kuwatsutsa. Chotero, kalankhulidwe kake kanali kabwino. Anapereka maumboni nachirikiza mfundo zake mwa kutchula Malemba.

Awo amene amalalikira uthenga wabwino lerolino amachita bwino kutsatira chitsanzo cha Petro. Ayenera kukhazikitsa maziko omvaniranapo ndi omvetsera awo ndiyeno kukambitsirana nawo Malemba mwaluso. Pamene choonadi cha Baibulo chiperekedwa m’njira yabwino, anthu a mitima yoongoka adzachitapo kanthu.​—Machitidwe 13:48.

Changu ndi kulimba mtima kwa Petro pa tsiku la Pentekoste zikusiyana kwambiri ndi kukana kwake Yesu pafupifupi milungu isanu ndi iŵiri yapitayo. Panthaŵiyo Petro analefulidwa ndi kuwopa munthu. (Mateyu 26:69-75) Koma Yesu anali atachita pembedzero kaamba ka Petro. (Luka 22:31, 32) Mosakayikira, kuonekera kwa Yesu ataukitsidwa kwa Petro kunalimbikitsa mtumwiyo. (1 Akorinto 15:5) Choncho, chikhulupiriro cha Petro sichinasweke. Posapita nthaŵi, anali kulalikira molimba mtima. Chotero analalikira osati pa Pentekoste pokha koma kwa moyo wake wonse.

Bwanji ngati talakwa m’njira ina yake, ngakhale monga mmene anachitira Petro? Tiyeni tisonyeze kulapa, tipemphere kaamba ka chikhululukiro, ndi kuchitapo kanthu kuti tipeze thandizo lauzimu. (Yakobo 5:14-16) Ndiyeno tingapite patsogolo ndi chidaliro chakuti utumiki wathu wopatulika ngwovomerezeka kwa Atate wathu wakumwamba wachifundo, Yehova.​—Eksodo 34:6.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena